Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 2

Baibulo Ndi Buku Lochokera Kwa Mulungu

Baibulo Ndi Buku Lochokera Kwa Mulungu
  • Kodi Baibulo ndi losiyana bwanji ndi mabuku ena?

  • Kodi mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni bwanji kupirira mavuto anu?

  • N’chifukwa chiyani simuyenera kukayikira kuti maulosi onse a m’Baibulo adzakwaniritsidwa?

1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo ndi mphatso yapadera kwambiri?

KODI munayamba mwalandirapo mphatso inayake kuchokera kwa mnzanu wapamtima? Sitikukayikira kuti munasangalala nayo kwambiri komanso inakupangitsani kudziwa kuti mnzanuyo amakukondani kwambiri. Nthawi zonse munthu ukalandira mphatso umadziwa kuti amene wakupatsa mphatsoyo amakuganizira. Muyenera kuti munamuthokoza kwambiri chifukwa cha mphatsoyo.

2 Baibulo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo tiyenera kumuyamikira kwambiri chifukwa cha mphatsoyi. Buku limeneli ndi lapadera chifukwa limatifotokozera zinthu zimene sitikanatha kuzidziwa. Mwachitsanzo, limatiuza za kulengedwa kwa nyenyezi zakumwamba, dziko lapansi, komanso kulengedwa kwa mwamuna ndi mkazi oyamba. M’Baibulo muli mfundo zimene zingatithandize kupirira mavuto amene timakumana nawo. Limafotokozanso mmene Mulungu adzakwaniritsire cholinga chake n’kuchititsa kuti moyo ukhale wabwino kwambiri padzikoli. Zimenezi zikusonyeza kuti Baibulo ndi mphatso yapaderadi.

3. Kodi zimene Yehova anachita potipatsa Baibulo ndi umboni wa chiyani?

3 Kuwonjezera pamenepa, Baibulo limatifotokozeranso za Yehova Mulungu, yemwe anatipatsa mphatsoyi. Zimene anachita potipatsa buku lotere ndi umboni wakuti akufuna kuti timudziwe bwino. Ndipotu Baibulo lingakuthandizeni kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova.

4. N’chiyani chimakuchititsani chidwi ndi kufalitsidwa kwa Baibulo?

4 Ngati muli ndi Baibulo, dziwani kuti muli ndi buku limene limapezeka ndi anthu ambiri kuposa buku lina lililonse. Baibulo lonse kapena mbali yake likupezeka m’zinenero pafupifupi 2,600 moti anthu oposa 90 pa 100 alionse padziko lapansi akhoza kulipeza. Mabaibulo oposa 1 miliyoni amafalitsidwa mlungu uliwonse. Mabaibulo onse amene apangidwa, kaya lonse lathunthu kapena mbali yake, ndi mabiliyoni ambiri. Palibe buku limene lafalitsidwa kwambiri ngati Baibulo.

“Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika” likupezeka m’zinenero zambiri

5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo ‘linauziridwa ndi Mulungu’?

5 Komanso, Baibulo ‘linauziridwa ndi Mulungu.’ (Werengani 2 Timoteyo 3:16.) Kodi analiuzira bwanji? Baibulo limayankha lokha kuti: “Anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Petulo 1:21) Mwachitsanzo: Tinene kuti gogo wokalamba wapempha mdzukulu wake kuti amulembere kalata. Maganizo ndi mawu ali m’kalatayo ndi a gogoyo. Choncho tingati kalatayo ndi ya gogoyo, osati ya mdzukulu wakeyo. N’chimodzimodzinso ndi uthenga umene uli m’Baibulo, ndi wa Mulungu osati wa anthu amene analilemba. N’chifukwa chake timanena kuti Baibulo lonse ndi “mawu a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13.

NKHANI ZAKE NDI ZOGWIRIZANA KOMANSO ZOLONDOLA

6, 7. N’chifukwa chiyani kugwirizana kwa nkhani za m’Baibulo kuli kochititsa chidwi?

6 Ntchito yolemba Baibulo inatenga zaka zoposa 1,600. Anthu amene anagwiritsidwa ntchito kulemba Baibulo anakhala ndi moyo pa nthawi zosiyanasiyana komanso ankagwira ntchito zosiyanasiyana. Ena anali alimi, asodzi, abusa, aneneri, oweruza komanso mafumu. Luka, yemwe analemba nawo Uthenga Wabwino, anali dokotala. Ngakhale kuti Baibulo linalembedwa ndi anthu osiyanasiyana, mfundo zake n’zogwirizana kuyambira m’buku la Genesis mpaka Chivumbulutso. *

7 Buku loyamba la m’Baibulo limatiuza mmene mavuto a anthu anayambira, pamene buku lomaliza limafotokoza kuti dziko lonse lapansi lidzakhala munda wokongola, kapena kuti paradaiso. Nkhani zonse za m’Baibulo zimafotokoza za zinthu zimene zinachitika zaka masauzande ambiri ndipo nkhani zimenezi zimatithandiza kumvetsa cholinga cha Mulungu ndi mmene adzachikwaniritsire. Kugwirizana kwa nkhani za m’Baibulo n’kochititsa chidwi kwambiri ndipo ndi mmenedi buku lochokera kwa Mulungu linayenera kukhalira.

8. Fotokozani zitsanzo zomwe zimasonyeza kuti Baibulo ndi lolondola pa nkhani za sayansi.

8 Baibulo ndi lolondola pa nkhani za sayansi. Ndipo ngakhale kuti linalembedwa kalekale, lili ndi mfundo zothandiza komanso zotsogola kwambiri. Mwachitsanzo, m’buku la Levitiko muli malamulo amene anaperekedwa kwa Aisiraeli okhudza ukhondo komanso kuika kwaokha anthu odwala matenda opatsirana. Koma pa nthawiyo mitundu ina sinkadziwa kalikonse pa nkhani ngati zimenezi. Baibulo linafotokozanso mfundo yolondola yoti dziko lapansi ndi lozungulira ngakhale kuti anthu pa nthawiyo anali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhaniyi. (Yesaya 40:22) Baibulo linanenanso molondola kuti dziko lapansi analikoloweka “m’malere.” (Yobu 26:7) Baibulo si buku la sayansi koma likamafotokoza nkhani zokhudza sayansi, limanena zolondola. Umu ndi mmenedi buku lochokera kwa Mulungu likufunika kukhalira.

9. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zimasonyeza kuti Baibulo limafotokoza mbiri yakale molondola? (b) N’chifukwa chiyani olemba Baibulo ankafotokoza zinthu moona mtima?

9 Baibulo limafotokozanso mbiri yakale molondola. Limafotokoza zinthu momveka bwino moti nkhani zake zimatchula mayina enieni a anthu komanso mibadwo ya makolo awo. * Mosiyana ndi olemba mbiri yakale ena, omwe salemba chilichonse chokhudza kugonjetsedwa kwa mtundu wawo, olemba Baibulo ankalemba zinthu moona mtima moti ankalemba ngakhale zinthu zimene iwowo kapena mtundu wawo unalakwitsa. Mwachitsanzo, Mose analemba yekha m’buku la Numeri zinthu zimene analakwitsa n’kudzudzulidwa nazo mwamphamvu. (Numeri 20:2-12) Kufotokoza zinthu moona mtima chonchi sikupezeka kawirikawiri m’mabuku ena a mbiri yakale koma kumapezeka m’Baibulo chifukwa ndi buku lochokera kwa Mulungu.

M’BAIBULO MULI MFUNDO ZOTHANDIZA

10. N’chifukwa chiyani sizodabwitsa kuti Baibulo ndi buku lothandiza kwambiri?

10 Popeza Baibulo ndi louziridwa ndi Mulungu, ndi lopindulitsa “pa kuphunzitsa, kudzudzula, [ndi] kuwongola zinthu.” (2 Timoteyo 3:16) Baibulo ndi buku lothandiza kwambiri. Mfundo zake zimasonyeza kuti wolemba wake amadziwa bwino chibadwa cha anthu. Zimenezi sizodabwitsa chifukwa amene analemba Baibulo ndi Yehova Mulungu yemwenso ndi Mlengi wathu. Amadziwa bwino mmene timaganizira ndi mmene timamvera kuposa mmene eniakefe timadzidziwira. Ndiponso Yehova amadziwa zimene timafunikira kuti tikhale osangalala. Amadziwanso zinthu zimene tiyenera kupewa.

11, 12. (a) Kodi Yesu anafotokoza mfundo zotani pa ulaliki wake wa paphiri? (b) Kodi Baibulo limafotokozanso mfundo zina ziti zothandiza, ndipo n’chifukwa chiyani malangizo ake ali opindulitsabe mpaka pano?

11 Taganizirani mawu a Yesu opezeka m’buku la Mateyu chaputala 5 mpaka 7, omwe amadziwika kuti Ulaliki wa Paphiri. Pa ulaliki umenewu Yesu anaphunzitsa mwaluso kwambiri. Anafotokoza nkhani zosiyanasiyana monga zokhudza mmene munthu angapezere chimwemwe chenicheni, kuthetsa kusamvana, mmene tingapempherere ndiponso mmene munthu angakhalire ndi maganizo oyenera pa nkhani ya chuma. Mawu a Yesu ndi amphamvube komanso othandiza mpaka pano.

12 Mfundo zina za m’Baibulo zimafotokoza za moyo wa m’banja, kagwiridwe ka ntchito ndiponso mmene tingakhalire ndi anthu ena. Mfundo za m’Baibulo ndi zothandiza kwa anthu onse ndipo malangizo ake ndi opindulitsa nthawi zonse. Zimene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yesaya zimafotokoza bwino mfundo yoti Baibulo ndi lothandiza kwambiri. Iye anati: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.”—Yesaya 48:17.

BAIBULO NDI BUKU LA MAULOSI

Yesaya ananeneratu za kuwonongedwa kwa Babulo

13. Kodi Yehova anauza mneneri Yesaya kuti alembe zinthu ziti zokhudza Babulo?

13 M’Baibulo muli maulosi ambirimbiri ndipo ambiri mwa maulosiwo anakwaniritsidwa kale. Tiyeni tione chitsanzo chimodzi. Kudzera mwa mneneri Yesaya, yemwe anakhala ndi moyo zaka za m’ma 700 B.C.E., Yehova ananeneratu zoti mzinda wa Babulo udzawonongedwa. (Yesaya 13:19; 14:22, 23) Anafotokozanso mmene mzindawo adzaugonjetsere. Anafotokoza kuti asilikali adzaphwetsa madzi a mumtsinje womwe unazungulira mzindawo, n’kulowa mumzindawo popanda kumenya nkhondo. Komatu sizokhazo, ulosi wa Yesaya unachita kutchula dzina lenileni la mfumu imene idzagonjetse mzinda wa Babulo. Unanena kuti dzina lake lidzakhala Koresi.—Werengani Yesaya 44:27–45:2.

14, 15. Kodi zinthu zina zimene Yesaya analosera zinakwaniritsidwa bwanji?

14 Patadutsa zaka pafupifupi 200, usiku wa pa October 5, mu 539 B.C.E., gulu la asilikali linasonkhana pafupi ndi mzinda wa Babulo. Kodi mtsogoleri wawo anali ndani? Anali mfumu ya Perisiya dzina lake Koresi. Apa zinthu zonse zinali m’malo mwake kuti ulosi wochititsa chidwi uja ukwaniritsidwe. Koma kodi asilikali a Koresi analowadi mumzinda wa Babulo popanda kumenya nkhondo, ngati mmene ulosi uja unanenera?

15 Pa nthawi imeneyo Ababulo anali pa phwando ndipo ankaona kuti ndi otetezeka mkati mwa mpanda waukulu umene anamanga kuzungulira mzindawo. Koma Koresi anapatutsa madzi a mumtsinje umene unazungulira mzindawo. Madziwo ataphwera asilikali ake anawoloka n’kukafika pakhoma la mpanda wa mzindawo. Koma kodi asilikali a Koresi akanalowa bwanji mumpanda wa mzindawo? Pa chifukwa chosadziwika bwino, usiku umenewo mageti a mzindawo anangowasiya osatseka.

16. (a) Kodi Yesaya ananeneratu kuti chidzachitike n’chiyani Babulo akadzawonongedwa? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti ulosi wa Yesaya wonena za kuwonongedwa kwa Babulo unakwaniritsidwa?

16 Ulosi wina unanena kuti: “M’Babulo simudzakhalanso anthu, ndipo iye sadzakhalaponso ku mibadwomibadwo. Kumeneko Mluya sadzakhomako hema wake, ndipo abusa sadzagonekako ziweto zawo.” (Yesaya 13:20) Ulosi umenewu unaneneratu zoti mzinda wa Babulo udzawonongedwa komanso kuti mumzindawo simudzakhalanso anthu mpaka kalekale. Masiku ano pali umboni wosonyeza kuti ulosi umenewu unakwaniritsidwadi. Malo amene panali mzinda wa Babulo ali pamtunda wa makilomita pafupifupi 80 kum’mwera kwa mzinda wa Baghdad, ku Iraq ndipo mpaka pano sikukhala munthu aliyense. Zimenezi ndi umboni wakuti zomwe Yehova ananena kudzera mwa Yesaya zinakwaniritsidwa, zakuti: “Ndidzamusesa ndi tsache la chiwonongeko.”—Yesaya 14:22, 23. *

Malo opanda anthu pomwe panali mzinda wa Babulo

17. Kodi kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo kumalimbikitsa bwanji chikhulupiriro chathu?

17 Kudziwa kuti maulosi a m’Baibulo amakwaniritsidwa kumalimbitsa kwambiri chikhulupiriro chathu. Timatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngati Yehova anakwaniritsa malonjezo ake m’mbuyomu, ndiye kuti adzakwaniritsanso lonjezo lake la dziko la paradaiso. (Werengani Numeri 23:19.) Tili ndi “chiyembekezo cha moyo wosatha, chomwe Mulungu amene sanganame, analonjeza kalekale.”—Tito 1:2. *

“MAWU A MULUNGU NDI AMOYO”

18. Kodi mtumwi Paulo anati chiyani ponena za “mawu a Mulungu”?

18 Zimene taphunzira m’mutu uno, zatithandiza kuona kuti Baibulo ndi buku lapaderadi. Taona kuti nkhani zake n’zogwirizana, zolondola pa nkhani za sayansi ndi mbiri yakale, lili ndi mfundo zothandiza ndiponso maulosi ake amakwaniritsidwa. Komatu sizokhazi, n’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu, komanso mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.”—Aheberi 4:12.

19, 20. (a) Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji kudzifufuza? (b) Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira Baibulo, lomwe ndi mphatso yapadera yochokera kwa Mulungu?

19 Kuwerenga “mawu” kapena kuti uthenga wa Mulungu m’Baibulo kungasinthe moyo wathu. Kungatithandize kuti tizidzifufuza. Tikhoza kunena kuti timakonda Mulungu, koma zimene timachita tikazindikira zimene Baibulo limaphunzitsa n’zimene zingasonyeze zimene timaganiza komanso zimene zili mumtima mwathu.

20 Baibulo ndi buku lochokeradi kwa Mulungu, choncho n’lofunika kuti tiziliwerenga, kuliphunzira ndiponso kulikonda. Mungasonyeze kuti mumayamikira mphatso yochokera kwa Mulungu imeneyi popitiriza kuwerenga nkhani zake. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kumvetsa bwino cholinga cha Mulungu kwa anthu. Mutu wotsatira udzafotokoza kuti cholingacho n’chiyani komanso mmene chidzakwaniritsidwire.

^ ndime 6 Ngakhale kuti anthu ena amanena kuti nkhani zina za m’Baibulo zimatsutsana, zimene amanenazo zilibe umboni. Onani Mutu 7 m’buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 9 Mwachitsanzo, taonani mmene anafotokozera momveka bwino mayina a makolo a Yesu pa Luka 3:23-38.

^ ndime 16 Kuti mumve zambiri zokhudza maulosi a m’Baibulo, onani tsamba 27-29 m’kabuku kakuti Buku la Anthu Onse, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 17 Kuwonongedwa kwa Babulo ndi chitsanzo chimodzi cha maulosi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa. Koma palinso zitsanzo zina monga za kuwonongedwa kwa mzinda wa Turo ndi Nineve. (Ezekieli 26:1-5; Zefaniya 2:13-15) Komanso ulosi wa Danieli unaneneratu kuti maulamuliro amphamvu a Mediya ndi Perisiya ndiponso Girisi ndi amene adzalamulire pambuyo pa ulamuliro wa Babulo. (Danieli 8:5-7, 20-22) Palinso maulosi ena ambiri onena za Mesiya omwe anakwaniritsidwa pa Yesu Khristu ndipo kuti mumve zambiri za maulosi amenewa, onani Zakumapeto tsamba 199-201.