Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Kodi “Babulo Wamkulu” N’chiyani?

Kodi “Babulo Wamkulu” N’chiyani?

M’BUKU la Chivumbulutso muli mawu ambiri okuluwika. (Chivumbulutso 1:1) Mwachitsanzo, limafotokoza za mkazi wina yemwe analembedwa dzina lakuti “Babulo Wamkulu” pamphumi pake. Mkaziyu amamufotokoza kuti wakhala pa ‘makamu a anthu ndi mayiko.’ (Chivumbulutso 17:1, 5, 15) Popeza palibe mkazi aliyense amene angathe kuchita zimenezi, ndiye kuti mawu akuti Babulo Wamkulu ndi okuluwika. Ndiye kodi hule limeneli likuimira chiyani?

Pa Chivumbulutso 17:18, mkazi yemweyu akufotokozedwa kuti ndi “mzinda waukulu umene ukulamulira mafumu a dziko lapansi.” Mawu akuti “mzinda” akusonyeza kuti limeneli ndi gulu la anthu omwe amachita zinthu mogwirizana. Popeza “mzinda waukulu” umenewu umalamulira “mafumu a dziko lapansi,” ndiye kuti mkazi amene amatchulidwa kuti Babulo Wamkulu ayenera kukhala gulu lomwe zochita zake zimakhudza dziko lonse lapansi, moti n’zomveka kunena kuti ndi ufumu wa padziko lonse. Ufumu umenewu, kapena kuti ulamuliro, ndi wachipembedzo. Tiyeni tione nkhani zina za m’buku la Chivumbulutso zimene zikutichititsa kuona choncho.

Ulamuliro ukhoza kukhala m’manja mwa anthu andale, abizinezi, kapena achipembedzo. Mkazi yemwe akutchulidwa kuti ndi Babulo Wamkuluyu sakuimira ulamuliro wa andale, chifukwa mawu a Mulungu amanena kuti ‘mafumu a dziko lapansi anachita naye dama.’ Dama lake ndi lakuti wakhala akugwirizana ndi olamulira adziko lapansi ndiponso kuchita zinthu zina zambiri n’cholinga choti aziwalamulira. N’chifukwa chake amatchulidwa kuti ndi “hule lalikulu.”—Chivumbulutso 17:1, 2; Yakobo 4:4.

Babulo Wamkulu sangakhalenso ulamuliro wa anthu abizinezi chifukwa “amalonda oyendayenda a padziko lapansi,” kutanthauza anthu abizinezi, adzamulira akadzawonongedwa. Ndipotu Baibulo limanena kuti mafumu ndi amalonda oyendayenda azidzayang’ana Babulo Wamkulu ataima “patali.” (Chivumbulutso 18:3, 9, 10, 15-17) Choncho, n’zomveka kunena kuti Babulo Wamkulu si ulamuliro wa andale kapena abizinezi, koma wachipembedzo.

Umboni wina wosonyeza kuti Babulo Wamkulu ndi ulamuliro wachipembedzo ndi wakuti amanenedwa kuti amasocheretsa mitundu yonse ya anthu ndi ‘zochita zake zamizimu.’ (Chivumbulutso 18:23) Popeza zinthu zonse zamizimu zimachokera kwa ziwanda, n’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Babulo Wamkulu ndi “malo okhala ziwanda.” (Chivumbulutso 18:2; Deuteronomo 18:10-12) Baibulo limafotokozanso kuti ulamuliro umenewu umalimbana ndi chipembedzo choona, moti umazunza “aneneri” ndiponso anthu “oyera.” (Chivumbulutso 18:24) Ndipotu Babulo Wamkulu amadana kwambiri ndi chipembedzo choona mpaka kufika pozunza mwankhanza komanso kupha “mboni za Yesu.” (Chivumbulutso 17:6) Zinthu zonsezi zikusonyeza kuti Babulo Wamkulu ndi zipembedzo zonse zonyenga zimene zimatsutsana ndi Yehova Mulungu.