ZAKUMAPETO
Yesu Ndi Mesiya Amene Mulungu Ananeneratu Kuti Adzabwera
POFUNA kutithandiza kuti tidzathe kuzindikira Mesiya, Yehova Mulungu anauzira aneneri ambiri kuti alembe nkhani zokhudza kubadwa kwa Mpulumutsiyu, utumiki wake, ndiponso imfa yake. Maulosi onsewa anakwaniritsidwa pa Yesu Khristu. N’zochititsa
chidwi kuona mmene maulosiwa anafotokozera zinthu motsatirika komanso molondola. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyeni tikambirane maulosi angapo okhudza kubadwa kwa Mesiya ndiponso zinthu zimene zinachitika ali mwana.Mneneri Yesaya ananeneratu kuti Mesiya adzabadwira m’banja la Mfumu Davide. (Yesaya 9:7) Yesu anabadwiradi m’banja la Davide.—Mateyu 1:1, 6-17.
Mika 5:2) Pa nthawi imene Yesu anabadwa, ku Isiraeli kunali mizinda iwiri imene inkadziwika ndi dzina lakuti Betelehemu. Mzinda umodzi unali kufupi ndi ku Nazareti, pomwe wina unali kufupi ndi Yerusalemu ku Yuda. Mzinda wa Betelehemu wakufupi ndi Yerusalemu poyamba unkatchulidwa kuti Efurata ndipo kumeneku ndi komwe Yesu anabadwira mogwirizana ndi mmene ulosi unanenera.—Mateyu 2:1.
Mneneri winanso wa Mulungu, dzina lake Mika, ananeneratu kuti mwana ameneyu akadzakula adzakhala mfumu komanso kuti adzabadwira ku “Betelehemu Efurata.” (Ulosi wina unaneneratu kuti Mwana wa Mulungu adzaitanidwa kuti “atuluke mu Iguputo.” Yesu ali mwana makolo ake anapita naye ku Iguputo. Iwo anabwerera naye kwawo pambuyo pa imfa ya Herode ndipo kumeneku kunali kukwaniritsidwa kwa ulosiwu.—Hoseya 11:1; Mateyu 2:15.
Pa tchati chimene chili patsamba 200, malemba amene ali pansi pa mutu wakuti “Ulosi” akufotokoza zinthu zosiyanasiyana zokhudza Mesiya. Yerekezetsani zimene malemba amenewa akunena ndi zomwe zili m’malemba omwe ali pansi pa mutu wakuti “kukwaniritsidwa kwake.” Kuchita zimenezi kungawonjezere zifukwa zina zokuchititsani kukhulupirira kuti Mawu a Mulungu ndi oona.
Mukamawerenga malembawa muyenera kukumbukira kuti malemba amene ali ndi ulosiwo analembedwa zaka zambirimbiri Yesu asanabadwe. Yesu ananena kuti: “Zonse zokhudza ine zolembedwa m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri ndi m’Masalimo ziyenera kukwaniritsidwa.” (Luka 24:44) Ndipo mukaona m’Baibulo lanu mungatsimikizire kuti maulosi onsewa anakwaniritsidwadi.