Macitidwe a Atumwi 6:1-15

  • Amuna 7 asankhidwa kuti atumikile (1-7)

  • Sitefano aimbidwa mlandu wonyoza Mulungu (8-15)

6  Tsopano m’masiku amenewo pamene ophunzila anali kuonjezeka, Ayuda okamba Cigiriki anayamba kudandaula za Ayuda okamba Ciheberi, cifukwa akazi amasiye a Cigiriki anali kunyalanyazidwa pa kagawidwe ka cakudya ca tsiku ndi tsiku. 2  Conco atumwi 12 aja anasonkhanitsa khamu la ophunzila n’kunena kuti: “Sibwino* kuti ife tilekeze kuphunzitsa mau a Mulungu n’kuyamba kugawa cakudya. 3  Conco abale, sankhani amuna 7 pakati panu a mbili yabwino, odzala ndi mzimu komanso nzelu kuti tiwapatse udindo wosamalila nchitoyi. 4  Koma ife tidzadzipeleka pa kupemphela ndi pa utumiki wokhudza mau a Mulungu.” 5  Zimene anakamba zinasangalatsa khamu lonse, moti anasankha Sitefano munthu wacikhulupililo colimba, ndiponso wodzala ndi mzimu woyela. Anasankhanso Filipo, Pulokoro, Nikanora, Timoni, Pamenasi, komanso Nikolao wocokela ku Antiokeya, wotembenukila ku Ciyuda. 6  Iwo anawapeleka kwa atumwi, ndipo atumwiwo atawapemphelela anaika manja ao pa amunawo. 7  Zitatelo, mau a Mulungu anapitiliza kufalikila, ndipo ciwelengelo ca ophunzila cinali kuonjezeka kwambili mu Yerusalemu. Ngakhale ansembe ambili anakhala okhulupilila. 8  Tsopano Sitefano wokondedwa ndi Mulungu, komanso amene Mulungu anamupatsa mphamvu, anali kucita zodabwitsa zazikulu ndi zizindikilo pakati pa anthu. 9  Koma amuna ena a gulu lochedwa Sunagoge wa Omasulidwa anabwela pamodzi ndi anthu a ku Kurene, a ku Alekizandiriya, ku Kilikiya, komanso ku Asia kudzatsutsana ndi Sitefano. 10  Koma iwo sanathe kulimbana naye cifukwa ca nzelu zake komanso mzimu umene anali nao polankhula. 11  Zitatelo, iwo mwamseli ananyengelela anthu kuti anene kuti: “Ife tamumva akulankhula zinthu zonyoza Mose komanso Mulungu.” 12  Iwo anatuntha gulu la anthu, akulu, komanso alembi, kuti amugwile modzidzimutsa n’kupita naye ku Khoti Yaikulu ya Ayuda.* 13  Iwo anabweletsa mboni zonama zimene zinakamba kuti: “Munthu uyu akungolankhula zinthu zambili zonyoza malo oyelawa komanso Cilamulo. 14  Mwacitsanzo, tamumva akunena kuti Yesu Mnazareti adzagwetsa malo ano n’kusintha miyambo imene Mose anatipatsa.” 15  Ndipo anthu onse amene anali m’Khoti Yaikulu ya Ayuda, atamuyang’anitsitsa Sitefano, anaona kuti nkhope yake inali kuoneka ngati ya mngelo.

Mau a m'Munsi

Kucokela ku Cigiriki, “N’zosakondweletsa.”
Kucokela ku Cigiriki, “ku Sanihedirini.”