Macitidwe a Atumwi 19:1-41

  • Paulo ku Efeso; ena abatizika kaciwili (1-7)

  • Nchito yophunzitsa ya Paulo (8-10)

  • Apeza cipambano ngakhale kuti ena anali kukhulupilila zamizimu (11-20)

  • Cipolowe ku Efeso (21-41)

19  Apolo ali ku Korinto, Paulo anadzela ku madela a kumtunda mpaka anafika ku Efeso. Kumeneko iye anapeza ophunzila ena, 2  ndipo anawafunsa kuti: “Kodi munalandila mzimu woyela mutakhala okhulupilila?” Iwo anamuyankha kuti: “Sitinamvepo kuti kuli mzimu woyela.” 3  Iye anawafunsanso kuti: “Ndiye kodi munabatizidwa ubatizo wotani?” Iwo anayankha kuti: “Ubatizo wa Yohane.” 4  Ndiyeno Paulo anati: “Yohane anali kubatiza anthu ndipo ubatizowo unali cizindikilo cakuti munthu walapa. Anali kuuza anthu kuti akhulupilile amene anali kubwela m’mbuyo mwake, kutanthauza Yesu.” 5  Atamva izi, anthuwo anabatizika m’dzina la Ambuye Yesu. 6  Ndiyeno Paulo ataika manja ake pamutu pao, iwo analandila mzimu woyela, ndipo anayamba kukamba zinenelo zina komanso kulosela. 7  Onse pamodzi anali amuna pafupifupi 12. 8  Kwa miyezi itatu, Paulo anali kulowa m’sunagoge ndipo anali kulankhula molimba mtima. Kumeneko anali kukamba nkhani ndi kuwafotokozela mfundo zogwila mtima za Ufumu wa Mulungu. 9  Koma ena anakana mwamwano kukhulupilila* ndipo anali kukamba zinthu zonyoza Njilayo pamaso pa khamu la anthu. Conco iye anacoka n’kucotsanso ophunzila pakati pao. Ndipo tsiku ndi tsiku anali kukamba nkhani mu holo ya pa sukulu ya Turano. 10  Izi zinacitika kwa zaka ziwili, moti anthu onse okhala m’cigao ca Asia, anamva mau a Ambuye, onse Ayuda ndi Agiriki. 11  Ndipo kupitila mwa Paulo, Mulungu anapitiliza kucita zinthu zamphamvu komanso zodabwitsa, 12  cakuti anthu anali kutenga ngakhale tunsalu ndi zobvala* zimene zinakhudza thupi la Paulo n’kupita nazo kwa odwala, ndipo matenda ao anali kuthelatu. Mizimu yoipa nayonso inali kutuluka. 13  Koma Ayuda ena amene anali kuyenda-yenda n’kumatulutsa ziwanda, naonso anayesa kuchula dzina la Ambuye Yesu pofuna kucilitsa anthu amene anali ndi mizimu yoipa. Iwo anali kunena kuti: “Ndikukulamula m’dzina la Yesu amene Paulo amalalikila za iye.” 14  Tsopano panali ana aamuna 7 a Sikeva, wansembe wamkulu waciyuda, amene anali kucita zimenezi. 15  Koma mzimu woipa unawauza kuti: “Yesu ndimamudziwa, komanso Paulo ndimamudziwa bwino. Nanga inu ndinu ndani?” 16  Ndiyeno munthu uja amene anali ndi mzimu woipa anawalumphila. Analimbana nao mmodzi ndi mmodzi ndipo anawagonjetsa onsewo, moti anathawa m’nyumbamo ali malisece komanso atabvulazidwa. 17  Izi zinadziwika kwa onse, kwa Ayuda ndi Agiriki amene anali kukhala ku Efeso. Onsewo anagwidwa ndi mantha, ndipo dzina la Ambuye Yesu linapitiliza kulemekezedwa. 18  Anthu ambili mwa amene anakhala okhulupilila anali kubwela kudzaulula macimo ao, ndiponso kudzafotokoza poyela zoipa zimene anali kucita. 19  Anthu ambili amene anali kucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao n’kuwatentha anthu onse akuona. Ndipo atawelengetsela mtengo wake, anapeza kuti anali okwana ndalama zasiliva 50,000. 20  Conco mau a Yehova* anapitiliza kufalikila ndipo sanagonjetsedwe. 21  Izi zitacitika, Paulo anatsimikiza mu mtima mwake kuti adzele ku Makedoniya ndi ku Akaya, popita ku Yerusalemu. Iye anakamba kuti: “Ndikakafika kumeneko, ndidzapitanso ku Roma.” 22  Conco ku Makedoniya anatumizako awili mwa amene anali kumutumikila, iwo anali Timoteyo ndi Erasito. Koma iye anakhalabe m’cigao ca Asia kwa kanthawi ndithu. 23  Panthawiyo, panali patabuka msokonezo waukulu wokhudza Njila ya Ambuye. 24  Panali munthu wina dzina lake Demetiriyo, wopanga zinthu zasiliva. Amisili anali kupeza phindu kwambili cifukwa ca nchito yake yopanga tuakacisi twasiliva twa Atemi. 25  Demetiriyo anasonkhanitsa amisiliwo, limodzi ndi ena amene anali kugwila nchito ngati zimenezi n’kuwauza kuti: “Anthu inu, mukudziwa kuti timapeza cuma kucokela m’bizinesi imeneyi. 26  Tsopano mukuona ndi kumva mmene Paulo ameneyu wakopela anthu ambili kuti ayambe kukhulupilila zinthu zina. Iye wacita zimenezi osati mu Efeso mokha, koma pafupifupi m’cigao conse ca Asia. Iye akukamba kuti milungu yopangidwa ndi manja si milungu yeniyeni. 27  Komanso cimene cikuopsya kwambili si kunyozeka kwa bizinesi yathuyi cabe ai, koma kacisi wa mulungu wamkazi Atemi adzaonedwa wacabe-cabe. Atemi ameneyu amene amalambilidwa m’cigao conse ca Asia, komanso kulikonse kumene kuli anthu pa dziko lapansi adzaleka kupatsidwa ulemelelo wake.” 28  Anthuwo atamva zimenezi anakwiya kwambili, ndipo anayamba kupfuula kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!” 29  Zitatelo, mu mzindawo munadzala msokonezo, ndipo anthu onse anathamangila m’bwalo la masewela, n’kukokela Gayo ndi Arisitako m’bwalomo. Gayo ndi Arisitako amene anali kuyenda ndi Paulo, kwao kunali ku Makedoniya. 30  Paulo anali kufuna kulowa mkati m’gulu la anthulo, koma ophunzila sanamulole. 31  Ngakhale ena mwa oyang’anila zikondwelelo ndi masewela, amene anali anzake a Paulo, anatumiza uthenga kumucondelela kuti asaike moyo wake pangozi mwa kulowa m’bwalo la masewelalo. 32  Kukamba zoona, khamu lonse linali litasokonezeka, ena anali kupfuula zinthu zina pamene ena zinthu zina. Ndipo ambili a iwo sanadziwe kuti n’cifukwa ciani anasonkhana kumeneko. 33  Conco anatulutsa Alekizanda m’khamulo ndipo Ayuda anali kumukankhila kutsogolo. Ndiyeno Alekizanda anakweza dzanja lake kuti alankhule podziteteza kwa anthuwo. 34  Koma atazindikila kuti ndi Myuda, anayamba kupfuula capamodzi kwa maola pafupifupi awili kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!” 35  Woyang’anila mzindawo atauza khamulo kuti likhale cete anati: “Anthu inu a mu Efeso, kodi pali amene sadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndi umene umayang’anila kacisi wamkulu wa Atemi ndi cifanizilo cimene cinagwa kucokela kumwamba? 36  Popeza palibe amene angatsutse zimenezi, muyenela kudekha, ndipo musacite zinthu mopupuluma. 37  Cifukwa anthu amene mwabweletsa kunowa si akuba mu akacisi kapena onyoza mulungu wathu wamkaziyo. 38  Conco ngati Demetiriyo ndi amisili awa akuimba mlandu munthu winawake, pali masiku osamalila milandu ndipo abwanamkubwa* alipo. Apite akafole kumeneko. 39  Koma ngati mukufuna zina zoposa pamenepa, cigamulo cake ciyenela kukapelekedwa pa bwalo lobvomelezeka. 40  Pakuti zimene zacitikazi n’zoopsya kwambili cifukwa tingaimbidwe nazo mlandu woukila boma. Pakuti palibe cifukwa comveka cimene tingapeleke pa cipolowe cimene cacitikaci.” 41  Atanena zimenezi, anauza anthuwo kuti acoke pamalopo.

Mau a m'Munsi

Kapena kuti, “ena anaumitsa mitima yao, moti sanakhulupilile.”
Kapena kuti, “ndi maepuloni.”
Bwanamkubwa wa cigao ca Roma.