Macitidwe a Atumwi 11:1-30

  • Petulo apeleka lipoti kwa atumwi (1-18)

  • Baranaba ndi Saulo ku Antiokeya wa ku Siriya (19-26)

    • Ophunzila ayamba kuchedwa Akhristu (26)

  • Agabo alosela za njala (27-30)

11  Tsopano atumwi ndi abale amene anali ku Yudeya anamva kuti anthu a mitundu ina naonso alandila mau a Mulungu. 2  Conco Petulo atapita ku Yerusalemu, anthu olimbikitsa mdulidwe anayamba kumuimba mlandu.* 3  Anali kumuuza kuti: “Iwe unalowa m’nyumba ya anthu osadulidwa ndipo unadya nao.” 4  Petulo atamva izi anayamba kuwafotokozela mwatsatane-tsatane zimene zinacitika kuti: 5  “Ndinali kupemphela mumzinda wa Yopa ndipo ndinaona masomphenya. M’masomphenyawo ndinaona cinthu cooneka ngati cinsalu cacikulu, cikutsika kucokela kumwamba. Cinthuco anacigwila m’makona ake anai n’kucitsitsila pamene panali ine. 6  N’taciyang’anitsitsa, ndinaonapo nyama za miyendo inai za padziko lapansi, nyama zakuchile, nyama zokwawa, komanso mbalame za mumlengalenga. 7  Ndinamvanso mau ondiuza kuti: ‘Petulo, nyamuka, uphe ndi kudya zinthu zimenezi!’ 8  Koma ine ndinati: ‘Ai Ambuye, cinthu codetsedwa komanso conyansa sicinalowepo m’kamwa mwanga.’ 9  Kaciwili, ndinamvanso mau ocokela kumwamba akuti: ‘Ulekeletu kuchula zinthu zimene Mulungu waziyeletsa kuti zodetsedwa.’ 10  Mauwa anamvekanso kacitatu, ndipo zonse zinatengedwa n’kubwelela kumwamba. 11  Nthawi yomweyo amuna atatu ocokela ku Kaisareya amene anatumidwa kwa ine, anafika panyumba imene tinali kukhala. 12  Kenako mzimu unandiuza kuti ndipite nao ndisakaikile ngakhale pang’ono. Abale 6 awa anapita nane, ndipo tinakalowa m’nyumba ya munthuyo. 13  “Iye anatifotokozela kuti ali m’nyumba mwake anaona mngelo ataimilila, ndipo anamuuza kuti: ‘Tuma anthu ku Yopa kuti akaitane Simoni wodziwikanso kuti Petulo. 14  Iye adzakuuza zimene iwe ndi a m’banja lako mungacite kuti mupulumuke.’ 15  Koma nditangoyamba kulankhula, mzimu woyela unafika pa iwo monga unacitila kwa ife poyamba paja. 16  Zitatelo, ndinakumbukila mau amene Ambuye anali kukonda kukamba akuti: ‘Yohane anali kubatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyela.’ 17  Conco, ngati Mulungu anawapatsa mphatso yaulele imenenso anapeleka kwa ife amene tinakhulupilila mwa Ambuye Yesu Khristu, ndiye ndine ndani kuti ndimuletse Mulungu?”* 18  Iwo atamva zimenezi analeka kumutsutsa,* ndipo anatamanda Mulungu kuti: “Ndiye kuti Mulungu wapatsanso mwai anthu a mitundu ina wakuti alape ndi kukapeza moyo.” 19  Anthu amene anabalalika kaamba ka mabvuto amene anayamba cifukwa ca zimene zinacitikila Sitefano, anafika mpaka ku Foinike, ku Kupuro, ndi Antiokeya. Koma anali kungolalikila kwa Ayuda okha. 20  Komabe, ena mwa anthu ocokela ku Kupuro ndi ku Kurene atafika ku Antiokeya, anayamba kulengeza uthenga wabwino wa Ambuye Yesu kwa anthu okamba Cigiriki. 21  Kuonjezela apo, dzanja la Yehova* linali nao, ndipo anthu ambili anakhala okhulupilila, ndiponso anayamba kutsatila Ambuye. 22  Mpingo wa ku Yerusalemu unamva zokhudza anthuwa, ndipo unatumiza Baranaba kuti apite ku Antiokeya. 23  Atafika kumeneko n’kuona cisomo ca Mulungu, anasangalala ndipo anayamba kulimbikitsa onse kuti apitilize kukhala okhulupilika kwa Ambuye ndi mtima wonse. 24  Baranaba anali munthu wabwino wa cikhulupililo colimba, komanso wodzazidwa ndi mzimu woyela. Cifukwa ca zimenezo, khamu la anthu linayamba kukhulupilila Ambuye. 25  Kenako iye anapita ku Tariso kukafuna-funa Saulo mosamala. 26  Atamupeza, anapita naye ku Antiokeya. Kwa caka cathunthu, iwo anali kusonkhana ndi mpingo, ndipo anaphunzitsa anthu ambili. Motsogoleledwa ndi Mulungu, ku Antiokeya n’kumene ophunzilawo anayamba kuchedwa Akhristu. 27  M’masiku amenewo, aneneli ocokela ku Yerusalemu anapita ku Antiokeya. 28  Mmodzi wa iwo dzina lake Agabo analosela mothandizidwa ndi mzimu woyela kuti padziko lonse lapansi padzagwa njala yaikulu. Ndipo zimenezi zinadzacitikadi m’nthawi ya Kalaudiyo. 29  Conco ophunzilawo anatsimikiza mtima kutumiza thandizo* kwa abale a ku Yudeya, aliyense malinga n’zimene akanakwanitsa. 30  Iwo anacitadi zimenezo, ndipo anatumiza thandizolo kwa akulu mwa kupatsila Baranaba ndi Saulo.

Mau a m'Munsi

Kapena kuti, “anayamba kulimbana naye.”
Kapena kuti, “kuti nditsekeleze njila ya Mulungu?”
Kucokela ku Cigiriki, “zimenezi anakhala cete.”
Kapena kuti, “mtima kucita utumiki wothandiza anthu.”