Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesu Weniweni

Yesu Weniweni

Yesu Weniweni

YESU atamva kwa ophunzira ake zomwe anthu ankanena zokhudza iye, anawafunsa ophunzirawo kuti: “Koma inu mutani kuti Ine ndine yani?” Nkhani ya mu Uthenga Wabwino wa Mateyu imanena zomwe Petro anayankha. Iye anati: “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” (Mateyu 16:15, 16) Ophunzira ena analinso ndi maganizo omwewo. Natanayeli yemwe kenako anadzakhala mtumwi, anauza Yesu kuti: “Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israyeli.” (Yohane 1:49) Yesu mwiniyo anatchulapo kufunika kwa udindo wake. Iye anati: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” (Yohane 14:6) Pa zochitika zosiyanasiyana Yesu anali kudzitcha “Mwana wa Mulungu.” (Yohane 5:24, 25; 11:4) Ndipo anapereka umboni woti analidi mwana wa Mulungu mwakuchita zodabwitsa ngakhale kuukitsa akufa.

Kodi Pali Chifukwa Chomveka Chokayikirira?

Kodi tingakhulupiriredi nkhani zokhudza Yesu zomwe Mauthenga Abwino amanena? Kodi Mauthenga Abwino amasimbadi za Yesu weniweni? Malemu Frederick F. Bruce, yemwe anali pulofesa wamaphunziro wofufuza ndi kufotokoza Baibulo pa yunivesite ya Manchester ku England ananena kuti: “Nthaŵi zambiri n’kosatheka kutsutsa mfundo iliyonse ya zomwe zinalembedwa kale m’Baibulo kapena m’mabuku ena, mwa kupereka umboni wa zomwe zinachitika kalelo. Ndi bwino kungokhulupirira kuti wolembayo analembadi zoona zokhazokha chifukwa ngati zolemba zakezo zinakhazikika ndiye kuti n’zoona. . . . Mfundo ya Akristu yakuti Chipangano Chatsopano ndi mawu opatulika siingakhale chifukwa chonenera kuti nkhani zake n’zosadalirika.”

Atafufuza mfundo zokayikira mmene Mauthenga Abwino amam’fotokozera Yesu, James R. Edwards, yemwe ndi pulofesa wa zachipembedzo pa koleji ya Jamestown, m’chigawo cha North Dakota, U.S.A., analemba kuti: “Tingatsimikize ndi mtima wonse kuti Mauthenga Abwino ali ndi umboni wosiyanasiyana ndiponso wochititsa chidwi wokhudza zoona zake zenizeni za Yesu. . . . Ndipo yankho lanzeru pa funso lakuti n’chifukwa chiyani Mauthenga Abwino amam’fotokoza Yesu motero n’lakuti, zomwe amanenazo ndimo mmene Yesuyo analili. Munthu akaŵerenga Mauthenga Abwino amaona malingaliro omwe Yesu anasiyira otsatira ake oti iyeyo anatumidwadi ndi Mulungu ndipo kuti anam’patsa mphamvu zoyeneradi Mwana wa Mulungu ndiponso Mtumiki wake.” *

Kufunafuna Yesu

Kodi mabuku ena osati Baibulo amanenanji pankhani ya Yesu Kristu? Kodi timadziŵa bwanji phindu la mabuku oterewa? Mabuku olembedwa ndi Tacitus, Suetonius, Josephus, Pliny Wamng’ono, ndiponso olemba ena angapo, amatchula za Yesu kambirimbiri. Ponena za mabuku ameneŵa, The New Encyclopædia Britannica (1995) imati: “Nkhani zosiyanasiyana za m’mabuku ameneŵa zimapereka umboni wakuti kalelo ngakhale anthu amene ankadana ndi Chikristu sanali kukayikira mpang’ono pomwe mbiri ya Yesu. Anthu anayamba kutsutsa mbiri ya Yesu kwanthaŵi yoyamba pazifukwa zosakwanira kumapeto kwa zaka za m’ma 1700, ndi m’kati mwa zaka za m’ma 1800 ndiponso kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900.”

N’zokhumudwitsa kuti akatswiri a masiku ano abisa zoona zake za Yesu weniweni chifukwa cha zomwe iwo akupeka, kukayikira kopanda nako nzeru, ndiponso njira zawo zopanda maziko, pofuna kupeza Yesu “weniweni” yemwe “analikodi kalelo.” Mwa kuchita zimenezi iwo ali ndi mlandu wopeka nthano zimene mwachinyengo amatsutsa nazo amene analemba Mauthenga Abwino. Ena akuyesetsa kuti akhale otchuka mwa kupeza njira zamakono zomwe zimawalepheretsa kufufuza moona mtima umboni wonena za Yesu. Chifukwa cha njira zoterozo, akatswiriwo amapeza “Yesu” wongoganizira.

Amene akufuna kudziŵa Yesu weniweni atha kum’peza m’Baibulo. Luke Johnson wa pasukulu ya zaumulungu ya Candler School of Theology pa yunivesite ya Emory yemwe ndi pulofesa wa Chipangano Chatsopano ndiponso chiyambi cha Akristu ananena kuti, ofufuza Yesu ambiri amanyalanyaza cholinga cha mfundo za m’Baibulo. Iye anatinso, n’zoona kuti n’kwabwinodi kufufuza zomwe Yesu anachita pankhani ya chikhalidwe, ndale, ndiponso miyambo ndi zikhulupiriro za anthu pa nthaŵi yomwe iye anali ndi moyo pano padziko lapansi. Komabe, kupeza Yesu amene akatswiriwo amati ndiye analiko, sindicho cholinga cha Malemba. Cholinga cha Malemba ndicho “kufotokoza makhalidwe a Yesu,” uthenga wake, ndiponso udindo wake monga Muwomboli. Choncho, kodi makhalidwe enieni a Yesu ndi uthenga wake zinali zotani?

Yesu Weniweni

Mauthenga Abwino anayi omwe ndi nkhani za m’Baibulo zosimba mbiri ya Yesu, amasonyeza kuti anali munthu wachifundo kwambiri. Chifundo ndiponso kukoma mtima zinam’chititsa Yesu kuthandiza anthu amene anali kuvutika ndi matenda, khungu, ndiponso mavuto ena. (Mateyu 9:36; 14:14; 20:34) Imfa ya bwenzi lake Lazaro ndiponso chisoni chomwe alongo ake anali nacho chinam’chititsa Yesu ‘kudzuma mumzimu, ndi kulira.’ (Yohane 11:32-36) Ndiponso Mauthenga Abwino amavumbula mmene Yesu ankamvera pa zochitika zosiyanasiyana. Anamva chisoni ndi munthu wakhate, anakondwa kwambiri pamene ophunzira ake zinawayendera bwino, anakwiya ndi anthu oumirira malamulo, ndiponso anakhumudwa ndi Yerusalemu yemwe anakana Mesiya.

Yesu ankati akachita chozizwitsa, iye nthaŵi zambiri anali kuyamikira zomwe wochitiridwa chozizwitsayo wachita. Nthaŵi ina anati: “Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” (Mateyu 9:22) Yesu anatamanda Natanayeli mwa kumutcha kuti: “Mwisrayeli weniweni, mwa iye mulibe chinyengo!” (Yohane 1:47, Today’s English Version) Pamene ena anaganiza kuti mphatso yomwe mkazi wina anapereka pothokoza kunali kuwononga ndalama, Yesu anamuikira kumbuyo mkaziyo ndipo ananena kuti nkhani ya kuwolowa manja kwake sidzaiŵalika. (Mateyu 26:6-13) Iye anali bwenzi lenileni lapamtima la otsatira ake ndipo “anawakonda kufikira chimaliziro.”​—Yohane 13:1; 15:11-15.

Mauthenga Abwino amasonyezanso kuti Yesu anali kuzindikira mwamsanga maganizo a anthu amene ankakumana nawo. Kaya akulankhula ndi mkazi pachitsime, mphunzitsi wa chipembedzo m’munda, kapena msodzi wa nsomba kunyanja, Yesu anali kulankhula zogwira mitima yawo. Yesu ankati akalankhula mawu ake oyamba, ambiri mwa anthu ameneŵa anali kuulula zakukhosi. Anali kukhudza kwambiri mtima wawo. Ambiri anali kumuunjirira Yesu ngakhale kuti panthaŵiyo mwina anthu sanali kuyandikira anthu apamwamba. Anthu anali kusangalala ndiponso kumasuka akakhala ndi Yesu. Ana nawonso anali kumasuka akakhala ndi Yesu. Pogwiritsa ntchito kamwana monga chitsanzo, Yesu sanangokaimika kutsogolo kwa ophunzira ake koma ‘anakayangata’ kamwanako. (Marko 9:36; 10:13-16) Inde, Mauthenga Abwino amasonyeza kuti Yesu anali munthu wachikoka choterocho moti mpaka anthu anakhala masiku atatu akungomvetsera mawu ake ochititsa chidwiwo.​—Mateyu 15:32.

Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, iye sanali kufufuza zolakwa za anthu kapena kuumitsa zinthu ndi kupondereza anthu amene anali kukhala nawo ndi kuwalalikira. (Mateyu 9:10-13; 21:31, 32; Luka 7:36-48; 15:1-32; 18:9-14) Yesu sanali kufuna zinthu mopambanitsa kwa anthu ena. Sanawonjezere mtolo wolemetsa pa mavuto omwe anthu anali nawo kale. Mmalo mwake, anati: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema . . . ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.” Ophunzira ake anaona kuti iye anali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima,” ndiponso kuti goli lake linali lofeŵa ndi katundu wake analidi wopepuka.​—Mateyu 11:28-30.

Mutha kuona m’nkhani za m’Mauthenga Abwino kuti khalidwe la Yesu linali logwirizana ndi choonadi. Zikanakhala zovuta kwambiri kuti anthu anayi osiyana apeka khalidwe la munthu wapamwamba kenako n’kulilemba mofanana m’nkhani zinayi zochititsa chidwi. Zikanakhala zosatheka kuti olemba osiyana anayi afotokoze za munthu mmodzimodziyo mofanana kwambiri ngati munthuyo akanakhala kuti sanakhaleko.

Wolemba mbiri, Michael Grant, anafunsa funso lochititsa munthu kuganiza kwambiri lakuti: “Zikutheka bwanji kuti Mauthenga Abwino onse amasimba za mwamuna wachinyamata wokongola yemwe anali kucheza ndi akazi amitundu yonse ngakhale a makhalidwe oipa popanda kukhala ndi maganizo owasirira, m’malo mwake, nthaŵi zonse akumasonyeza khalidwe labwino?” Yankho lomveka pa funso limeneli n’lakuti munthu woteroyo analikodi ndipo anachitadi monga momwe Baibulo limanenera.

Kugwirizana kwa Yesu Weniweni ndi Tsogolo Lanu

Kuwonjezera pa kufotokoza molondola za moyo wa Yesu ali pano padziko lapansi, Baibulo limasonyezanso kuti asanakhale munthu, iye analiko monga Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Zaka masauzande aŵiri zapitazi, Mulungu anasamutsira moyo wa Mwana wake wakumwamba m’mimba mwa namwali wachiyuda kuti iye akabadwe monga munthu. (Mateyu 1:18) Yesu panthaŵi ya utumiki wake wa padziko lapansi ankalalikira Ufumu wa Mulungu kuti ndiwo njira yokha yothetsera mavuto a anthu ndipo anaphunzitsa ophunzira ake kupitiriza ntchito yolalikira imeneyi.​—Mateyu 4:17; 10:5-7; 28:19, 20.

Pa Nisani 14 (mwina pa April 1), 33 C.E., Yesu anamugwira, kum’zenga mlandu, kumuweruza ndi kumupha pa mlandu wabodza wa kuukira boma. (Mateyu 26:18-20, 26:48–27:50) Imfa ya Yesu ndiyo dipo lowombolera anthu onse okhulupirira iye ku uchimo wawo ndiponso kuwatsegulira njira yopita ku moyo wosatha. (Aroma 3:23, 24; 1 Yohane 2:2) Pa Nisani 16, Yesu anaukitsidwa ndipo patapita nthaŵi anakwera kumwamba. (Marko 16:1-8; Luka 24:50-53; Machitidwe 1:6-9) Yesu woukitsidwayo tsopano ndi Mfumu imene Yehova waisankha ndipo ali ndi mphamvu zokwanira zokwaniritsira chifuniro cha Mulungu choyambirira kwa anthu. (Yesaya 9:6, 7; Luka 1:32, 33) Inde, Baibulo limanena kuti Yesu ndiye m’tsogoleri pa ntchito yokwaniritsa chifuniro cha Mulungu.

M’zaka za zana loyamba, anthu miyandamiyanda anavomereza kuti Yesu analidi Mesiya wolonjezedwayo, kapena kuti Kristu. Anazindikira kuti Yesu anatumidwa kudzatsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndiponso kudzafa monga dipo lowombolera anthu. (Mateyu 20:28; Luka 2:25-32; Yohane 17:25, 26; 18:37) Anthu sakanalolera kuzunzidwa koopsa chifukwa chokhala ophunzira a Yesu ngati akanapanda kudziŵa zoona zake zokhudza Yesuyo. Iwo molimba mtima ndiponso mwachangu anayamba kugwira ntchito yomwe anawalamulira yoti ‘aphunzitse anthu a mitundu yonse.’​—Mateyu 28:19.

Lerolino, miyandamiyanda ya Akristu oona mtima ndiponso ozindikira amadziŵa kuti Yesu ndi weniweni osati munthu wa m’nthano ayi. Iwo amavomereza kuti iye ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu womwe unakhazikitsidwa kumwamba, ndipo kuti posachedwapa adzalamulira dziko lonse lapansi. Boma la Mulungu limeneli ndi nkhani yosangalatsa kwambiri chifukwa limalonjeza kuti lidzathetsa mavuto a dziko lapansi. Akristu oona amathandiza mokhulupirika Mfumu imeneyi yomwe Yehova anaisankha. Amachita zimenezi mwa kulalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” kwa anthu ena.​—Mateyu 24:14.

Anthu amene akuthandiza zomwe Ufumu wakonza kudzera mwa Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo, adzasangalala ndi madalitso osatha. Inunso mutha kupeza madalitso amenewo! Amene amafalitsa magazini ino ali okonzeka kukuthandizani kudziŵa Yesu weniweni.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani chaputala 5 ndi 7 cha buku lakuti Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mmenemo tinafotokoza mwatsatanetsatane nkhani za m’Mauthenga Abwino.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 6]

Zomwe Anthu Ena Anena

“Ndimaona kuti Yesu wa ku Nazarete ndi mmodzi mwa aphunzitsi amphamvu kwambiri omwe anakhalapo padziko lapansi. . . . Ahindu ndingawauze kuti ngati sangaphunzire zomwe Yesu anaphunzitsa ndiye kuti moyo wawo n’ngopereŵera.” Anatero Mohandas K. Gandhi, m’buku lakuti The Message of Jesus Christ.

“Anali munthu weniweni, wamphumphu, wosasinthasintha, wangwiro, wakhalidwe, koma wapamwamba kwambiri kuposa anthu onse. Iye sangakhale wachinyengo kapena wopeka. . . . Zikanafunika munthu woposa Yesu kuti apange Yesu.” Anatero Philip Schaff, m’buku lakuti History of the Christian Church.

“Zoti anthu wamba ochepa anangopeka nkhani ya munthu wosonkhezera kwambiri ndi wosangalatsa chotero, wakhalidwe lapamwamba chotero, ndiponso chithunzi champhamvu cha ubale wa anthu ngati chimenecho, zingakhale chozizwitsa chachikulu kwambiri kuposa china chilichonse cholembedwa m’Mauthenga Abwino.” Anatero Will Durant, m’buku lakuti Caesar and Christ.

“Zingakhale zovuta kumvetsa kuti magulu onseŵa achipembedzo omwe afala padziko lonse lapansi anasonkhezeredwa ndi munthu wongopeka amene sanakhaleko, ndiponso kuti yangokhala njira yolimbikitsira chipembedzo poganizira mfundo yakuti pali anthu enieni ambiri amene ayesetsa kuyambitsa chipembedzo koma alephera.” Anatero Gregg Easterbrook, m’buku lakuti Beside Stil Waters.

“Monga wolemba mbiri, ndine wotsimikiza kotheratu kuti zilizonse zimene Mauthenga Abwino amanena, si nthano ayi. Sanazilembe mwa luso losonyeza kuti ndi nthano. . . . Mbali zambiri za moyo wa Yesu sitikuzidziŵa ndipo anthu olemba nthano sangalole kuti zimenezi zikhale choncho.” Anatero C. S. Lewis, m’buku lakuti God in the Dock.

[Zithunzi patsamba 7]

Mauthenga Abwino amavumbula mmene Yesu ankamvera pa zochitika zosiyanasiyana