Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kodi Anthu Anena Kuti Ine Ndine Yani?”

“Kodi Anthu Anena Kuti Ine Ndine Yani?”

 “Kodi Anthu Anena Kuti Ine Ndine Yani?”

NTHAŴI ya Khirisimasi yafikanso. Anthu padziko lonse amakondwerera tsiku la kubadwa kwa winawake. Kodi winawakeyo n’ndani? Kodi ndi Mwana wa Mulungu kapena Myuda wamba wodzipereka yemwe zolinga zake zinali kukonzanso chipembedzo chomwe chinali chofala m’dera lakwawo m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino? Kodi mwina ndi munthu woteteza amphaŵi kapena woukira yemwe anaopseza kwambiri Ufumu wa Roma moti mpaka anamupha, kapena anali munthu wanzeru kwambiri yemwe anali kudzitama chifukwa cha zomwe ankadziŵa ndiponso nzeru zochuluka zomwe anali nazo? Ndithudi, mpake kudzifunsa kuti: ‘Kodi Yesu Kristu anali ndani?’

Yesu nayenso anali ndi chidwi chofuna kudziŵa mmene anthu anali kuyankhira funso limeneli. Iye nthaŵi ina anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthu anena kuti Ine ndine yani?” (Marko 8:27) Kodi anafunsiranji funso limeneli? Anthu ambiri anali atayamba kale kusiya kum’tsatira. Ena mwachionekere anali atasokonezeka ndiponso kukhumudwa Yesu atakana zomwe iwo ankafuna zoti amulonge ufumu. Komanso adani a Yesu atam’kayikira, iye sanaonetse chizindikiro chochokera kumwamba chotsimikiza kuti iye anali ndani. Choncho, kodi ophunzira ake anayankha kuti chiyani pa funso lomwe iye anawafunsa? Iwo anatchula zina mwa zomwe anthu ambiri ankanena. Iwo anati: “Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.” (Mateyu 16:13, 14) Iwo sanatchule mawu achipongwe ambiri onena za Yesu omwe anali mkamwamkamwa ku Palesitina konse. Anthu ankanena kuti Yesu anali  wochitira chipongwe Mulungu, kathyali, mneneri wonyenga, ndiponso wamisala.

Maganizo Osiyanasiyana Onena za Yesu

Ngati Yesu akanafunsa funso lomwelo lerolino, mwina akanalifunsa motere: “Kodi akatswiri amaphunziro akunena kuti Ine ndine yani?” Yankho lake likanakhalanso lakuti: Pali maganizo osiyanasiyana onena za Yesu. David Tracy wa pa yunivesite ya Chicago anati:“Anthu ambiri akhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya mmene Yesu ankaonekera, zomwe ankalankhula ndiponso zomwe ankachita.” Kwa zaka 100 zapitazi, akatswiri amaphunziro agwiritsa ntchito njira zachikhalidwe ndi miyambo ya anthu zovuta kuzimvetsa poyankha funso loti kodi Yesu kwenikweni anali ndani? Ndiyeno, kodi iwo amaganiza kuti Yesu n’ndani?

Akatswiri ena amanenabe kuti Yesu wamakedzana anali mneneri wachiyuda wonena za kutha kwa dziko yemwe ankapempha anthu kuti alape. Komabe, akatswiriwo anasiya kumutcha kuti ndi Mwana wa Mulungu, Mesiya, ndiponso Mombolo. Ambiri amakayikira nkhani ya m’Baibulo yoti Yesu anachokera kumwamba ndiponso ya kuuka kwake. Kwa anthu ena, Yesu anali chabe munthu amene chifukwa cha khalidwe lake labwino ndiponso zomwe anali kuphunzitsa anatha kuyambitsa zikhulupiriro zambiri zomwe m’kupita kwa nthaŵi zinakhala Chikristu. Komanso monga momwe magazini ya Theology Today inanenera, anthu ena amaonabe kuti Yesu anali “wopeza ena zifukwa, munthu wanzeru wongoyendayenda, mlimi wa m’nthano, munthu wodziŵa kusonkhanitsa anthu, wotsutsa miyambo ya anthu, munthu wanzeru wosokoneza yemwe ankayenda m’misewu kuuza mfundo zake anthu amene anali kukhala m’midzi mmene munali umphaŵi ndi chiwawa ku dera losatukuka la ku Palesitina.”

Palinso maganizo ena ambiri achilendo. Zithunzi za Yesu wakuda zayamba kuoneka pa zikuto za nyimbo za rap, m’misika ya zosemasema ya m’matauni ndiponso m’magule. * Ena amanena kuti Yesu anali wamkazi. M’chilimwe cha mu 1993, alendo omwe anapita ku chionetsero cha zamalonda cha Orange County Fair mumzinda wa California anaona chiboliboli cha “Kristu” wamkazi wamaliseche wotchedwa “Christie” atam’pachika pa mtanda. Panthaŵi imodzimodziyo ku New York nakonso anali kuonetsa “Yesu” wamkazi wotchedwa “Christa” atam’pachika pa mtanda. Ziboliboli ziŵiri zonsezi zinayambitsa maganizo ambiri olakwika. Kumayambiriro a 1999, buku “losimba za chikondi [chimene] Yesu Wachinyamata ndi galu wake Mngelo, anali kusonyezana,” linayamba kupezeka m’masitolo a mabuku. Mgwirizano wawo akuti unali “wokhudza mtima mwauzimu ndipo umasonyeza mmene mnyamata ndi galu alili ofunitsitsa kuferana.”

Kodi Kudziŵa Yesu Kuli N’phindu Lanji?

N’chifukwa chiyani muyenera kukhala ndi chidwi chofuna kudziŵa kuti Yesu anali ndani ndiponso kuti iye n’ndani lerolino? Mwa zina, n’chifukwa cha mfundo yomwe Napolioni anatchula kuti: “Yesu Kristu walimbikitsa ndiponso kulamulira otsatira Ake popanda Iye kuoneka ndi maso.” Yesu wakhudza miyoyo ya anthu miyandamiyanda kwa zaka masauzande aŵiri chifukwa cha ziphunzitso zake zamphamvu ndiponso khalidwe lake. Wolemba wina moyenerera anati: “Magulu ankhondo onse amene akhalako, sitima zonse za nkhondo ya pamadzi zomwe zapangidwa, nyumba zamalamulo zonse zimene zakhalako, mafumu onse amene alamulira, zonse kuziphatikiza pamodzi, sizinakhudze mwamphamvu miyoyo ya anthu padziko lapansi pano monga amachitira Yesu.”

Komanso, n’kofunika kudziŵa kuti Yesu anali ndani ndipo kuti iye ndani lerolino chifukwa chakuti tsogolo lanu lili m’manja mwake. Muli ndi mwayi wodzakhala nzika za Ufumu wa Mulungu womwe ndi boma la kumwamba lomwe linakhazikitsidwa kale m’manja mwa Yesu. Dziko lathu lamavutoli lidzakhalanso malo abwino ndi ochititsa chidwi mu ulamuliro wa Yesu. Ulosi wa m’Baibulo umatitsimikizira kuti Ufumu wa Yesu udzadyetsa anjala, kusamalira aumphaŵi kuchiritsa odwala, ndiponso kuukitsa akufa.

Ndithudi, mukulakalaka mutadziŵa kuti ndi munthu wamtundu wanji amene akulamulira boma lofunika ngati limeneli. Nkhani yotsatirayi ikuthandizani kudziŵa Yesu weniweni.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Kuti mudziŵe mmene Yesu ankaonekera, onani nkhani yakuti “Kodi Yesu Ankaoneka Bwanji?” mu Galamukani! ya December 8, 1998.