Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:

Kodi Khoti la Federal Constitution la ku Germany linathandiza kupambana mlandu wotani wokhudza chipembedzo?

Khotilo linasintha zomwe khoti lina linagamula moipira Mboni za Yehova ndiponso kuti izo sizidziŵika monga bungwe lovomerezeka ndi lamulo la boma. Chigamulo chabwinocho chinanena kuti, ngati munthu ‘atsatira zikhulupiriro zake zachipembedzo’ koposa lamulo la Boma ndiye kuti sakupitirira malire a ufulu wachipembedzo.​—8/15, tsamba 8.

Kodi Yobu anavutika kwa nthaŵi yaitali motani?

Buku la Yobu silimanena kuti iye anavutika kwa zaka zambiri. Kuvutika kwa Yobu ndiponso kutha kwa mavuto akewo kuyenera kuti kunatenga miyezi yoŵerengeka chabe mwinanso osakwana ndi chaka chomwe.​—8/15, tsamba 31.

N’chifukwa chiyani tingatsimikize kuti Mdyerekezi alipodi, si nthano chabe?

Yesu Kristu ankadziŵa kuti Mdyerekezi alipodi. Yesu anayesedwa ndi munthu weniweni osati zinthu zoipa za m’thupi lake lomwe. (Mateyu 4:1-11; Yohane 8:44; 14:30)​—9/1, masamba 5-6.

Lemba la Miyambo 10:15 limati: “Chuma cha wolemera ndi mudzi wake wolimba; koma umphaŵi wawo uwononga osauka.” Kodi zimenezi n’zoona motani?

Chuma chingatchinjirize kumavuto ena amene angagwe mwadzidzidzi, monga momwe tauni yam’mpanda nthaŵi zina imatchinjirizira anthu amene akukhalamo. Ndipo umphaŵi ungakhale wopweteka pakagwa vuto mwadzidzidzi.​—9/15, tsamba 24.

Kodi anthu m’nthaŵi ya Enosi anayamba kutchula dzina la Yehova mulingaliro lotani? (Genesis 4:26)

Dzina la Mulungu linayamba kugwiritsidwa ntchito kuchokera pachiyambi cha mbiri ya anthu. Chotero, kutchula dzina la Mulungu komwe kunayamba m’nthaŵi ya Enosi sikunali kuitanira pa Yehova m’chikhulupiriro. Anthu ayenera kuti ankadzitcha kuti Yehova kapena ankapatsa anthu ena dzinali ndipo mwa kulambira anthu ameneŵa ankati akulambira Mulungu.​—9/15 tsamba 29.

Kodi liwu lakuti “kulanga” monga mmene aligwiritsira ntchito m’Baibulo limatanthauzanji?

Liwu limeneli silitanthauza kuzunza kapena nkhanza. (Miyambo 4:13; 22:15) Tanthauzo lalikulu la liwu la Chigiriki limene analimasulira kuti “kulanga” limanena za kulangiza, kuphunzitsa, kuwongolera, ndipo nthaŵi zina, kukwapula ndithu koma mwachikondi. Njira yofunika kwambiri yomwe makolo angatsanzirire Yehova ndiyo mwa kuyesetsa kulankhulana ndi ana awo nthaŵi zonse. (Ahebri 12:7-10)​—10/1, masamba 8, 10.

Kodi Akristu enieni lerolino angasonyeze motani kuti amakonda ulamuliro wa Mulungu?

Polalikira Ufumu wa Mulungu, Mboni za Yehova siziloŵerera m’nkhani zandale kapena kupanga magulu oukira boma ngakhale m’mayiko omwe amaziletsa kugwira ntchito yawo. (Tito 3:1) M’malo mwake, zimayesetsa kuthandiza anthu monga momwe Yesu ndi ophunzira ake oyambirira anachitira. Zimathandiza anthu kuti aphunzire makhalidwe abwino a m’Baibulo monga kuona mtima, kudzisunga, ndiponso makhalidwe abwino a ku ntchito.​—10/15, tsamba 6.

Kodi madzi opatsa moyo akuyenda motani ku Andes?

Mboni za Yehova zikuyesetsa kulalikira choonadi cha m’Baibulo kwa anthu a ku Andes ngakhalenso m’zinenero ziŵiri za kumeneko, Quechua ndi Aymara. Mboni zimalalikira kwa anthu amene amakhala pa zilumba za nyanja ya Titicaca, komanso pa zilumba “zoyandama” zimene amazipanga ndi udzu womwe umamera m’madzi.​—10/15, masamba 8-10.

Kodi Mulungu wapereka chiyani kuti chititsogolere chomwe tingachifanizire ndi kompyuta youlutsira ndege zamakono zonyamula anthu?

Mulungu anaika mwa anthu chinthu choti chiziwatsogolera pankhani za makhalidwe. Chinthu chimenechi ndicho chikumbumtima chathu chobadwa nacho. (Aroma 2:14, 15)​—11/1, masamba 3-4.

N’chifukwa chiyani imfa ya Yesu ili yamtengo wapatali kwambiri?

Munthu wangwiro Adamu atachimwa, anataya moyo wake ndiponso wa mbadwa zake. (Aroma 5:12) Yesu monga munthu wangwiro, anapereka moyo wake nsembe kuti ikhale dipo lomwe limachititsa kuti anthu okhulupirika akapeze moyo wosatha.​—11/15, masamba 5-6.

Kodi Asikuti otchulidwa pa Akolose 3:11 anali ndani?

Asikuti anali anthu omwe sanali kukhazikika malo amodzi. Ankalamulira dera lalikulu la udzu wokhawokha la ku Ulaya ndi Asia kuchokera mu 700 mpaka 300 B.C.E. Asikuti anali akatswiri pokwera akavalo ndiponso okonda nkhondo kwambiri. Choncho, lemba la Akolose 3:11 liyenera kuti linali kutanthauza osati mtundu winawake wa anthu koma gulu lonse la anthu osadziŵa zinthu.​—11/15, masamba 24-5.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti Lamulo la Chikhalidwe n’lofunika kulisamalira nthaŵi zonse?

Ayuda, Abuda, Agiriki anzeru, ndi Confucius, ankalimbikitsa mwambi wa chikhalidwe umenewu. Komabe, zomwe Yesu ananena pa Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri zimafuna kuchitapo kanthu ndiponso zimakhudza miyoyo ya anthu amene akhala ndi moyo nthaŵi zosiyanasiyana kulikonse. (Mateyu 7:12)​—12/1, tsamba 3.