Oweruza 13:1-25

13  Tsopano ana a Isiraeli anayambiranso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ moti Yehova anawapereka m’manja mwa Afilisiti+ zaka 40.  Pa nthawiyi panali mwamuna wina wa ku Zora+ wa fuko la Dani,+ ndipo dzina lake anali Manowa.+ Mkazi wake anali wosabereka, moti analibe mwana.+  Ndiyeno tsiku lina, mngelo wa Yehova anaonekera kwa mkaziyo+ ndi kumuuza kuti: “Tamvera, panopa ndiwe wosabereka ndipo ulibe mwana. Koma udzatenga pakati ndi kubereka mwana wamwamuna.+  Choncho samala, usamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa,+ ndipo usadye chilichonse chodetsedwa.+  Pakuti udzatenga pakati ndi kubereka mwana wamwamuna. M’mutu mwake musadzadutse lezala+ chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri+ wa Mulungu potuluka m’mimba.+ Iye adzakhala patsogolo populumutsa Isiraeli m’manja mwa Afilisiti.”+  Kenako mkaziyo anapita kukauza mwamuna wake kuti: “Munthu wa Mulungu woona anabwera kwa ine, ndipo maonekedwe ake anali ofanana ndi mngelo wa Mulungu woona,+ maonekedwe ochititsa mantha kwambiri.+ Koma sindinam’funse kumene wachokera ndiponso sanandiuze dzina lake.+  Koma iye wandiuza kuti, ‘Pakuti udzakhala ndi pakati ndi kubereka mwana wamwamuna.+ Choncho, usamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, ndipo usadye chilichonse chodetsedwa, chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri wa Mulungu potuluka m’mimba mpaka pa tsiku la imfa yake.’”+  Pamenepo Manowa anayamba kuchonderera Yehova kuti: “Yehova,+ lolani kuti munthu wa Mulungu woona amene munam’tuma, abwerenso kuti adzatilangize+ zoyenera kuchita ndi mwana amene adzabadweyo.”+  Mulungu woona anamvetsera mawu a Manowa,+ moti mngelo wa Mulungu woona uja anabweranso kwa mkaziyo, ndipo anam’peza atakhala pansi kunja kwa mzinda. Pa nthawiyi sanali limodzi ndi mwamuna wake Manowa. 10  Nthawi yomweyo mkaziyo ananyamuka mofulumira ndi kuthamanga kukauza mwamuna wake+ kuti: “Munthu amene anabwera tsiku lija waonekeranso kwa ine.”+ 11  Atatero, Manowa ananyamuka ndi kupitira limodzi ndi mkazi wakeyo kwa munthuyo ndipo anam’funsa kuti: “Kodi ndiwe amene unalankhula ndi mkazi uyu?”+ Poyankha iye anati: “Inde ndine.” 12  Ndiyeno Manowa anati: “Mawu ako akwaniritsidwe. Koma kodi mwanayo tidzamulere bwanji, nanga ntchito yake idzakhala yotani?”+ 13  Pamenepo mngelo wa Yehova anauza Manowa kuti: “Mkaziyu apewe kuchita zonse zimene ndamuletsa.+ 14  Asadye chilichonse chochokera ku mphesa zopangira vinyo, asamwe vinyo+ kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, ndipo asadye chilichonse chodetsedwa.+ Asunge zonse zimene ndamuuza.”+ 15  Tsopano Manowa anauza mngelo wa Yehova kuti: “Tiloleni tikuchedwetseni pang’ono, kuti tikukonzereni kamwana ka mbuzi.”+ 16  Poyankha, mngelo wa Yehova anauza Manowa kuti: “Ngakhale mundichedwetse sindidya mkate wanu. Koma ngati mungathe kupereka kwa Yehova nsembe yopsereza,+ perekani.” Manowa ananena zimenezi chifukwa sanadziwe kuti anali mngelo wa Yehova. 17  Ndiyeno Manowa anafunsa mngelo wa Yehova kuti: “Dzina lanu ndani?+ Tikufuna tidzakulemekezeni mawu anu akadzakwaniritsidwa.” 18  Koma mngelo wa Yehovayo anamuyankha kuti: “Usandifunse dzina langa, chifukwa dzina langa ndi lodabwitsa.” 19  Pamenepo Manowa anatenga kamwana ka mbuzi ndi nsembe yambewu n’kuzipereka nsembe kwa Yehova pathanthwe.+ Ndipo Mulungu anali kuchita zodabwitsa, Manowa ndi mkazi wake akuonerera. 20  Pamene lawi la moto linali kukwera m’mwamba kuchokera paguwalo, mngelo wa Yehova nayenso anakwera kumwamba m’lawi la moto wa paguwa lansembelo, Manowa ndi mkazi wake akuonerera.+ Nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 21  Mngelo wa Yehova uja sanaonekerenso kwa Manowa ndi mkazi wake. Pamenepo Manowa anadziwa kuti anali mngelo wa Yehova.+ 22  Ndiyeno Manowa anauza mkazi wake kuti: “Ife tifa basi,+ chifukwa taona Mulungu.”+ 23  Koma mkazi wakeyo anati: “Yehova akanakhala kuti akufuna kutipha, sakanalandira m’manja mwathu nsembe yopsereza ndi nsembe yathu yambewu.+ Komanso sakanationetsa ndi kutiuza zinthu zonsezi.”+ 24  Patapita nthawi, mkaziyo anabereka mwana wamwamuna ndipo dzina lake anamutcha kuti Samisoni.+ Mnyamatayo anali kukula, ndipo Yehova anapitiriza kumudalitsa.+ 25  Kenako mzimu wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa iye ku Mahane-dani+ pakati pa Zora+ ndi Esitaoli.+

Mawu a M'munsi