Oweruza 18:1-31

18  Masiku amenewo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Ndipo m’masiku amenewo fuko la Dani+ linali kufuna cholowa chake kuti likakhale kumeneko, chifukwa mpaka pa nthawi imeneyi linali lisanalandirebe cholowa pakati pa mafuko onse a Isiraeli.+  Nthawi ina, ana a Dani anatumiza amuna asanu a m’banja lawo, amuna olimba mtima ochokera pakati pawo, kuchokera kumizinda ya Zora+ ndi Esitaoli+ kuti akazonde dziko ndi kuliyendera. Ndiyeno anawauza kuti: “Pitani mukaone+ dzikolo.” Choncho anafika kudera lamapiri la Efuraimu,+ mpaka kunyumba ya Mika,+ ndipo anagona kumeneko.  Atayandikira nyumba ya Mika anamva ndi kuzindikira mawu a mnyamata uja, Mlevi. Motero anapatukira kumeneko ndi kum’funsa kuti: “Wabwera ndi ndani kuno ndipo ukudzachita chiyani? Chimene ukufuna kuno n’chiyani?”  Poyankha iye anati: “Mika anagwirizana ndi ine kuti andilembe ntchito,+ ndi cholinga choti ndizitumikira monga wansembe+ wake.”  Ndiyeno iwo anamuuza kuti: “Tifunsire+ kwa Mulungu+ kuti tidziwe ngati kumene tikupita tidzayendako bwino.”  Pamenepo wansembeyo anawauza kuti: “Pitani mu mtendere. Yehova ali ndi inu pa ulendowu.”  Choncho amuna asanu aja anapitiriza ulendo wawo ndipo anafika kumzinda wa Laisi.+ Kumeneko anaona kuti anthu a mumzindawo anali kukhala mosadalira aliyense, malinga ndi chikhalidwe cha Asidoni. Iwo anali kukhala phee, mosatekeseka,+ ndipo panalibe amene anawagonjetsa n’kumawachitira nkhanza kapena kuwavutitsa m’dzikolo. Kuwonjezera apo, anali kukhala kutali kwambiri ndi Asidoni+ ndipo sanali kuyenderana ndi anthu a m’madera ena.  Patapita nthawi, anafika kwa abale awo ku Zora+ ndi ku Esitaoli.+ Ndipo abale awo anayamba kuwafunsa kuti: “Munayendako bwanji?”  Poyankha iwo anati: “Nyamukani, tiyeni tipite kukamenyana nawo, chifukwa ife taliona dzikolo ndipo ndi labwino kwambiri.+ Mukuzengerezatu. Musachite ulesi, koma nyamukani mukatenge dzikolo kukhala lanu.+ 10  Mukakafika kumeneko, mukapeza anthu okhala mosatekeseka,+ ndipo dzikolo ndi lalikulu kwambiri. Mulungu walipereka m’manja mwanu,+ ndipo ndi dziko losasowa kena kalikonse kopezeka padziko lapansi.”+ 11  Pamenepo amuna 600 ovala zida zankhondo, ochokera m’banja la Dani,+ ananyamuka ku Zora ndi ku Esitaoli.+ 12  Amunawa ananyamuka pa ulendo wawo ndipo anayenda mpaka kukafika pafupi ndi Kiriyati-yearimu+ ku Yuda, n’kumanga msasa pamenepo. N’chifukwa chake malowo amatchedwa dzina lakuti Mahane-dani*+ kufikira lero. Malo amenewa ali kumadzulo kwa Kiriyati-yearimu. 13  Atachoka pamenepo, anayenda ndi kukafika kudera lamapiri la Efuraimu, mpaka kukafika kunyumba ya Mika.+ 14  Ndiyeno amuna asanu amene anapita kukazonda+ dziko la Laisi+ aja, anauza abale awo kuti: “Kodi mukudziwa kuti m’nyumba izi muli efodi, aterafi,+ chifaniziro chosema+ ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula?+ Ndiyetu dziwani chochita.”+ 15  Choncho anapatukira kumeneko ndi kufika panyumba ya mnyamata uja, Mlevi,+ kunyumba ya Mika. Pamenepo anayamba kulonjerana naye.+ 16  Pamenepa n’kuti amuna 600 ovala zida zankhondo aja,+ ana a Dani,+ ataima pachipata. 17  Tsopano amuna asanu amene anapita kukazonda dziko+ aja anapita kuti akalowe m’nyumba ndi kutenga chifaniziro chosema,+ efodi,+ aterafi+ ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ (Wansembe+ uja anali ataima pachipata pamodzi ndi amuna 600 ovala zida zankhondowo.) 18  Amuna asanuwo analowa m’nyumba ya Mika ndi kutenga chifaniziro chosema, efodi, aterafi ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Atatero wansembeyo+ anawafunsa kuti: “Mukutani kodi?” 19  Iwo anamuyankha kuti: “Khala chete. Gwira pakamwa pako, ndipo upite nafe kuti ukakhale tate+ ndi wansembe+ wathu. Chabwino n’chiti, kuti upitirize kukhala wansembe m’nyumba ya munthu mmodzi,+ kapena kuti ukhale wansembe wa banja ndi fuko lonse mu Isiraeli?”+ 20  Mtima wa wansembeyo unasangalala+ atamva mawu amenewa, ndipo iye anatenga efodi, aterafi ndi chifaniziro chosema+ n’kulowa pakati pa anthuwo. 21  Pamenepo anatembenuka n’kuyamba ulendo wawo, ndipo anaika patsogolo ana, ziweto ndi zinthu zamtengo wapatali.+ 22  Ndiyeno atayenda kamtunda ndithu kuchokera panyumba ya Mika, anthu a m’nyumba zoyandikana ndi nyumba ya Mika+ anasonkhanitsidwa pamodzi n’kuyamba kutsatira ana a Dani kuti apezane nawo. 23  Pamene anthuwo anali kufuulira ana a Dani, ana a Daniwo anatembenuka ndi kufunsa Mika kuti: “Vuto lako n’chiyani+ kuti usonkhanitse anthu onsewa?” 24  Poyankha, iye anati: “Mwatenga milungu yanga+ imene ndinapanga,+ ndipo mwatenganso wansembe+ n’kumapita naye. Nanga ine nditsala ndi chiyani?+ Ndiye mungandifunse bwanji kuti, ‘Vuto lako n’chiyani?’” 25  Pamenepo ana a Dani anamuuza kuti: “Usayandikire kuno ndipo tisamvenso mawu akowo, chifukwa anthu olusa+ angakupwetekeni, ndipo iweyo ungataye moyo wako ndi kutayitsa moyo wa anthu a m’nyumba yako.” 26  Zitatero ana a Dani anapitiriza ulendo wawo, ndipo Mika anaona kuti anali amphamvu kuposa iye.+ Chotero Mika anatembenuka ndi kubwerera kunyumba kwake. 27  Ana a Dani anatenga zimene Mika anapanga komanso wansembe+ wake, ndipo anapitiriza ulendo wawo wa ku Laisi+ kukaukira anthu aphee ndi osatekeseka.+ Atafika kumeneko anapha anthuwo ndi lupanga+ n’kutentha mzindawo ndi moto.+ 28  Iwo analibe owalanditsa chifukwa mzindawo unali kutali ndi Sidoni+ ndipo sankayenderana ndi anthu a m’madera ena. Komanso, mzindawo unali m’chigwa cha Beti-rehobu.+ Choncho ana a Dani anamanganso mzindawo ndi kuyamba kukhalamo.+ 29  Kuwonjezera apo, anatcha mzindawo kuti Dani, kutengera dzina la bambo awo lakuti Dani,+ amene anali wobadwa kwa Isiraeli.+ Ngakhale zili choncho, dzina loyamba la mzindawo linali Laisi.+ 30  Kenako ana a Dani anadziimikira chifaniziro chosema+ chija, ndipo Yonatani+ mwana wa Gerisomu,+ mwana wa Mose, pamodzi ndi ana ake, anakhala ansembe a fuko la Dani kufikira tsiku limene anthu a m’dzikolo anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.+ 31  Ndipo chifaniziro chosema chimene Mika anapanga chinakhalabe choimiritsa masiku onse amene nyumba+ ya Mulungu woona inakhalabe ku Silo.+

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza, “Msasa wa Dani.”