Oweruza 10:1-18
10 Pambuyo pa Abimeleki, panabwera Tola, munthu wa fuko la Isakara, amene anapulumutsa+ Isiraeli. Iye anali kukhala ku Samiri m’dera lamapiri la Efuraimu,+ ndipo anali mwana wa Puwa, amene anali mwana wa Dodo.
2 Iye anaweruza Isiraeli zaka 23. Kenako anamwalira ndipo anaikidwa ku Samiri.
3 Pambuyo pa Tola panabwera Yairi wa ku Giliyadi.+ Iye anaweruza Isiraeli zaka 22.
4 Iye anadzakhala ndi ana 30 aamuna amene anali kuyenda pa abulu 30,+ ndipo iwo anali ndi mizinda 30. Mizinda imeneyi ikutchedwabe kuti Havoti-yairi*+ kufikira lero, ndipo ili m’dziko la Giliyadi.
5 Kenako Yairi anamwalira ndipo anaikidwa ku Kamoni.
6 Zitatero, ana a Isiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo anayamba kutumikira Abaala,+ zifaniziro za Asitoreti,+ milungu ya ku Siriya,+ milungu ya ku Sidoni,+ milungu ya ku Mowabu,+ milungu ya ana a Amoni+ ndi milungu ya Afilisiti.+ Motero iwo anasiya Yehova ndipo sanam’tumikire.+
7 Pamenepo, mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Isiraeli,+ moti anawagulitsa+ kwa Afilisiti+ ndi kwa ana a Amoni.+
8 Choncho, amenewa anazunza ndi kupondereza kwambiri ana a Isiraeli chaka chimenecho. Kwa zaka 18, anapondereza ana onse a Isiraeli amene anali kum’mawa kwa Yorodano, m’dziko la Aamori limene linali ku Giliyadi.
9 Ndipo ana a Amoni anali kuwoloka Yorodano kukamenyana ndi fuko la Yuda, la Benjamini, ndi la Efuraimu, moti Isiraeli anasautsika kwambiri.+
10 Pamenepo ana a Isiraeli anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+ Iwo anati: “Takuchimwirani+ inu Mulungu wathu, chifukwa takusiyani ndipo tikutumikira Abaala.”+
11 Ndiyeno Yehova anauza ana a Isiraeli kuti: “Kodi Aiguputo,+ Aamori,+ ana a Amoni,+ Afilisiti,+
12 Asidoni,+ Aamaleki+ ndi Amidiyani+ atakuponderezani,+ sindinakupulumutseni m’manja mwawo mutafuulira kwa ine?
13 Koma inu munandisiya+ n’kuyamba kutumikira milungu ina.+ N’chifukwa chake sindidzakupulumutsaninso.+
14 Pitani, kapempheni thandizo kwa milungu+ imene mwasankhayo.+ Milungu imeneyo ndi imene ikupulumutseni pa nthawi ya nsautso yanu.”
15 Poyankha, ana a Isiraeli anauza Yehova kuti: “Tachimwa.+ Inuyo mutichite zilizonse zimene zingakukomereni m’maso mwanu.+ Koma chonde, ingotipulumutsani lero.”+
16 Atatero, iwo anayamba kuchotsa milungu yonse yachilendo pakati pawo+ n’kuyamba kutumikira Yehova,+ moti mtima wake+ unagwidwa ndi chisoni chifukwa cha kuvutika kwa ana a Isiraeli.+
17 Patapita nthawi, ana a Amoni+ anasonkhanitsidwa pamodzi ndipo anamanga msasa wawo ku Giliyadi.+ Zitatero, ana a Isiraeli anasonkhana pamodzi ndi kumanga msasa wawo ku Mizipa.+
18 Ndiyeno anthu ndi akalonga a Giliyadi anayamba kufunsana kuti: “Ndani atitsogolere kukamenyana ndi ana a Amoni?+ Ameneyo akhale mtsogoleri wa anthu onse okhala m’Giliyadi.”+
Mawu a M'munsi
^ Dzinali limatanthauza, “Midzi ya Mahema ya Yairi.”