Oweruza 14:1-20

14  Tsopano Samisoni anapita ku Timuna+ ndipo kumeneko anaona mkazi mwa ana aakazi a Afilisiti.  Kenako anapita kukauza bambo ndi mayi ake kuti: “Ine ndaona mkazi ku Timuna mwa ana aakazi a Afilisiti, choncho mukam’tenge kuti akhale mkazi wanga.”+  Koma bambo ndi mayi akewo anam’funsa kuti: “Kodi wasowa mkazi pakati pa ana aakazi a abale ako ndi anthu onse a mtundu wathu,+ kuti upite kukatenga mkazi kwa Afilisiti osadulidwa?”+ Koma Samisoni anauza atate akewo kuti: “Ingonditengerani mkazi ameneyu, chifukwa ndi amene ali woyenera kwa ine?”  Bambo ndi mayi a Samisoni sanadziwe kuti Yehova ndi amene anali kuchititsa zimenezi.+ Iwo sanadziwe kuti anali kufunafuna mpata woti amenyane ndi Afilisiti, chifukwa pa nthawiyi Afilisiti anali kulamulira Isiraeli.+  Pamenepo Samisoni anapita ku Timuna+ pamodzi ndi bambo ndi mayi ake. Atafika m’minda ya mpesa ya ku Timuna, anakumana ndi mkango wamphamvu umene unayamba kubangula utamuona.  Ndiyeno mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa iye,+ moti anakhadzula mkangowo pakati ngati mmene munthu angakhadzulire kamwana ka mbuzi. Iye analibe chida chilichonse m’manja mwake. Zimene anachitazi sanauze bambo kapena mayi ake.  Iye anapita kwawo kwa mkazi uja ndipo analankhula naye. Kwa Samisoni, mkaziyu anali woyenerabe.+  Patapita nthawi, Samisoni anabwerera kwa mkaziyo kuti akam’tenge ndi kupita naye kwawo.+ Ali m’njira, anapatuka kuti aone mkango umene anapha uja. Atafika pamene anaphera mkango paja anapeza kuti m’thupi la mkango wakufa uja muli njuchi ndi uchi.+  Ndiyeno anatengako uchiwo m’manja n’kumadya akuyenda.+ Atapezananso ndi bambo ndi mayi ake, anawagawira uchiwo ndipo iwo anayamba kudya. Iye sanawauze kuti uchiwo wautenga m’thupi la mkango wakufa. 10  Bambo ake anapitiriza ulendo wopita kwawo kwa mkazi uja, ndipo Samisoni anakonza phwando kumeneko,+ popeza umu ndi mmene achinyamata anali kuchitira. 11  Ndiyeno anthu a kumeneko atamuona, nthawi yomweyo anatenga amuna 30 kuti azikhala ndi Samisoni monga anzake a mkwati. 12  Kenako Samisoni anawauza kuti: “Ndiloleni ndikuphereni mwambi.+ Ngati mundiuza tanthauzo lake, m’masiku 7+ a phwandoli, ndidzakupatsani malaya 30 amkati ndi zovala zina 30.+ 13  Koma mukalephera kundiuza tanthauzo lake, inuyo mudzandipatsa malaya 30 amkati ndi zovala zina 30.” Atatero iwo anamuuza kuti: “Ipha mwambi wakowo kuti tiumve.” 14  Choncho iye anati:“M’chinthu chodya zinzake+ munatuluka chakudya,Ndipo m’chinthu champhamvu munatuluka zinthu zokoma.”+ Koma anzake a mkwatiwo analephera kumasulira mwambiwo kwa masiku atatu. 15  Ndiyeno pa tsiku lachinayi anayamba kuuza mkazi wa Samisoni kuti: “Umunyengerere mwamuna wako kuti atiuze tanthauzo la mwambiwu.+ Akapanda kutiuza, tikutentha ndi moto pamodzi ndi nyumba ya bambo ako.+ Kodi anthu inu mwatiitana kuti mutilande katundu wathu?”+ 16  Pamenepo mkazi wa Samisoni anayamba kulira pamaso pa mwamuna wake,+ ndipo ankamuuza kuti: “Umandida, sundikonda ayi.+ Iwe waphera mwambi anthu a mtundu wanga,+ koma ine sunandiuze tanthauzo lake.” Atatero anamuuza kuti: “Ndikuuze chifukwa chiyani, pamene bambo kapena mayi anga sindinawauze?”+ 17  Koma mkaziyo anapitiriza kulira pamaso pa Samisoni kwa masiku 7 a phwandolo. Pamapeto pake, pa tsiku la 7, Samisoni anauza mkaziyo tanthauzo lake chifukwa anamuumiriza.+ Kenako mkaziyo anaulula tanthauzo la mwambiwo kwa anthu a mtundu wake.+ 18  Choncho pa tsiku la 7, Samisoni asanalowe m’chipinda cha mkaziyo,+ amuna a mumzindawo anamuuza kuti:“Kodi chokoma kuposa uchi n’chiyani,Ndipo champhamvu kuposa mkango n’chiyani?”+Poyankha iye anawauza kuti:“Mukanapanda kulima ndi ng’ombe yanga yaikazi,+Simukanatha kumasulira mwambi wanga.”+ 19  Pamenepo mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa iye.+ Choncho anapita ku Asikeloni+ kumene anakapha amuna 30, ndipo anatenga zovala zawo n’kuzipereka kwa amene anamasulira mwambi aja.+ Koma mkwiyo wake unapitiriza kuyaka, ndipo anapita kunyumba ya bambo ake. 20  Koma mkazi wa Samisoni+ anakwatiwa ndi mwamuna amene anali kukhala ndi Samisoni,+ monga mnzake wa mkwati.

Mawu a M'munsi