Oweruza 16:1-31

16  Nthawi ina, Samisoni anapita ku Gaza+ ndipo anaona hule kumeneko ndi kulowa m’nyumba ya huleyo.+  Pamenepo anthu a ku Gaza anauzidwa kuti: “Samisoni wabwera, ali kuno.” Choncho anam’zungulira+ ndi kum’bisalira usiku wonse kuchipata cha mzindawo.+ Iwo anakhala chete usiku wonse, n’kumanena mumtima mwawo kuti: “Kukangocha timuphe.”+  Koma Samisoni anagonabe mpaka pakati pa usiku. Kenako anadzuka pakati pa usikupo ndi kugwira zitseko za chipata cha mzinda+ pamodzi ndi nsanamira zake ziwiri, n’kuzizula pamodzi ndi mpiringidzo wake. Atatero anazinyamula pamapewa+ n’kupita nazo pamwamba pa phiri limene lili moyang’anana ndi Heburoni.+  Pambuyo pake, Samisoni anayamba kukonda mkazi wina kuchigwa* cha Soreki, ndipo dzina lake anali Delila.+  Pamenepo olamulira ogwirizana+ a Afilisiti anafika kwa mkaziyo ndi kumuuza kuti: “Umunyengerere+ kuti udziwe chinsinsi cha mphamvu zake zazikuluzo ndi zimene tingachite kuti timugonjetse. Ufufuzenso zimene tingam’mange nazo kuti tithane naye. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva zokwana 1,100.”+  Kenako Delila anauza Samisoni kuti: “Tandiuza, kodi chinsinsi cha mphamvu zako zazikuluzi n’chiyani? Ndipo kodi munthu angakumange ndi chiyani kuti athane nawe?”+  Samisoni anamuyankha kuti: “Atandimanga ndi zingwe zatsopano zaziwisi 7 za mitsempha ya nyama,+ ndingafooke ndi kukhala ngati munthu wamba.”  Choncho olamulira ogwirizana+ a Afilisiti anam’bweretsera zingwe zatsopano zaziwisi 7 za mitsempha ya nyama. Kenako Delila anamanga nazo Samisoni.  Pamenepa n’kuti anthu atabisalira Samisoni m’chipinda cha mkaziyo,+ ndipo mkaziyo anamuuza kuti: “Afilisiti+ aja abwera Samisoni!” Pamenepo Samisoni anadula zingwe zija pakati, monga mmene ulusi wopota wabwazi umadukira ukayandikira moto.+ Ndipo chinsinsi cha mphamvu zake sichinadziwike.+ 10  Kenako Delila+ anauza Samisoni kuti: “Iwe wandipusitsa pondiuza bodza.+ Tsopano ndiuze, chonde, zimene angakumange nazo.” 11  Poyankha Samisoni anamuuza kuti: “Atandimanga mwamphamvu ndi zingwe zatsopano zimene sanazigwiritsepo ntchito, ndingafooke ndi kukhala ngati munthu wamba.” 12  Ndiyeno Delila anatenga zingwe zatsopano ndi kum’manga nazo, n’kumuuza kuti: “Afilisiti aja abwera Samisoni!” Pa nthawiyi n’kuti anthu atam’bisalira m’chipinda cha mkaziyo.+ Pamenepo, Samisoni anadula pakati zingwe zimene anam’manga nazo manjazo, ngati kuti akudula ulusi.+ 13  Kenako Delila anauza Samisoni kuti: “Wakhala ukundipusitsa mpaka pano mwa kundiuza bodza.+ Ndiuze zimene angakumange nazo.”+ Poyankha Samisoni anati: “Uluke zingongo 7 za m’mutu mwanga ndi ulusi wa m’litali+ mwa nsalu.” 14  Iye analukadi mwamphamvu zingongozo, n’kuzilimbitsa ndi chikhomo. Kenako anamuuza kuti: “Afilisiti aja abwera Samisoni!”+ Pamenepo Samisoni anagalamuka ku tulo take ndi kuzula chikhomo chija n’kudula ulusiwo. 15  Ndiyeno Delila anauza Samisoni kuti: “Kodi ulibe manyazi kundiuza kuti, ‘Ndimakukonda,’+ pamene mtima wako suli pa ine? Katatu konse tsopano wakhala ukundipusitsa, ndipo sunandiuze chinsinsi cha mphamvu zako zazikuluzi.”+ 16  Ndiyeno chifukwa chakuti Delila anapanikiza+ Samisoni ndi mawu ake mosalekeza, ndi kum’chonderera, Samisoni anafika potopa nazo kwambiri.+ 17  Pamapeto pake, Samisoni anamuululira zonse za pansi pa mtima wake,+ kuti: “M’mutu mwanga simunadutsepo lezala,+ chifukwa ndine Mnaziri wa Mulungu kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga.+ Atandimeta, mphamvu zanga zikhoza kundichokera, ndipo ndingafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.”+ 18  Delila ataona kuti Samisoni wamuululira zonse za pansi pa mtima wake, nthawi yomweyo anatumiza mthenga kukaitana olamulira ogwirizana a Afilisiti,+ kuti: “Bwerani tsopano popeza wandiululira zonse za pansi pa mtima wake.”+ Pamenepo olamulira ogwirizana a Afilisiti aja anabwera kwa Delila ndipo anam’patsa ndalama.+ 19  Zitatero, Delila anagonetsa Samisoni tulo pamawondo ake, ndipo anaitana mwamuna wina amene anam’meta zingongo 7 za m’mutu mwake. Kenako Delila anayamba kukula mphamvu pa Samisoni ndipo mphamvu za Samisoni zinam’chokera. 20  Ndiyeno Delila anati: “Afilisiti aja abwera Samisoni!” Pamenepo Samisoni anagalamuka ku tulo take ndi kunena kuti: “Ndituluka monga mwa masiku onse+ kukalimbana nawo.” Koma iye sanadziwe kuti Yehova anali atam’chokera.+ 21  Chotero Afilisiti anam’gwira ndi kum’boola maso+ n’kupita naye ku Gaza.+ Anam’manga ndi zomangira ziwiri zamkuwa,+ ndipo anakhala woyendetsa mwala wa mphero+ m’ndende.+ 22  Atangometedwa, tsitsi lake linayamba kukula kwambiri.+ 23  Ndiyeno olamulira ogwirizana a Afilisiti anasonkhana pamodzi kuti achite phwando lalikulu lopereka nsembe kwa Dagoni+ mulungu wawo, ndi kuchita chikondwerero, ndipo anali kunena kuti: “Mulungu wathu wapereka m’manja mwathu mdani wathu Samisoni!”+ 24  Anthu ataona Samisoni, nthawi yomweyo anayamba kutamanda mulungu wawo,+ kuti: “Mulungu wathu wapereka m’manja mwathu mdani wathu,+ ndi munthu wowononga dziko lathu,+ ndiponso amene anali kuchulukitsa chiwerengero cha anthu athu ophedwa.”+ 25  Ndiyeno chifukwa chakuti mitima yawo inali yosangalala,+ anayamba kunena kuti: “Itanani Samisoni kuti adzatisangalatse.”+ Chotero anaitana Samisoni ndipo anam’tulutsa m’ndende kuti awachitire masewera.+ Atabwera anamuimiritsa pakati pa zipilala. 26  Pamenepo Samisoni anauza mnyamata amene anam’gwira dzanja kuti: “Ndilole ndigwire zipilala zimene zalimbitsa nyumbayi kuti ndizitsamire.” 27  (Pa nthawiyi m’nyumbamo munadzaza amuna ndi akazi, ndipo olamulira onse ogwirizana a Afilisiti anali mmenemo.+ Padenga la nyumbayo panali amuna ndi akazi pafupifupi 3,000 amene anali kuonerera Samisoni akuchita zoseketsa.)+ 28  Ndiyeno Samisoni+ anafuulira Yehova,+ kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, chonde, ndikumbukireni+ ndi kundipatsa mphamvu+ kamodzi kokhaka, inu Mulungu woona. Ndiloleni ndiwabwezere Afilisiti chifukwa cha limodzi mwa maso anga awiriwa.”+ 29  Pamenepo Samisoni anagwira mwamphamvu zipilala ziwiri zapakati zimene zinalimbitsa nyumbayo. Anagwira mwamphamvu chipilala chimodzi ndi dzanja lamanja ndipo chipilala china anachigwira ndi dzanja lamanzere. 30  Ndipo Samisoni anati: “Ndife nawo limodzi+ Afilisitiwa.” Pamenepo anawerama atasonkhanitsa mphamvu zake zonse moti nyumbayo inagwera olamulira ogwirizana a Afilisiti ndi anthu onse amene anali m’nyumbayo.+ Anthu amene Samisoni anawapha pa imfa yake anali ambiri kuposa anthu amene anawapha pa moyo wake.+ 31  Kenako abale ake ndi anthu onse a m’nyumba ya bambo ake, anapita kumeneko kukatenga mtembo wa Samisoni ndi kubwera nawo kwawo, ndipo anamuika m’manda a bambo ake Manowa,+ pakati pa Zora+ ndi Esitaoli.+ Samisoni anali ataweruza Isiraeli zaka 20.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.