Oweruza 17:1-13

17  Panali mwamuna wina wa kudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Mika.  Nthawi ina anauza mayi ake kuti: “Ndalama zanu zasiliva zokwana 1,100 zimene zinasowa zija, zimene munatemberera+ nazo munthu amene anazibayo, ine ndikumva, zili ndi ine. Ndine amene ndinatenga.”+ Pamenepo mayi akewo anati: “Yehova akudalitse mwana wanga.”+  Ndiyeno anabweza ndalama zasiliva zokwana 1,100 zija kwa mayi ake.+ Atabweza ndalamazo, mayi akewo anati: “Ndithudi ndipereka ndalama zasilivazi kwa Yehova kuti zikhale zopatulika. Ndichita zimenezi kuti ndithandize mwana wanga, ndi kuti papangidwe chifaniziro chosema+ ndiponso chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Tsopano ndikubweza ndalamazi kwa iwe.”  Koma Mika anabweza ndalamazo kwa mayi ake, ndipo mayi akewo anatenga ndalama zasiliva zokwana 200 n’kuzipereka kwa wosula siliva.+ Pamenepo wosula silivayo anapanga chifaniziro chosema+ ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Zinthu zimenezi anaziika m’nyumba ya Mika.  Ndiyeno Mika anali ndi nyumba ya milungu,+ chotero anapanga efodi+ ndi aterafi,*+ komanso anapatsa mmodzi mwa ana ake mphamvu,*+ kuti azitumikira monga wansembe wake.+  Masiku amenewo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Aliyense anali kuchita zimene anali kuona kuti n’zoyenera.+  Ndiyeno mu Betelehemu+ wa ku Yuda munali mnyamata wina, wa m’banja la Yuda, ndipo anali Mlevi.+ Iye anakhala kumeneko kwa kanthawi.  Mnyamata ameneyu anachoka kumzinda wa Betelehemu wa ku Yuda, kuti akakhale kwa kanthawi kulikonse kumene angapeze malo okhala. Atayenda mtunda wautali ndithu, anafika m’dera lamapiri la Efuraimu, mpaka kunyumba ya Mika.+  Pamenepo Mika anam’funsa kuti: “Wachokera kuti?” Poyankha, iye anati: “Ine ndine Mlevi. Ndachokera ku Betelehemu wa ku Yuda, ndipo ndikupita kulikonse kumene ndingapeze malo okhala, kuti ndikakhale kumeneko kwa kanthawi.” 10  Atatero Mika anamuuza kuti: “Ukhale ndi ine ndipo uzitumikira ngati tate+ ndi wansembe+ wanga. Ine ndizikupatsa ndalama zasiliva 10 pa chaka, komanso zovala zako zoyenera ndi chakudya.” Pamenepo Mleviyo analowa m’nyumbamo. 11  Choncho Mleviyo anavomera kukhala ndi Mika ndipo anakhala ngati mmodzi wa ana a Mika. 12  Kuwonjezera apo, Mika anapatsa mphamvu Mleviyo+ kuti atumikire monga wansembe+ wake ndi kupitiriza kukhala m’nyumba ya Mika. 13  Choncho Mika anati: “Tsopano ndadziwa kuti Yehova andichitira zabwino, chifukwa Mlevi wakhala wansembe wanga.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Gen 31:19.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:41.