Oweruza 19:1-30

19  Tsopano masiku amenewo, mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Ndiyeno Mlevi wina anakhala kwa kanthawi m’dera lamapiri lakutali kwambiri la Efuraimu.+ Patapita nthawi, anatenga mkazi wa ku Betelehemu,+ ku Yuda, kukhala mdzakazi wake.+  Mdzakazi wakeyo anakhala wosakhulupirika kwa iye, moti anayamba kuchita dama.+ Pamapeto pake, mkaziyo anachoka n’kukakhala kwa bambo ake ku Betelehemu wa ku Yuda miyezi inayi yathunthu.  Zitatero, mwamuna wakeyo ananyamuka kukakambirana naye mofatsa kuti abwerere. Pa ulendowo anali limodzi ndi mtumiki wake+ ndi abulu awiri. Atafika kumeneko, mkaziyo analowetsa mwamuna wakeyo m’nyumba ya bambo ake ndipo iwo atamuona anasangalala kwambiri kukumana naye.  Ndiyeno apongozi akewo, bambo a mtsikanayo, anam’chonderera kuti akhalebe, moti anakhala ndi kugona kumeneko masiku atatu. Masiku onsewa, iwo anali kudya ndi kumwa.+  Pa tsiku lachinayi, atadzuka m’mawa kwambiri monga mwa nthawi zonse, anakonzeka kuti anyamuke, koma bambo a mtsikanayo anauza mkamwini wawoyo kuti: “Yambani mwadya kaye mkate,+ kenako mukhoza kupita.”  Choncho anakhala pansi ndipo onse awiri anayamba kudya ndi kumwera pamodzi. Kenako bambo a mtsikanayo anauza mwamunayo kuti: “Chonde, lero mugone, mupite mawa,+ ndipo musangalatse mtima wanu.”+  Mwamunayo ataimirira kuti azipita, apongozi ake anapitirizabe kum’chonderera, moti anagonanso komweko.+  Atadzuka m’mawa kwambiri tsiku lachisanu kuti azipita, bambo a mtsikanayo anati: “Idyaniko chakudya kuti musangalatse mtima wanu.”+ Pamenepo iwo anakhalabe mpaka chakumadzulo, ndipo onse awiri anali kudya.  Tsopano mwamunayo+ anaimirira kuti azipita, iyeyo pamodzi ndi mdzakazi wake+ ndiponso mtumiki wake,+ koma apongozi ake, bambo a mtsikanayo, anamuuza kuti: “Anotu ndi madzulo tsopano, ndipo posachedwa kuchita mdima. Chonde, lero mugone kuno.+ Onani, kunja kwatsala pang’ono kuda. Lero mugone kuno ndipo musangalatse mtima wanu.+ Mawa mudzuke m’mawa kwambiri ndi kuyamba ulendo wanu wopita kuhema wanu.” 10  Koma mwamunayo sanavomere kuti agone, ndipo ananyamuka ndi kuyamba ulendo wake. Iye anayenda mpaka kukafika pafupi ndi Yebusi,+ amene ndi Yerusalemu.+ Pa ulendowu, anali ndi abulu awiri amphongo aja, okhala ndi zishalo, ndipo analinso ndi mdzakazi wake ndi mtumiki wake. 11  Pamene ankayandikira Yebusi, dzuwa linali litapendeka ndithu,+ ndipo mtumiki uja anauza mbuye wake kuti: “Tiyeni tipatukire mumzinda uwu wa Ayebusi+ kuti tigone mmenemu.” 12  Poyankha mbuye wakeyo anati: “Tisapatukire mumzinda wa anthu achilendo+ amene si ana a Isiraeli. Tiyeni tipitirire ndi kukafika ku Gibeya.”+ 13  Anauzanso mtumiki wakeyo kuti: “Tiyeni tifike pa amodzi mwa malo awa, Gibeya kapena Rama,+ ndipo tigone kumeneko.” 14  Choncho anadutsa ndi kupitirizabe ulendo wawo ndipo dzuwa linayamba kulowa atayandikira Gibeya, m’dera la Benjamini. 15  Atafika kumzinda wa Gibeya, anapatuka kuti akalowe ndi kugona mmenemo. Ndiyeno analowa ndi kukhala pabwalo la mzindawo. Koma panalibe wowatenga kuti akagone m’nyumba yake.+ 16  Patapita nthawi, mwamuna wina wokalamba anatulukira madzulowo+ akuchokera ku ntchito yake ya kumunda. Kwawo kwa mwamunayo kunali kudera lamapiri la Efuraimu,+ ndipo anali kukhala ku Gibeya kwa kanthawi, koma amuna a mumzindawo anali Abenjamini.+ 17  Atakweza maso, anaona mwamuna wapaulendoyo ali m’bwalo la mzinda. Pamenepo mwamuna wokalambayo anam’funsa kuti: “Ukupita kuti, ndipo ukuchokera kuti?”+ 18  Poyankha anamuuza kuti: “Tikudutsa kuchokera ku Betelehemu wa ku Yuda kupita kudera lamapiri lakutali kwambiri la Efuraimu.+ Kumeneko ndiye kwathu, koma ndinapita ku Betelehemu wa ku Yuda.+ Panopa ndikupita kunyumba kwanga, koma palibe amene akunditenga kuti ndikagone m’nyumba yake.+ 19  Udzu ndi chakudya+ china cha abulu athu tili nazo, ndipo tilinso ndi mkate+ ndi vinyo wa ine ndi kapolo wanu wamkazi+ komanso wa mtumiki+ wa kapolo wanu. Sitikusowa kanthu.” 20  Koma mwamuna wokalamba uja anati: “Mtendere ukhale nawe!+ Ine ndidzakupatsa chilichonse chimene ungafunikire.+ Koma usagone pabwalo la mzinda.” 21  Atatero anatengera Mlevi uja kunyumba kwake+ ndipo anapatsa abulu ake aja chakudya.+ Ndiyeno anasamba mapazi awo+ n’kuyamba kudya ndi kumwa. 22  Pamene anali kusangalatsa mitima yawo,+ mwadzidzidzi amuna a mumzindawo, anthu opanda pake,+ anazungulira nyumbayo,+ ndipo anali kukankhanakankhana pachitseko. Iwo anali kuuza mwamuna wokalamba uja, mwini nyumbayo, kuti: “Tulutsa mwamuna amene wabwera m’nyumba yako kuti tigone naye.”+ 23  Pamenepo mwini nyumbayo anatuluka ndi kuwauza kuti:+ “Iyayi abale anga,+ chonde, musachite choipa chilichonse, chifukwa munthuyu wabwera m’nyumba yanga. Musachite chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi ngati chimenechi.+ 24  Ndili ndi mwana wamkazi amene ndi namwali ndiponso pali mdzakazi wa mwamunayu. Ndiloleni ndiwatulutse, muwagwirire+ amenewa ndi kuchita nawo chilichonse chimene mungafune. Koma mwamunayu musam’chite chinthu chochititsa manyazi ndi chopusa ngati chimenechi.” 25  Koma amunawo sanafune kumumvera, moti Mleviyo anatenga mdzakazi wake+ ndi kum’pereka kwa amunawo kunja. Pamenepo, anthuwo anayamba kumugona,+ ndipo anapitiriza kum’zunza+ usiku wonse mpaka m’mawa. M’bandakucha anamusiya kuti apite. 26  Kutayamba kucha, mkaziyo anafika ndi kugwera pakhomo la nyumba ya mwamuna uja, mmene munali mbuye wake,+ ndipo anakhala pomwepo kufikira kutayera. 27  Mbuye wake anadzuka m’mawa ndi kutsegula zitseko za nyumbayo, n’kutuluka kuti ayambe ulendo wake. Mwadzidzidzi, anangopeza mkazi uja, mdzakazi wake,+ ali thapsa patsogolo pa nyumba, manja ake ali pakhomo la nyumbayo! 28  Ndiyeno anauza mkaziyo kuti: “Dzuka tizipita.” Koma sanamuyankhe.+ Zitatero, anamukweza pabulu n’kupita kunyumba kwake.+ 29  Atafika kwawo, analowa m’nyumba yake ndi kutenga mpeni wophera nyama, n’kuduladula mdzakazi wake uja zigawo 12,+ n’kuzitumiza m’dera lililonse la Isiraeli.+ 30  Zitatero, aliyense amene anaona zimenezo anati: “Zoterezi sizinachitikepo kapena kuonekapo kuchokera pa tsiku limene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo mpaka lero. Iganizireni mofatsa nkhaniyi, munenepo maganizo+ anu ndipo tigwirizane.”

Mawu a M'munsi