Oweruza 6:1-40

6  Kenako ana a Isiraeli anayamba kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Motero Yehova anawapereka m’manja mwa Amidiyani+ kwa zaka 7.  Amidiyaniwo anayamba kusautsa Aisiraeli.+ Chifukwa cha kusautsidwa ndi Amidiyani kumeneku, ana a Isiraeli anadzikonzera malo apansi osungiramo zinthu m’mapiri. Anadzikonzeranso mapanga ndi malo ena ovuta kufikako kuti azithawirako.+  Ndiyeno Aisiraeli akalima minda yawo,+ Amidiyani, Aamaleki+ ndi anthu a Kum’mawa+ anali kubwera kudzawaukira.  Anali kuwazungulira ndi kuwawonongera zokolola zawo zonse mpaka kukafika ku Gaza. Sanali kuwasiyira chakudya chilichonse ngakhalenso nkhosa, ng’ombe kapena bulu mu Isiraeli.+  Iwo anali kubwera ndi ziweto zawo ndi mahema awo. Anali kubwera ochuluka kwambiri ngati dzombe,+ ndipo iwo ndi ngamila zawo anali osawerengeka.+ Iwo anali kubwera m’dzikomo n’kumaliwononga.+  Choncho Aisiraeli anasautsika kwadzaoneni chifukwa cha Amidiyani. Pamenepo, ana a Isiraeli anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+  Ana a Isiraeli atafuulira Yehova kuti awathandize chifukwa cha Amidiyani,+  Yehova anatumiza munthu wina, mneneri,+ kwa ana a Isiraeli, ndipo anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndine amene ndinakutulutsani mu Iguputo,+ m’nyumba yaukapolo.+  Choncho ndinakulanditsani m’manja mwa Iguputo ndiponso m’manja mwa onse amene anali kukuponderezani, ndipo ndinapitikitsa adani anu pamaso panu ndi kukupatsani dziko lawo.+ 10  Komanso ndinakuuzani kuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ Musaope milungu ya Aamori+ amene mukukhala m’dziko lawo.”+ Koma inu simunamvere mawu anga.’”+ 11  Kenako, kunabwera mngelo wa Yehova+ ndi kukhala pansi pa mtengo waukulu umene unali ku Ofira. Mtengo umenewu unali wa Yowasi, Mwabi-ezeri.+ Pa nthawiyi, Gidiyoni+ mwana wa Yowasi, anali kupuntha tirigu moponderamo mphesa kuti akamubise mwamsanga Amidiyani asanaone. 12  Pamenepo mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye, ndipo anati: “Yehova ali ndi iwe,+ munthu wolimba mtima ndi wamphamvuwe.” 13  Ndiyeno Gidiyoni anayankha kuti: “Pepani mbuyanga, koma ngati Yehova ali ndi ife, n’chifukwa chiyani zonsezi zatigwera?+ Nanga ntchito zake zodabwitsa zija,+ zimene makolo athu anatisimbira zili kuti?+ Iwo anatiuza kuti, ‘Yehova ndiye anatitulutsa mu Iguputo.’+ Koma tsopano Yehova watisiya,+ ndipo watipereka m’manja mwa Amidiyani.” 14  Atatero, Yehova anamuyang’ana ndi kunena kuti: “Pita ndi mphamvu zimene ndakupatsazi,+ ndipo udzapulumutsadi Isiraeli m’manja mwa Amidiyani.+ Si ine amene ndakutuma kodi?”+ 15  Koma iye anayankha kuti: “Pepani Yehova. Kodi Isiraeli ndidzam’pulumutsa ndi chiyani?+ Pajatu banja lathu* ndilo laling’ono zedi m’fuko lonse la Manase, ndipo m’nyumba ya bambo anga, wamng’ono kwambiri ndine.”+ 16  Koma Yehova anamuuza kuti: “Popeza ndidzakhala ndi iwe,+ udzaphadi Amidiyani+ ngati kuti ukupha munthu mmodzi.” 17  Pamenepo iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima,+ mundisonyeze chizindikiro kuti nditsimikize kuti ndinudi amene mukulankhula nane.+ 18  Chonde musachoke, kufikira nditabwera+ ndi kukupatsani mphatso yanga.”+ Choncho iye anati: “Ineyo ndikhalabe pompano kufikira utabweranso.” 19  Ndiyeno Gidiyoni analowa m’nyumba ndi kuphika nyama ya mwana wa mbuzi.+ Anatenganso ufa wokwana muyezo umodzi wa efa* ndi kupanga mikate yopanda chofufumitsa.+ Atatero, anatenga nyamayo ndi kuiika m’dengu, ndipo msuzi anauika mumphika. Kenako, anatenga zinthu zimenezi ndi kukamupatsa mngelo uja pansi pa mtengo waukulu uja. 20  Pamenepo mngelo wa Mulungu woona anamuuza kuti: “Tenga nyamayi ndi mikate yopanda chofufumitsayo, ndi kuziika pamwala waukuluwo,+ ndipo ukhuthule msuziwo.” Gidiyoni anachitadi zomwezo. 21  Atatero, mngelo wa Yehova anatambasula dzanja lake, ndipo anakhudza nyama ndi mikate yopanda chofufumitsayo ndi nsonga ya ndodo imene inali m’dzanja lake. Pamenepo, moto wotuluka m’mwalawo unayamba kulilima, n’kunyeketsa nyama ndi mkate wopanda chofufumitsawo,+ koma mngelo wa Yehova anazimiririka. 22  Tsopano Gidiyoni anazindikira kuti anali mngelo wa Yehova.+ Nthawi yomweyo Gidiyoni anati: “Kalanga ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Ndaonana ndi mngelo wa Yehova maso ndi maso.”+ 23  Koma Yehova anamuuza kuti: “Mtendere ukhale nawe.+ Usachite mantha.+ Suufa.”+ 24  Choncho, Gidiyoni anamangira Yehova guwa lansembe+ pamenepo, ndipo limatchedwa+ Yehova-salomu* kufikira lero. Guwalo lili ku Ofira,+ mzinda wa Aabi-ezeri, mpaka pano. 25  Ndiyeno zinachitika kuti usiku womwewo, Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Tenga ng’ombe yaing’ono yamphongo ya bambo ako, ng’ombe yachiwiri yazaka 7 ija. Kenako ugwetse guwa lansembe la Baala+ la bambo ako ndipo udule mzati wopatulika umene uli pafupi ndi guwalo.+ 26  Ndipo umangire Yehova Mulungu wako guwa lansembe mwa kuyala miyala. Ulimange pamwamba pa linga la malo otetezekawa. Ukatero, utenge ng’ombe yaing’ono yamphongo yachiwiri ija, ndi kuipereka monga nsembe yotentha ndi moto pankhuni za mzati wopatulika umene udulewo.” 27  Choncho Gidiyoni anatenga amuna 10 mwa atumiki ake ndi kuchita zonse zimene Yehova anamuuza.+ Koma chifukwa choopa kwambiri anthu a m’nyumba ya bambo ake ndi anthu a mumzindawo, anachita zimenezi usiku osati masana.+ 28  Amuna a mumzindawo atadzuka m’mawa kwambiri monga mwa nthawi zonse, anangoona kuti guwa lansembe la Baala lagwetsedwa, ndipo mzati wopatulika+ umene unali pambali pake wadulidwa. Iwo anaonanso kuti paguwa lansembe latsopano limene lamangidwa, panali pataperekedwa ng’ombe yaing’ono yamphongo yachiwiri ija. 29  Ndiyeno anayamba kufunsana kuti: “Ndani wachita zimenezi?” Choncho anayamba kufufuza ndi kufunafuna amene anachita zimenezo. Pamapeto pake iwo anati: “Ndi Gidiyoni, mwana wa Yowasi amene wachita zimenezi.” 30  Pamenepo amuna a mumzindawo anauza Yowasi kuti: “Tulutsa mwana wako kuti timuphe,+ chifukwa wagwetsa guwa lansembe la Baala ndi kudula mzati wopatulika umene unali pambali pake.” 31  Koma Yowasi+ anauza onse amene anamuukirawo kuti:+ “Kodi inu mungaweruzire Baala mlandu kuti mum’pulumutse? Aliyense womuweruzira mlandu ayenera kuphedwa m’mawa womwe uno.+ Ngati Baalayo ndi Mulungu,+ adziweruzire yekha mlanduwu,+ chifukwa wina wake wagwetsa guwa lake lansembe.” 32  Choncho Yowasi anatcha Gidiyoni dzina lakuti Yerubaala*+ pa tsiku limenelo, ndipo anati: “Baala adziweruzire yekha mlandu, chifukwa winawake wagwetsa guwa lake lansembe.”+ 33  Ndiyeno Amidiyani+ ndi Aamaleki onse,+ pamodzi ndi anthu onse a Kum’mawa+ anasonkhana pamodzi+ ndi kuwoloka mtsinje, ndipo anamanga msasa wawo m’chigwa cha Yezereeli.+ 34  Zitatero, Gidiyoni anagwidwa ndi mzimu wa Yehova,+ moti anayamba kuliza lipenga+ la nyanga ya nkhosa ndipo Aabi-ezeri+ anasonkhana pamodzi n’kuyamba kumutsatira. 35  Iye anatumiza mithenga+ m’dera lonse la fuko la Manase, ndipo anthu a m’fuko limeneli nawonso anasonkhana pamodzi n’kuyamba kumutsatira. Anatumizanso mithenga m’madera onse a mafuko a Aseri, Zebuloni ndi Nafitali, ndipo nawonso anabwera kudzakumana naye. 36  Tsopano Gidiyoni anauza Mulungu woona kuti: “Kuti ndidziwe kuti mudzapulumutsa Isiraeli kudzera mwa ine, monga mmene mwalonjezera,+ 37  ndiika ubweya wa nkhosa pansi, pamalo opunthira mbewu. Ngati mame angagwe paubweya wokhawu, koma nthaka yonse n’kukhala youma, pamenepo ndidzadziwa kuti mudzapulumutsadi Isiraeli kudzera mwa ine, monga mmene mwalonjezera.” 38  Ndipo zinachitikadi momwemo. Atadzuka m’mawa kwambiri tsiku lotsatira n’kufinya ubweya wa nkhosawo, ubweyawo unatulutsa madzi ochuluka oti n’kudzaza chikho chachikulu cha pa phwando. 39  Komabe, Gidiyoni anauza Mulungu woona kuti: “Mkwiyo wanu usandiyakire chonde, ndiloleni ndilankhulenso kamodzi kokhaka. Ndiloleni chonde, ndikuyeseninso kamodzi kokha ndi ubweyawu, kuti nditsimikizire za nkhaniyi. Nthaka yonse ikhathamire ndi mame, koma ubweya wokhawu ukhale wouma.” 40  Choncho, Mulungu anachitadi zimenezo usiku umenewo. Nthaka yonse inakhathamira ndi mame, koma ubweya wokhawo unali wouma.

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “banja lathu” mawu ake enieni ndi “sauzande yanga.”
“Muyezo umodzi wa efa” ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.
Dzinali limatanthauza kuti, “Yehova ndi Mtendere.”
Dzinali limatanthauza kuti, “Baala Adziweruzire Yekha Mlandu wa Munthuyu.”