Oweruza 4:1-24

4  Ehudi atamwalira, ana a Isiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+  Choncho Yehova anawagulitsa+ kwa Yabini mfumu yachikanani, imene inali kulamulira ku Hazori.+ Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Sisera,+ yemwe anali kukhala ku Haroseti-ha-goimu.+  Ana a Isiraeli anayamba kulirira Yehova,+ chifukwa Yabini anawapondereza+ kwambiri zaka 20, ndipo iye anali ndi magaleta ankhondo 900 okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa m’mawilo.+  Pa nthawi imeneyo Debora mneneri wamkazi,+ mkazi wa Lapidoti, anali kuweruza Isiraeli.  Iye anali kukhala patsinde pa mtengo wa kanjedza wa Debora, pakati pa mzinda wa Rama+ ndi wa Beteli,+ m’dera lamapiri la Efuraimu. Ana a Isiraeli anali kupita kwa iye kukalandira zigamulo zochokera kwa Mulungu.  Ndiyeno iye anatumiza uthenga kwa Baraki+ mwana wa Abinowamu, yemwe anali ku Kedesi-nafitali,+ womuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli walamula kuti, ‘Tenga amuna 10,000 pakati pa ana a Nafitali+ ndi ana a Zebuloni+ ndipo mukasonkhane paphiri la Tabori.+  Ine ndidzakokera kwa iwe+ m’chigwa* cha Kisoni,+ Sisera+ mkulu wa gulu lankhondo la Yabini,+ pamodzi ndi magaleta ake ankhondo ndi gulu lake lonse. Pamenepo ndidzam’pereka m’manja mwako.’”+  Ndiyeno Baraki anauza Debora kuti: “Ngati ungatsagane nane, ndipitadi, koma ngati sutsagana nane, sindipita.”  Pamenepo Debora anati: “Sindilephera, tipitira limodzi. Ngakhale zili choncho, ulemerero sukhala wako kumene ukupitako, chifukwa Yehova adzapereka Sisera m’manja mwa munthu wamkazi.”+ Atatero, Debora ananyamuka n’kutsagana ndi Baraki ku Kedesi.+ 10  Ndipo Baraki anasonkhanitsa pamodzi fuko la Zebuloni+ ndi fuko la Nafitali ku Kedesi, moti amuna 10,000 anam’tsatira,+ ndipo Debora nayenso anapita nawo. 11  Zili choncho, Hiberi+ Mkeni anapatukana ndi Akeni,+ ana a Hobabu mpongozi wa Mose,+ ndipo anamanga hema wake pafupi ndi mtengo waukulu ku Zaananimu, ku Kedesi. 12  Ndiyeno kunafika uthenga kwa Sisera, wonena kuti Baraki, mwana wa Abinowamu,+ wapita kuphiri la Tabori.+ 13  Nthawi yomweyo, Sisera anasonkhanitsa magaleta ake onse ankhondo, magaleta 900 okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa m’mawilo.+ Anasonkhanitsanso anthu ake onse kuchokera ku Haroseti-ha-goimu, kupita kuchigwa cha Kisoni.+ 14  Kenako Debora anauza Baraki kuti: “Nyamuka, pakuti lero ndi tsiku limene Yehova adzapereka Sisera m’manja mwako. Yehova akuyendatu patsogolo pako.”+ Ndipo Baraki anatsikadi m’phiri la Tabori, amuna 10,000 akum’tsatira. 15  Pamenepo Yehova anayamba kusokoneza+ ndi kuwononga Sisera ndi magaleta ake onse ankhondo, pamodzi ndi anthu ake onse. Anawasokoneza ndi kuwawononga ndi lupanga pamaso pa Baraki. Zitatero Sisera anatsika m’galeta wake n’kuyamba kuthawa wapansi. 16  Baraki anathamangitsa+ magaleta ankhondowo+ ndi gulu lonselo mpaka ku Haroseti-ha-goimu, moti gulu lonse la Sisera linaphedwa ndi lupanga. Sipanatsale ndi mmodzi yemwe.+ 17  Koma Sisera+ anathawa wapansi kupita kuhema wa Yaeli,+ mkazi wa Hiberi Mkeni,+ pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori+ ndi nyumba ya Hiberi Mkeni. 18  Pamenepo Yaeli anatuluka kukachingamira Sisera ndi kumuuza kuti: “Bwerani kuno, mbuyanga, bwerani kuno kwathu. Musaope ayi.” Choncho anapatuka kukalowa m’hema wa Yaeli. Pambuyo pake, anam’funditsa bulangete. 19  Kenako Sisera anamuuza kuti: “Ndipatseko madzi akumwa, chifukwa ndili ndi ludzu.” Pamenepo anatsegula thumba lachikopa+ la mkaka ndi kum’patsa kuti amwe.+ Atatero, anam’funditsanso. 20  Ndipo Sisera anauza Yaeli kuti: “Uime pakhomo la hema, ndipo pakabwera munthu n’kukufunsa kuti, ‘Kodi pali mwamuna pano?’ umuuze kuti, ‘Palibe.’” 21  Ndiyeno Yaeli mkazi wa Hiberi anatenga chikhomo cha hema ndi nyundo. Kenako analowa m’hemamo, akuyenda monyang’ama n’kukhoma chikhomocho m’mutu mwa Sisera pafupi ndi khutu,+ mpaka chikhomocho chinalowa pansi. Apa n’kuti Sisera ali m’tulo tofa nato ndiponso ali wotopa kwambiri. Mmenemu ndi mmene Sisera anafera.+ 22  Pa nthawiyi, Baraki anatulukira akusakasaka Sisera. Pamenepo Yaeli anapita kukamuchingamira, ndipo anamuuza kuti: “Tabwerani ndikuonetseni munthu amene mukum’funafunayo.” Iye anam’tsatira, ndipo anangoona Sisera ali thasa pansi wakufa, chikhomo chili m’mutu mwake pafupi ndi khutu. 23  Umu ndi mmene Mulungu anagonjetsera+ Yabini mfumu ya Kanani, pamaso pa ana a Isiraeli pa tsiku limenelo. 24  Ndipo dzanja la ana a Isiraeli linakulirakulirabe mphamvu popanikiza Yabini mfumu ya Kanani,+ mpaka anapha Yabini mfumu+ ya Kanani.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.