Oweruza 15:1-20

15  Ndiyeno patapita nthawi, m’masiku okolola tirigu, Samisoni anapita kukaona mkazi wake uja, atatenga kamwana ka mbuzi.+ Pamenepo iye anati: “Ndilowa m’chipinda cha mkazi wanga.”+ Koma bambo a mkaziyo sanam’lole kuti alowe.  Iwo anati: “Ine ndinali kuganiza kuti, ndithu ukudana naye mkaziyu,+ moti ndam’pereka kwa mwamuna amene anali kukhala nawe ngati mnzake wa mkwati.+ Kodi mng’ono wake wa mtsikanayu si wabwino kuposa iye? Bwanji osatenga ameneyu kukhala mkazi wako m’malo mwa iye?”  Koma Samisoni anawauza kuti: “Ulendo uno ndilibe mlandu ndi Afilisiti ngati ndingachite zinthu zowavulaza.”+  Pamenepo Samisoni ananyamuka ndi kugwira nkhandwe 300,+ ndipo anatenga nkhandwezo ziwiriziwiri n’kuzimanga michira. Atatero, anaika muuni umodzi pakati penipeni pa michira iwiriyo.  Kenako anayatsa miyuniyo ndi moto, n’kutumiza nkhandwezo m’minda ya Afilisti ya mbewu zosakolola. Choncho anayatsa chilichonse, kuyambira mitolo ya mbewu, mbewu zosakolola, minda ya mpesa mpaka minda ya maolivi.+  Zitatero, Afilisiti anayamba kufunsa kuti: “Wachita zimenezi ndani?” Ndiyeno iwo anati: “Ndi Samisoni, mkamwini wa munthu wa ku Timuna uja, chifukwa chakuti anatenga mkazi wake ndi kum’pereka kwa mwamuna amene anali mnzake wa mkwati.”+ Choncho Afilisiti anapita kukatentha ndi moto mtsikanayo pamodzi ndi bambo ake.+  Pamenepo Samisoni anawauza kuti: “Pa zimene mwachitazi, ine sindingachitire mwina koma kukubwezerani,+ ndipo ndikatero ndisiyira pamenepo.”  Ndiyeno anayamba kuwakantha koopsa.* Kenako anayamba kukhala m’phanga la m’thanthwe la Etami.+  Patapita nthawi, Afilisiti+ anabwera ndi kumanga msasa ku Yuda,+ n’kuyamba kuyendayenda ku Lehi.+ 10  Pamenepo anthu a ku Yuda anati: “N’chifukwa chiyani mwabwera kudzatiukira?” Poyankha, iwo anati: “Tabwera kudzamanga Samisoni, kuti tim’chitire zimene iye watichitira.” 11  Zitatero, amuna 3,000 a ku Yuda anapita kuphanga la thanthwe la Etami+ ndi kuuza Samisoni kuti: “Kodi iwe, sukudziwa kuti Afilisiti ndi amene akutilamulira?+ Ndiye wachitiranji zimenezi kwa ife?” Iye anawayankha kuti: “Ndawachitira zimene iwo anandichitira.”+ 12  Koma iwo anamuuza kuti: “Ife tabwera kudzakumanga kuti tikupereke m’manja mwa Afilisiti.” Poyankha Samisoni anati: “Lumbirani kuti inuyo simundiukira.” 13  Iwo anamuyankha kuti: “Ayi, ife sitikupha. Tingokumanga ndi kukupereka m’manja mwawo.” Pamenepo anam’manga ndi zingwe ziwiri zatsopano+ ndi kum’tulutsa kuphangako. 14  Choncho iye anafika ku Lehi, ndipo Afilisiti atamuona anafuula mokondwera.+ Pamenepo, mzimu wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo zingwe zimene anam’manga nazo manja zija zinaduka ngati ulusi wowauka ndi moto,+ moti zinadukaduka ndi kugwa. 15  Zitatero, anapeza fupa laliwisi la nsagwada za bulu wamphongo, n’kukantha nalo amuna 1,000.+ 16  Pamenepo Samisoni anati: “Ndi fupa la nsagwada za bulu wamphongo—milumilu! Ndi fupa la nsagwada za bulu wamphongo, ndapha anthu 1,000.”+ 17  Atamaliza kulankhula zimenezi, nthawi yomweyo anataya fupa lija ndi kutcha malowo kuti Ramati-lehi.*+ 18  Ndiyeno anamva ludzu koopsa, ndipo anayamba kufuulira Yehova kuti: “Ndinu amene mwapereka chipulumutso chachikulu chimenechi m’manja mwa mtumiki wanu.+ Tsopano kodi ndife ndi ludzu, ndigwere m’manja mwa anthu osadulidwa?”+ 19  Chotero Mulungu anang’amba nthaka ku Lehi ndipo madzi+ anayamba kutuluka panthakapo. Pamenepo Samisoni anamwa madziwo, moti anapezanso mphamvu+ ndi kutsitsimulidwa.+ N’chifukwa chake anatcha malowo kuti Eni-hakore.* Malo amenewa ali ku Lehi kufikira lero. 20  Chotero Samisoni anaweruza Isiraeli zaka 20 m’masiku a Afilisiti.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “kuwakantha, n’kuunjika miyendo ndi ntchafu pamodzi.”
Dzinali limatanthauza, “Malo Okwezeka a Fupa la Nsagwada.”
Dzinali limatanthauza, “Kasupe wa Munthu Wofuula.”