Oweruza 12:1-15

12  Ndiyeno amuna a ku Efuraimu anasonkhana pamodzi n’kuwolokera tsidya lina chakumpoto, ndi kuuza Yefita kuti: “N’chifukwa chiyani unawoloka kukamenya ndi ana a Amoni ife osatiitana kuti tipite nawe?+ Tikutentha ndi moto pamodzi ndi nyumba yako.”+  Koma Yefita anawauza kuti: “Ineyo ndi anthu anga tinalimbana koopsa ndi ana a Amoni.+ Inu ndinakuitanani kuti mudzandithandize koma simunandipulumutse m’manja mwawo.  Nditaona kuti inu simukubwera kudzandipulumutsa, ndinalolera kufa,* moti ndinapita kukamenyana ndi ana a Amoni,+ ndipo Yehova anawapereka m’manja mwanga.+ Tsopano n’chifukwa chiyani lero mwabwera kudzandiukira kuti mumenyane nane?”  Nthawi yomweyo Yefita anasonkhanitsa amuna onse a ku Giliyadi+ n’kumenyana ndi anthu a mu Efuraimu. Choncho amuna a ku Giliyadi anakantha Efuraimu, pakuti anati: “Ngakhale kuti inu anthu a mu Giliyadi mukukhala m’dera la Efuraimu ndi la Manase, kwenikweni ndinu gulu la anthu othawa ku Efuraimu.”  Ndiyeno amuna a ku Giliyadi anakatchinga powolokera Yorodano+ anthu a ku Efuraimu asanafike. Anthu othawa a ku Efuraimu akanena kuti: “Ndiloleni ndiwoloke,” pamenepo amuna a ku Giliyadi anali kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe wa ku Efuraimu?” Akayankha kuti: “Ayi!”  anali kumuuza kuti: “Nena kuti Shiboleti.”+ Koma iye anali kunena kuti: “Siboleti,” chifukwa sankatha kutchula mawuwa molondola. Akatero anali kumugwira ndi kumupha powolokera Yorodano pomwepo. Pa nthawi imeneyo panafa anthu 42,000 a ku Efuraimu.+  Yefita anaweruza Isiraeli zaka 6. Kenako Yefita wa ku Giliyadiyo anamwalira ndipo anaikidwa m’manda mumzinda wakwawo ku Giliyadi.  Pambuyo pa Yefita, Ibizani wa ku Betelehemu+ anayamba kuweruza Isiraeli.+  Ibizani anabereka ana aamuna 30 ndi ana aakazi 30. Iye anatuma anthu kukatenga atsikana 30 kuchokera kwina kuti akhale akazi a ana ake. Ndipo anaweruza Isiraeli kwa zaka 7. 10  Kenako Ibizani anamwalira ndipo anaikidwa m’manda ku Betelehemu. 11  Pambuyo pa Ibizani, Eloni wa fuko la Zebuloni+ anayamba kuweruza Isiraeli. Anaweruza Isiraeli zaka 10. 12  Kenako Eloni wa fuko la Zebuloni anamwalira, ndipo anaikidwa m’manda ku Aijaloni m’dziko la Zebuloni. 13  Pambuyo pa Eloni, Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni,+ anayamba kuweruza Isiraeli. 14  Iye anabereka ana aamuna 40 ndipo anali ndi zidzukulu 30. Onsewa anali kuyenda pa abulu 70.+ Ndipo Abidoni anaweruza Isiraeli zaka 8. 15  Kenako Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni anamwalira, ndipo anaikidwa m’manda ku Piratoni, m’dziko la Efuraimu, m’phiri la Aamaleki.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ndinaika moyo wanga m’dzanja langa.”