Oweruza 9:1-57

9  Patapita nthawi, Abimeleki+ mwana wa Yerubaala, anapita ku Sekemu+ kwa abale a mayi ake. Kumeneko anayamba kulankhula nawo ndiponso kulankhula ndi banja lonse la bambo a mayi akewo kuti:  “Chonde lankhulani nzika zonse za Sekemu zikumva, kuti, ‘Chabwino n’chiti kwa inu, kuti amuna 70,+ ana onse a Yerubaala akulamulireni, kapena munthu mmodzi akulamulireni? Ndipotu kumbukirani kuti ine ndine fupa lanu ndi mnofu wanu.’”+  Choncho abale a mayi ake anayamba kulankhula mawu onsewa nzika zonse za Sekemu zikumva, moti mitima yawo inakonda Abimeleki,+ chifukwa anati: “Ndi m’bale wathu ameneyu.”+  Kenako iwo anatenga ndalama zasiliva 70 m’kachisi wa Baala-beriti+ ndi kum’patsa. Ndalama zimenezi Abimeleki analembera ganyu anthu osowa ntchito ndi achipongwe+ kuti azim’tsatira.  Atatero anapita kunyumba ya bambo ake ku Ofira+ ndi kupha abale ake,+ ana aamuna 70 a Yerubaala, pamwala umodzi. Koma sanaphe Yotamu, mwana wamng’ono kwambiri mwa ana aamuna a Yerubaala, chifukwa anali atabisala.  Kenako nzika zonse za Sekemu ndi anthu onse m’nyumba ya Milo+ anasonkhana pamodzi kumene kunali chipilala pafupi ndi mtengo waukulu+ ku Sekemu.+ Kumeneko analonga Abimeleki ufumu.+  Yotamu atauzidwa zimene zinachitikazo, nthawi yomweyo anapita pamwamba pa phiri la Gerizimu+ ndi kulankhula nawo mofuula kuti: “Ndimvereni, inu nzika za Sekemu, ndipo Mulungu akumvereni:  “Kalekale mitengo inafuna kudzoza mfumu yawo. Pamenepo mitengoyo inauza mtengo wa maolivi+ kuti, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’+  Koma mtengo wa maoliviwo unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye kutulutsa mafuta amene amagwiritsidwa ntchito potamanda+ Mulungu ndi anthu, n’kupita kuti ndizikagwedezeka pamwamba pa mitengo ina?’+ 10  Kenako mitengoyo inauza mtengo wa mkuyu+ kuti, ‘Bwera kuno, ukhale mfumu yathu.’ 11  Koma mtengo wa mkuyuwo unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye kukoma kwanga ndi zipatso zanga zabwinozi, n’kupita kuti ndizikagwedezeka pamwamba pa mitengo ina?’+ 12  Kenako mitengoyo inauza mtengo wa mpesa kuti, ‘Bwera kuno, ukhale mfumu yathu.’ 13  Poyankha mtengo wa mpesawo unati, ‘Kodi ndisiye vinyo wanga watsopano amene amasangalatsa Mulungu ndi anthu,+ n’kupita kuti ndizikagwedezeka pamwamba pa mitengo ina?’ 14  Pamapeto pake, mitengo ina yonse inauza kamtengo kaminga+ kuti, ‘Bwera kuno, ukhale mfumu yathu.’ 15  Pamenepo kamtengo kamingako kanauza mitengoyo kuti, ‘Ngati mukunenadi zoona kuti mukufuna kundidzoza kuti ndikhale mfumu, bwerani mubisale mumthunzi wanga.+ Koma ngati si choncho, moto+ utuluke mwa ine ndi kunyeketsa mikungudza+ ya ku Lebanoni.’+ 16  “Tsopano kodi mwachita zimenezi m’choonadi komanso kuchokera pansi pa mtima, moti mwalonga Abimeleki ufumu?+ Ndipo kodi Yerubaala ndi nyumba yake mwamuchitira zinthu zabwino? Kodi mwamuchitira mogwirizana ndi zimene iye anachita, 17  poika moyo wake pangozi+ pamene anakumenyerani nkhondo+ kuti akulanditseni m’manja mwa Amidiyani?+ 18  Kodi inu mwaukira nyumba ya bambo anga lero kuti muphe ana ake+ aamuna 70+ pamwala umodzi, kuti muike Abimeleki, mwana wa kapolo wake wamkazi,+ kukhala mfumu+ yolamulira nzika za Sekemu chifukwa chakuti ndi m’bale wanu? 19  Ngati lero mwachitira zimenezi Yerubaala ndi a m’nyumba yake m’choonadi komanso kuchokera pansi pa mtima, sangalalani ndi Abimeleki ndipo nayenso asangalale nanu.+ 20  Koma ngati si choncho, moto+ utuluke mwa Abimeleki ndi kunyeketsa nzika za Sekemu ndi anthu a m’nyumba ya Milo,+ komanso moto+ utuluke mwa nzika za Sekemu ndi anthu a m’nyumba ya Milo ndi kunyeketsa Abimeleki.”+ 21  Zitatero Yotamu+ anathawira ku Beere, ndipo anakhala kumeneko chifukwa cha Abimeleki m’bale wake. 22  Choncho, Abimeleki modzikuza anakhala ngati mfumu ya Isiraeli zaka zitatu.+ 23  Ndiyeno Mulungu analola kuti pakhale kusamvana+ pakati pa Abimeleki ndi nzika za Sekemu, moti nzika za Sekemu zinayamba kuchitira Abimeleki zachinyengo.+ 24  Mulungu analola zimenezi kuti chiwawa chimene anachitira ana aamuna 70 a Yerubaala chiwabwerere pamutu pawo,+ ndi kuti aike magazi a anawo pa Abimeleki m’bale wawo chifukwa ndiye anawapha.+ Analolanso zimenezi kuti chiwawacho chibwerere pamutu pa nzika za Sekemu, chifukwa zinalimbikitsa+ Abimeleki kuti aphe abale ake. 25  Choncho, nzika za Sekemu zinamuikira obisalira anthu pamwamba pa mapiri kuti amuvulaze, ndipo obisalira anthuwo anali kulanda katundu wa munthu aliyense wodutsa njira imeneyo. Patapita nthawi, Abimeleki anauzidwa zimenezi. 26  Kenako kunabwera Gaala+ mwana wa Ebedi pamodzi ndi abale ake. Iwo analowa mu Sekemu,+ ndipo nzika za mu Sekemu zinayamba kum’khulupirira.+ 27  Ndiyeno monga mwa masiku onse, iwo analowa m’munda n’kuyamba kukolola ndi kuponda mphesa za m’minda yawo ndi kuchita chikondwerero.+ Kenako analowa m’nyumba ya mulungu wawo,+ ndipo anadya ndi kumwa+ ndi kutemberera+ Abimeleki. 28  Pamenepo Gaala mwana wa Ebedi anati: “Abimeleki ndani,+ ndipo Sekemu ndani kuti tim’tumikire? Kodi iye si mwana wa Yerubaala,+ ndipo mtumiki wake si Zebuli?+ Ena nonsenu tumikirani ana a Hamori,+ bambo a Sekemu, koma ifeyo tim’tumikire chifukwa chiyani? 29  Haa! Anthu awa akanakhala m’manja mwanga,+ ndikanam’chotsa Abimeleki.” Ndiyeno anauza Abimeleki kuti: “Chulukitsa asilikali ako ndipo udzamenyane ndi ine.”+ 30  Pamene Zebuli, kalonga wa mzindawo, anamva mawu a Gaala mwana wa Ebedi,+ anakwiya koopsa. 31  Choncho anachitira chinyengo Gaala ndi kutumiza mithenga kwa Abimeleki kuti: “Gaala mwana wa Ebedi pamodzi ndi abale ake alowa mu Sekemu+ ndipo akulimbikitsa anthu a mumzindawu kuti akuukireni. 32  Tsopano inu mudzuke usiku+ pamodzi ndi anthu anu, ndipo mukam’bisalire+ m’thengo. 33  Ndiyeno mawa mudzuke mwamsanga dzuwa likangotuluka, ndi kuthamangira mumzindawo. Ndipo iye ndi anthu amene ali nawo akatuluka kudzamenyana nanu, mum’chitire zimene mungathe kuti mum’gonjetse.” 34  Pamenepo Abimeleki ndi anthu onse amene anali naye anadzuka usiku ndi kubisalira Sekemu, atagawana m’magulu anayi. 35  Patapita nthawi, Gaala+ mwana wa Ebedi anatuluka ndi kuima pachipata cha mzinda. Ndiyeno Abimeleki ndi anthu amene anali naye anadzuka m’malo amene anam’bisalira. 36  Gaala ataona anthuwo, nthawi yomweyo anauza Zebuli kuti: “Taona, anthu akutsika kuchokera pamwamba pa mapiri.” Koma Zebuli anati: “Si anthu amenewo, ukuona zithunzithunzi za mapiri.”+ 37  Zitatero, Gaala ananenanso kuti: “Taona, anthu akubwera chakuno kuchokera pakati pa dziko, ndipo gulu limodzi likubwera kudzera njira yodutsa ku mtengo waukulu wa Meyonenimu.”* 38  Pamenepo Zebuli anamuuza kuti: “Kodi waiwala mawu ako aja amene unanena+ kuti, ‘Abimeleki ndani, kuti timutumikire?’+ Kodi amenewa si anthu amene unawakana?+ Ndiyetu pita, ukamenyane nawo.” 39  Choncho Gaala anatsogolera nzika za Sekemu ndi kuyamba kumenyana ndi Abimeleki. 40  Pamenepo Abimeleki anathamangitsa Gaala, ndipo Gaala anathawa. Anthu ochuluka anaphedwa ndipo mitembo inali paliponse mpaka kukafika kuchipata cha mzinda. 41  Zitatero, Abimeleki anapitiriza kukhala ku Aruma, ndipo Zebuli+ anathamangitsa Gaala+ ndi abale ake kuti asakhalenso m’Sekemu.+ 42  Ndiyeno tsiku lotsatira anthu anayamba kupita kunja kwa mzinda, ndipo ena anauza Abimeleki+ za nkhani imeneyi. 43  Atamva zimenezi anatenga anthu ake ndi kuwagawa m’magulu atatu+ n’kubisalira anthuwo m’thengo. Poyang’ana, anaona anthu akutuluka mumzindawo, ndipo anawaukira n’kuwakantha. 44  Abimeleki ndi magulu amene anali nawo anathamanga kuti akaime pachipata cha mzinda, pamene magulu ena awiri anathamangira kwa anthu amene anali kunja kwa mzinda, ndipo anayamba kuwakantha.+ 45  Ndiyeno Abimeleki anamenyana ndi mzindawo tsiku lonse, n’kuulanda. Anapha anthu amene anali mumzindawo+ ndipo anaugwetsa+ n’kuthira mchere panthaka ya mzindawo.+ 46  Nzika zonse za munsanja ya Sekemu zitamva nkhani imeneyi, nthawi yomweyo zinalowa m’chipinda chotetezeka cha m’nyumba ya Eli-beriti.*+ 47  Ndiyeno Abimeleki anauzidwa kuti nzika zonse za munsanja ya Sekemu zasonkhana pamodzi. 48  Zitatero Abimeleki anakwera phiri la Zalimoni+ pamodzi ndi anthu onse amene anali naye. Tsopano Abimeleki anatenga nkhwangwa m’manja mwake, n’kudula nthambi ya mtengo, ndipo nthambiyo anainyamula n’kuiika paphewa lake. Pamenepo anauza anthu amene anali naye kuti: “Zimene mwaona ine ndikuchita, muchitenso zomwezo mofulumira!”+ 49  Chotero anthu onsewo, aliyense wa iwo anadula nthambi yake ndi kutsatira Abimeleki. Kenako anatsamiritsa nthambizo pachipinda chotetezekacho n’kuchiyatsa moto, moti nawonso anthu onse okhala munsanja ya Sekemu, amuna ndi akazi pafupifupi 1,000, anafa.+ 50  Tsopano Abimeleki anapita ku Tebezi+ kumene anamenyana ndi mzindawo n’kuulanda. 51  Popeza pakati pa mzindawo panali nsanja yolimba, amuna ndi akazi onse, nzika zonse za mzindawo, zinathawira munsanjayo. Atalowa mmenemo, anatseka chitseko ndi kukwera padenga la nsanjayo. 52  Pamenepo Abimeleki anapita kunsanjayo ndi kuyamba kumenyana ndi anthu amene anali mmenemo. Ndiyeno anayandikira khomo la nsanjayo kuti aitenthe ndi moto.+ 53  Zitatero, mkazi wina anagwetsera mwala wa mphero pamutu wa Abimeleki ndi kuuphwanya.+ 54  Msangamsanga Abimeleki anaitana mtumiki wake womunyamulira zida ndi kumuuza kuti: “Tenga lupanga lako undiphe,+ kuopera kuti anthu anganene za ine kuti, ‘Anaphedwa ndi mkazi.’” Nthawi yomweyo, mtumiki wakeyo anamubaya* ndi lupanga, ndipo anafa.+ 55  Tsopano anthu a mu Isiraeli ataona kuti Abimeleki wafa, aliyense wa iwo anapita kwawo. 56  Chotero Mulungu anachititsa zoipa zimene Abimeleki anachitira bambo ake mwa kupha abale ake 70, kum’bwerera pamutu pake.+ 57  Ndipo zoipa zonse za amuna a m’Sekemu, Mulungu anachititsa kuti ziwabwerere pamutu pawo, kuti temberero+ la Yotamu+ mwana wa Yerubaala,+ liwagwere.+

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza, “Ochita Zamatsenga.” Onani De 18:14.
Dzinali limatanthauza, “Mulungu wa pangano.” Ameneyu ndi Baala wa ku Sekemu.
Ena amati “kugwaza.”