Oweruza 2:1-23
2 Ndiyeno mngelo wa Yehova+ ananyamuka ku Giligala+ kupita ku Bokimu,+ ndipo anati: “Ndinakutulutsani mu Iguputo ndi kukulowetsani m’dziko limene ndinalumbirira makolo anu.+ Komanso ndinakuuzani kuti, ‘Sindidzaphwanya konse pangano langa ndi inu.+
2 Ndipo inu musachite pangano ndi anthu okhala m’dziko ili,+ m’malomwake mugwetse maguwa awo ansembe.’+ Koma inu simunamvere mawu anga.+ N’chifukwa chiyani mwachita zimenezi?+
3 Choncho nanenso ndikuti, ‘Sindiwapitikitsa pamaso panu, koma akhala msampha kwa inu,+ ndipo milungu yawo ikhala ngati nyambo.’”+
4 Mngelo wa Yehova atalankhula mawu amenewa kwa ana onse a Isiraeli, anthuwo anayamba kulira mokweza mawu.+
5 Choncho anatcha malowo dzina lakuti Bokimu.* Ndipo anapereka nsembe kwa Yehova pamalowo.
6 Yoswa atauza anthuwo kuti apite, aliyense wa ana a Isiraeliwo anapita ku cholowa chake, kukatenga dzikolo kukhala lawo.+
7 Ndipo anthuwo anapitiriza kutumikira Yehova masiku onse a Yoswa ndi masiku onse a akulu amene anapitiriza kukhala ndi moyo Yoswa atamwalira, akulu amene anaona ntchito zonse zazikulu zimene Yehova anachitira Isiraeli.+
8 Yoswa mtumiki wa Yehova, mwana wa Nuni, anamwalira ali ndi zaka 110.+
9 Ndipo anamuika m’manda ku Timinati-heresi,*+ m’dera limene analandira monga cholowa chake, m’dera lamapiri la Efuraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.+
10 Anthu onse a m’badwo umenewo anamwalira ndi kugona ndi makolo awo,+ ndipo pambuyo pawo panauka m’badwo wina umene sunadziwe Yehova kapena ntchito zimene iye anachitira Isiraeli.+
11 Ndiyeno ana a Isiraeli anayamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova,+ n’kuyamba kutumikira Abaala.+
12 Iwo anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo,+ n’kuyamba kutsatira milungu ina mwa milungu ya anthu owazungulira.+ Anayamba kugwadira milungu imeneyo, moti anakhumudwitsa Yehova.+
13 Anasiya Yehova ndi kuyamba kutumikira Baala ndi zifaniziro za Asitoreti.+
14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Isiraeli,+ moti anawapereka m’manja mwa ofunkha, ndipo anayamba kufunkha zinthu zawo.+ Iye anawagulitsa kwa adani awo owazungulira+ moti sanathe kuima pamaso pa adani awo.+
15 Kulikonse kumene apita, dzanja la Yehova linali kuwaukira ndi kuwadzetsera masoka,+ monga mmene Yehova ananenera ndiponso monga mmene Yehova analumbirira kwa iwo,+ moti iwo anali kuvutika kwambiri.+
16 Zikatero, Yehova anali kuwapatsa oweruza,+ ndipo anali kuwapulumutsa m’manja mwa ofunkha.+
17 Ana a Isiraeli sanamvere ngakhale oweruza awo, koma anachita chiwerewere+ ndi milungu ina+ ndi kuigwadira. Iwo anapatuka mwamsanga panjira imene makolo awo anayendamo. Makolo awo anayenda m’njira imeneyo mwa kumvera malamulo a Yehova,+ koma iwo sanachite mofanana ndi makolo awo.
18 Yehova akawapatsa oweruza,+ Yehova anali kukhaladi ndi aliyense wa oweruzawo, ndipo iye anali kuwapulumutsa m’manja mwa adani awo masiku onse a moyo wa woweruzayo. Yehova anali kuchita zimenezo pakuti anali kuwamvera chisoni+ akamva kubuula kwawo chifukwa cha owapondereza ndi owakankhakankha.+
19 Ndiyeno zinali kuchitika kuti woweruza akamwalira, ana a Isiraeli anali kupatuka ndi kuchita zinthu zowawonongetsa kuposanso makolo awo. Anali kuchita zimenezi mwa kutsatira milungu ina, kuitumikira ndi kuigwadira.+ Iwo sanasiye zochita zawozo ndiponso khalidwe lawo la unkhutukumve.+
20 Chotero mkwiyo wa Yehova unayakira+ Isiraeli ndipo anati: “Popeza mtundu umenewu waphwanya pangano langa+ limene ndinalamula makolo awo kuti alisunge, ndipo sanamvere mawu anga,+
21 ine sindipitikitsanso pamaso pawo mtundu uliwonse pa mitundu imene Yoswa anaisiya pamene ankamwalira.+
22 Ndichita zimenezi kuti ndiyese+ Isiraeli kudzera mwa mitundu imeneyi, kuti ndione ngati angasunge njira ya Yehova mwa kuyendamo monga mmene makolo awo anachitira, kapena ayi.”
23 Choncho, Yehova analola mitundu imeneyi kukhalabe, osaipitikitsa mwamsanga,+ ndipo sanaipereke m’manja mwa Yoswa.