Oweruza 3:1-31

3  Pali mitundu+ imene Yehova anailola kukhalabe m’dzikoli n’cholinga choti ayese+ nayo Aisiraeli, kutanthauza Aisiraeli onse amene sanaonepo iliyonse mwa nkhondo zimene mtunduwo unamenya m’dziko la Kanani.+  (Mitunduyo anailola kukhalabe kuti mibadwo ya ana a Isiraeli imene sinaonepo nkhondo, iphunzire ndi kudziwa kumenya nkhondo).  Mitunduyo ndi olamulira asanu ogwirizana+ a Afilisiti,+ Akanani onse,+ ngakhalenso Asidoni+ ndi Ahivi+ okhala m’phiri la Lebanoni,+ kuchokera kuphiri la Baala-herimoni+ mpaka kumalire a dera la Hamati.+  Mulungu anapitirizabe kugwiritsa ntchito mitunduyo poyesa+ Aisiraeli, kuti aone ngati Aisiraeliwo adzamvera malamulo a Yehova amene anaperekedwa kwa makolo awo kudzera mwa Mose.+  Ana a Isiraeli anakhala pakati pa Akanani,+ amene ndi Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+  Aisiraeli anatenga ana aakazi a Akanani kukhala akazi awo,+ ndipo ana awo aakazi anawapereka kwa ana aamuna a Akanani,+ moti Aisiraeli anayamba kutumikira milungu ya Akanani.+  Chotero ana a Isiraeli anachita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo anaiwala Yehova Mulungu wawo,+ moti anayamba kutumikira Abaala+ ndi mizati yopatulika.+  Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Aisiraeli,+ moti anawagulitsa+ kwa Kusani-risataimu, mfumu ya Mesopotamiya.+ Ana a Isiraeli anatumikira Kusani-risataimu zaka 8.  Ndipo ana a Isiraeli anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+ Pamenepo Yehova anapereka mpulumutsi+ wa ana a Isiraeli kuti awapulumutse. Ameneyu anali Otiniyeli,+ mwana wamwamuna wa Kenazi,+ mng’ono wake wa Kalebe.+ 10  Mzimu+ wa Yehova unakhala pa iye, ndipo anakhala woweruza wa Isiraeli. Atapita kunkhondo, Yehova anapereka Kusani-risataimu mfumu ya Siriya m’manja mwake, moti anam’gonjetsa.+ 11  Zitatero dziko linakhala pa mtendere zaka 40. Kenako Otiniyeli, mwana wa Kenazi, anamwalira. 12  Ana a Isiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Pamenepo Yehova analola Egiloni mfumu ya Mowabu+ kukula mphamvu ndi kupondereza Isiraeli,+ chifukwa Aisiraeliwo anachita zoipa pamaso pa Yehova.+ 13  Kuwonjezera apo, anasonkhanitsa ana a Amoni+ ndi Amaleki+ kuti alimbane ndi Aisiraeli. Amenewa anakantha Isiraeli ndi kulanda mzinda wa mitengo ya kanjedza.+ 14  Ndipo ana a Isiraeli anatumikira Egiloni, mfumu ya Mowabu zaka 18.+ 15  Pamenepo ana a Isiraeli anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+ Choncho Yehova anawapatsa mpulumutsi, Ehudi,+ munthu wogwiritsa ntchito dzanja lamanzere,+ wa fuko la Benjamini,+ mwana wa Gera. M’kupita kwa nthawi, ana a Isiraeli anatumiza msonkho wawo kwa Egiloni mfumu ya Mowabu, kudzera mwa Ehudi. 16  Ehudi anali atadzipangira lupanga lakuthwa konsekonse,+ kutalika kwake mkono umodzi,* ndipo analimangirira m’chiuno kudzanja lamanja, mkati mwa chovala chake.+ 17  Atafika kwa Egiloni mfumu ya Mowabu,+ anapereka msonkho umene anabweretsa. Komatu Egiloni anali munthu wonenepa kwambiri. 18  Ehudi atapereka msonkhowo,+ anauza anthu amene ananyamula msonkhowo kuti azipita. 19  Atafika pamiyala yogoba* imene inali ku Giligala,+ anabwerera kwa mfumu ndi kuiuza kuti: “Pepanitu mfumu, ndili ndi uthenga wachinsinsi woti ndikuuzeni.” Pamenepo mfumuyo inati: “Khala chete!” Itatero, onse amene anaimirira pafupi ndi mfumuyo anatuluka.+ 20  Ehudi anafika kwa mfumuyo ili yokhayokha m’chipinda chapadera chozizira bwino, chimene chinali padenga.* Pamenepo Ehudi anati: “Uthenga umene ndili nawo ndi wochokera kwa Mulungu.” Atatero, mfumuyo inanyamuka pampando wake wachifumu. 21  Pamenepo, Ehudi analowetsa dzanja lake lamanzere m’chovala chake, ndipo anasolola lupanga limene linali m’chiuno kudzanja lake lamanja ndi kulizika m’mimba mwa Egiloni. 22  Lupangalo linalowa ndi chigwiriro chomwe moti mafuta anaphimba lupangalo chifukwa sanalizule m’mimba mwakemo, ndipo chimbudzi chinayamba kutuluka. 23  Zitatero Ehudi anatulukira polowera mphepo, koma anasiya atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda cha padenga, 24  iyeyo n’kutuluka panja.+ Pamenepo atumiki a Egiloni anafika n’kuyamba kuyang’ana, ndipo anapeza zitseko za chipinda cha padenga zili zokhoma. Ndiyeno anati: “Ayenera kuti akudzithandiza+ m’chipinda chozizira bwino cha mkatikati.” 25  Iwo anapitiriza kudikira mpaka anataya mtima chifukwa anaona kuti mfumu sikutsegula zitseko za chipinda cha padenga. Pamenepo anatenga kiyi ndi kutsegula zitsekozo. Atatero anangoona mbuye wawo ali thasa pansi, wakufa. 26  Iwo akuganizaganiza zimene zachitika, Ehudi anathawa, ndipo anadutsa pamiyala yogoba+ ndi kuthawira ku Seira. 27  Atafika kumeneko anayamba kuliza lipenga la nyanga+ ya nkhosa m’dera lamapiri la Efuraimu.+ Iye ali patsogolo, ana a Isiraeli anatsika naye limodzi kuchoka m’dera lamapirilo. 28  Pamenepo anawauza kuti: “Nditsatireni,+ chifukwa Yehova wapereka Amowabu, adani anu, m’manja mwanu.”+ Atatero, anam’tsatira kukatsekereza Amowabu pamalo owolokera mtsinje+ wa Yorodano, ndipo sanalole aliyense kuwoloka. 29  Pa nthawi imeneyo anakantha amuna achimowabu 10,000.+ Aliyense mwa amunawo anali wojintcha+ ndipo aliyense wa iwo anali mwamuna wolimba mtima, koma palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+ 30  Chotero Mowabu anagonjetsedwa tsiku limenelo ndi Isiraeli, ndipo dzikolo linakhala pa mtendere zaka 80.+ 31  Pambuyo pa Ehudi panadzakhala Samagara+ mwana wamwamuna wa Anati. Ameneyu anapha amuna achifilisiti+ 600 ndi chisonga chotosera ng’ombe pozitsogolera. Ameneyunso anapulumutsa Isiraeli.+

Mawu a M'munsi

“Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Koma ena amakhulupirira kuti lupanga limeneli kutalika kwake linali masentimita 38.
Kapena kuti, “mafano osema.”
Kapena kuti, “patsindwi.”