Oweruza 5:1-31

5  Pa tsiku limenelo, Debora+ ndi Baraki+ mwana wa Abinowamu,+ anayamba kuimba nyimbo,+ ndipo anati:   “Posunga tsitsi lalitali mu Isiraeli monga lumbiro la nkhondo,Chifukwa cha kudzipereka mwaufulu kwa anthu,+Tamandani Yehova.+   Mvetserani mafumu inu,+ inunso nduna, tcherani khutu:Ine ndidzaimbira Yehova, ndithu ndidzamuimbira.Ndidzaimbira Yehova, Mulungu wa Isiraeli,+ nyimbo zomutamanda.+   Yehova, pamene munayenda kuchokera ku Seiri,+Pamene munaguba kuchokera kudera la Edomu,+Dziko linagwedezeka,+ kumwamba kunagwetsa madzi,+Mitambo inagwetsa madzi.   Mapiri anasungunuka ndi kuyenda ngati madzi, kuchoka pamaso pa Yehova,+Sinai+ uyu anayenda ngati madzi kuchoka pamaso pa Yehova,+ Mulungu wa Isiraeli.+   M’masiku a Samagara+ mwana wa Anati,M’masiku a Yaeli,+ m’njira munalibe odutsamo,Ndipo oyenda m’misewu anayamba kuyenda njira zolambalala.+   Anthu okhala m’midzi anachoka m’midzi yawo, anachoka m’midzi ya Isiraeli,+Kufikira pamene ine Debora+ ndinauka,Kufikira pamene ine ndinauka monga mayi mu Isiraeli.+   Anayamba kusankha milungu yatsopano.+Atatero m’pamene nkhondo inafika m’mizinda.+Panalibe chishango kapena mkondo waung’ono,Pakati pa anthu 40,000 mu Isiraeli.+   Mtima wanga uli pa atsogoleri a asilikali a Isiraeli,+Amene anadzipereka mwaufulu pakati pa anthu awo.+Tamandani Yehova.+ 10  Inu okwera abulu ofiirira,+Inu okhala pansalu zokwera mtengo,Ndi inu oyenda mumsewu,Ganizirani ntchito za Mulungu izi:+ 11  Mawu a anthu ena otunga madzi anamveka pamalo otungira madzi,+Kumeneko anayamba kusimba ntchito zolungama za Yehova,+Anasimba ntchito zolungama za anthu ake okhala m’midzi ya Isiraeli.Atatero m’pamene anthu a Yehova anapita kumizinda. 12  Dzuka! Dzuka Debora iwe!+Dzuka! Dzuka! Imba nyimbo!+Imirira Baraki iwe!+ Tsogolera anthu ogwidwa, iwe mwana wa Abinowamu.+ 13  Pamenepo, opulumuka anapita kwa anthu otchuka.Anthu a Yehova anabwera kwa ine, pokalimbana ndi amphamvu. 14  Amene anali m’chigwa anachokera m’fuko la Efuraimu,+Ndipo iwo anali ndi iwe Benjamini, pakati pa anthu a mtundu wako.Atsogoleri a asilikali anachokera kwa Makiri,+Ndipo osunga zida za mlembi, anachokera m’fuko la Zebuloni.+ 15  Akalonga a fuko la Isakara+ anali ndi Debora,Mmene anachitira Isakara, ndi mmenenso anachitira Baraki.+Anamutumiza kuchigwa akuyenda wapansi.+Pakati pa magulu a m’fuko la Rubeni, panali kufufuza mozama za mumtima.+ 16  Unakhaliranji pansi pakati pa zikwama ziwiri za pachishalo,N’kumamvetsera nyimbo za zitoliro zoimbira nkhosa?+Pakuti m’magulu a fuko la Rubeni munali kufufuza mozama za mumtima.+ 17  Anthu a ku Giliyadi anakhalabe kwawo komweko, kutsidya lina la Yorodano.+Ndipo n’chifukwa chiyani Dani anakhalabe m’zombo kwa kanthawi?+Aseri anangokhala phee pagombe la nyanja,Nakhalabe pamadoko ake.+ 18  Anthu a m’fuko la Zebuloni ndiwo anatonza miyoyo yawo mpaka kuiika pangozi.+Anthu a m’fuko la Nafitali+ nawonso anachita zomwezo m’mapiri a dziko.+ 19  Mafumu anabwera ndi kumenya nkhondo.Pamenepo mafumu a Kanani anamenya nkhondo,+Anamenya nkhondo ku Taanaki,+ pafupi ndi madzi a ku Megido.+Iwo sanapezepo phindu la siliva.+ 20  Nyenyezi zinamenya nkhondo zili kumwamba,+Zinamenyana ndi Sisera zili m’njira zawo. 21  Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,+Mtsinje wakalekale, mtsinje wa Kisoni.+Moyo wangawe, unapondereza adani amphamvu.+ 22  Pamenepo ziboda za mahatchi* zinaguguda pansi,+Chifukwa cha kuthamangathamanga kwa mahatchiwo. 23  Mngelo wa Yehova+ anati: ‘Tembererani+ Merozi,Tembererani anthu ake mosaleka,Chifukwa sanathandize Yehova,Sanabwere ndi anthu amphamvu kudzathandiza Yehova.’ 24  Yaeli,+ mkazi wa Hiberi Mkeni,+ akhale wodalitsika pakati pa akazi onse,Akhale wodalitsika pakati pa akazi onse okhala m’mahema.+ 25  Sisera anapempha madzi, Yaeli anapereka mkaka.Anamupatsa mkaka, m’mbale yolowa yaikulu yomwera anthu olemekezeka pa phwando.+ 26  Kenako anatambasula dzanja lake ndi kugwira chikhomo cha hema.Anatambasulanso dzanja lake lamanja ndi kutenga nyundo yamtengo, ya anthu ogwira ntchito mwamphamvu.+Atatero anakhoma Sisera m’mutu ndipo chikhomocho chinatulukira mbali ina ya mutu wakewo.+Anaphwanya ndi kudula fupa la pafupi ndi khutu la Sisera. 27  Sisera anakomoka, kugwa ndi kugona pakati pa mapazi ake,Iye anakomoka n’kugwa.Pamene anakomokerapo, anagwera pomwepo, atagonja.+ 28  Munthu wamkazi anaima pawindo ndi kuyang’ana kunja, kumuyembekezera,Amayi a Sisera anayang’ana kunja pawindo,*+ kumuyembekezera, ndipo anati,‘N’chifukwa chiyani galeta lake lankhondo lachedwa kubwera?+N’chifukwa chiyani kuguguda kwa magaleta ake kwachedwa kumveka?’+ 29  Akazi anzeru pakati pa gulu la amayi ake olemekezeka+ anali kumuyankha,Iyenso n’kumadziyankhira mumtima mwake, kuti, 30  ‘Kodi sanapeze zofunkha ndipo ayenera kuzigawa?+Kodi sayenera kugawa mkazi mmodzi, kapenanso akazi awiri kwa mwamuna aliyense wamphamvu,+Ndi nsalu za Sisera zofunkhidwa zonyika mu utoto, ndithu nsalu zofunkhidwa zonyika mu utoto?Kodi sayenera kugawa chovala chopeta chonyika mu utoto, inde, zovala ziwiri zopeta,Kuti amuna ofunkha avale m’makosi awo?’ 31  Inu Yehova, adani anu onse afafanizidwe chimodzimodzi,+Ndipo okukondani inu+ akhale amphamvu ngati mmene dzuwa limakhalira.”+Choncho, dzikolo linakhala pa mtendere zaka 40.+

Mawu a M'munsi

“Hatchi” ena amati “hosi” kapena “kavalo.”
Pawindo limeneli panali potchingidwa ndi timatabwa tolukanalukana.