Oweruza 7:1-25

7  Pamenepo Yerubaala,+ kapena kuti Gidiyoni,+ pamodzi ndi anthu onse amene anali naye, anadzuka m’mawa kwambiri ndi kumanga msasa pachitsime cha Harodi. Msasa wa Amidiyani unali chakumpoto, m’chigwa, kuphiri la More.  Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene uli nawowa ndi ochuluka kwambiri kuti ndipereke Amidiyani m’manja mwawo,+ chifukwa mwina Isiraeli angadzitukumule+ pamaso panga ndi kunena kuti, ‘Ndinadzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.’+  Tsopano lengeza ndipo anthu onse amve, kuti, ‘Alipo kodi akuchita mantha ndi kunjenjemera? Abwerere.’”+ Choncho ndi mawu amenewa, Gidiyoni anayesa anthuwo. Pamenepo, anthu 22,000 anabwerera ndipo panatsala anthu 10,000.  Komabe, Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene atsalawa ndi ochulukabe.+ Pita nawo kumadzi kuti ndikawayese kumeneko. Ndiyeno amene ndidzakuuza kuti, ‘Uyu apite nawe,’ ameneyo apite nawe, koma aliyense amene ndidzakuuza kuti, ‘Uyu asapite nawe,’ ameneyo asapite nawe.”  Choncho Gidiyoni anauza anthuwo kuti apite kumadzi.+ Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Aliyense amene akamwe madzi potunga madziwo ndi manja n’kumamwera m’manjamo, ukamuike kumbali ina. Ndipo aliyense amene pakumwa madzi akawerame n’kugwada,+ ukamuike kumbali inanso.”  Ndipo anthu amene anamwa madzi ndi manja anakwana 300. Koma ena onse anamwa atawerama n’kugwada.  Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Ndidzapulumutsa anthu inu pogwiritsa ntchito amuna 300 amene anamwa madzi ndi manja awo, ndipo ndidzapereka Amidiyani m’manja mwanu.+ Koma ena onsewa, aliyense abwerere kwawo.”  Choncho, iye anabweza amuna onse a Isiraeli koma anatsala ndi amuna 300 aja. Amenewa anatenga chakudya ndi malipenga a nyanga ya nkhosa+ m’manja mwa anthu amene anali kubwerera kwawo. Apa n’kuti msasa wa Amidiyani uli kumunsi kwawo, m’chigwa.+  Ndiyeno usiku umenewo,+ Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Nyamuka, pita kumsasa wa Amidiyani ndi kuuthira nkhondo, chifukwa ndaupereka m’manja mwako.+ 10  Koma ngati ukuchita mantha kupita kumsasawo, choyamba upiteko ndi Pura, mtumiki wako.+ 11  Kumeneko ukamvetsere zolankhula zawo.+ Pambuyo pake udzalimba mtima+ ndipo udzapitadi kumsasawo ndi kuuthira nkhondo.” Pamenepo, Gidiyoni ndi Pura mtumiki wake, anapita kumunsi pafupi kwambiri ndi asilikali amene anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo amene anali mumsasawo. 12  Tsopano Amidiyani ndi Aamaleki pamodzi ndi anthu onse a Kum’mawa,+ anaphimba chigwa chonse chifukwa cha kuchuluka kwawo ngati dzombe.+ Ngamila zawo+ zinali zosawerengeka, zochuluka ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja. 13  Tsopano Gidiyoni anafika kumsasawo ndipo anangomva munthu akusimbira mnzake zimene analota, kuti: “Tamvera zimene ndalota ine.+ Ndalota mtanda wa mkate wa balere wozungulira ukugubuduzika kubwera mumsasa wa Amidiyani. Mtandawo unafika pahema lina ndi kuliwomba moti hemalo linagwa.+ Kenako mtandawo unagadabuza hemalo n’kuliphwasula.” 14  Pamenepo mnzakeyo anayankha+ kuti: “Si china ayi. Imeneyi ndi nkhondo ya Gidiyoni+ mwana wa Yowasi, mwamuna wa ku Isiraeli. Mulungu woona+ wapereka Amidiyani ndi msasa wathu wonse m’manja mwake.”+ 15  Gidiyoni atangomva lotolo ndi tanthauzo lake,+ analambira Mulungu.+ Kenako anabwerera kumsasa wa Isiraeli ndi kuwauza kuti: “Tiyeni,+ pakuti Yehova wapereka msasa wa Amidiyani m’manja mwanu.” 16  Ndiyeno amuna 300 aja anawagawa m’magulu atatu. Aliyense anamupatsa lipenga la nyanga ya nkhosa+ ndi mtsuko waukulu wopanda kanthu, ndipo m’mitsukomo anaikamo miyuni. 17  Kenako anawauza kuti: “Muonetsetse ndi kuphunzira pa zimene ine ndikuchita, ndipo nanunso muchite zomwezo. Ndikakafika m’malire a msasa, zimene ine ndikachite, nanunso mukachite zomwezo. 18  Ine ndikaliza lipenga la nyanga ya nkhosa pamodzi ndi anthu onse a m’gulu langa, nanunso mulize malipenga anu kuzungulira msasa wonse,+ ndipo munene kuti, ‘Nkhondo ya Yehova+ ndi ya Gidiyoni!’” 19  Chotero Gidiyoni anafika kumalire a msasa pamodzi ndi amuna 100 amene anali naye. Apa n’kuti ulonda wapakati pa usiku*+ ukungoyamba kumene, ndipo anali atangosintha kumene alonda a msasa. Pamenepo analiza malipenga a nyanga ya nkhosa+ ndi kuswa mitsuko yaikulu imene inali m’manja mwawo.+ 20  Ndipo magulu atatuwo analiza malipenga a nyanga ya nkhosa+ ndi kuphwanya mitsuko ikuluikulu ija. Atatero ananyamulanso miyuni ndi dzanja lawo lamanzere ndipo malipenga anali m’dzanja lawo lamanja, n’kuyamba kufuula kuti: “Nkhondo ya Yehova+ ndi ya Gidiyoni!” 21  Pa nthawi imeneyi aliyense anaimirirabe pamalo ake kuzungulira msasa wonsewo, ndipo mumsasa wonse wa Amidiyani munali chipwirikiti, anthu anali kufuula ndi kuthawa.+ 22  Amuna 300+ aja anapitiriza kuliza malipenga,+ ndipo Yehova anachititsa Amidiyani kuukirana okhaokha mumsasa wonsewo.+ Anthu onse a mumsasawo anathawa mpaka kukafika ku Beti-sita, ndi ku Zerera mpaka kumalire kwa mzinda wa Abele-mehola+ pafupi ndi Tabati. 23  Pa nthawiyi anasonkhanitsa pamodzi amuna a mu Isiraeli kuchokera m’madera a mafuko a Nafitali,+ Aseri+ ndi Manase+ yense, ndipo anapitikitsa+ Amidiyani. 24  Ndiyeno Gidiyoni anatumiza amithenga kudera lonse lamapiri la Efuraimu,+ kuti: “Pitani mofulumira ku Beti-bara ndi kumtsinje wa Yorodano, ndipo mukaike amuna m’malo owolokera kuti Amidiyani asadutse.” Choncho, amuna onse a Efuraimu anasonkhana pamodzi ndipo anatseka malo owolokera Yorodano ndi mitsinje yake ing’onoing’ono+ mpaka ku Beti-bara. 25  Anagwiranso akalonga awiri a Amidiyani, Orebi ndi Zeebi.+ Atatero, anapha Orebi pathanthwe la Orebi,+ ndipo Zeebi anamuphera pamalo opondera mphesa a Zeebi. Iwo anapitirizabe kuthamangitsa Amidiyani,+ kenako anabweretsa mutu wa Orebi ndi Zeebi kwa Gidiyoni m’chigawo cha Yorodano.+

Mawu a M'munsi

“Ulonda wapakati pa usiku” unali kuyamba 10 koloko usiku mpaka 2 koloko usiku.