Oweruza 11:1-40

11  Tsopano Yefita+ wa ku Giliyadi+ anakhala mwamuna wamphamvu ndi wolimba mtima.+ Mayi ake anali hule,+ ndipo bambo ake omubereka anali Giliyadi.  Mkazi wa Giliyadi anapitiriza kumuberekera ana aamuna. Anawo atakula, anathamangitsa Yefita ndi kumuuza kuti: “Iwe suyenera kulandira cholowa m’nyumba ya bambo athu,+ chifukwa ndiwe mwana wa mayi wina.”  Choncho Yefita anathawa chifukwa cha abale ake ndipo anakakhala m’dziko la Tobu.+ Kumeneko anthu osowa ntchito anali kusonkhana kwa Yefita ndi kupita naye limodzi kukaukira adani awo.+  Ndiyeno patapita nthawi, ana a Amoni anayamba kumenyana ndi Aisiraeli.+  Ana a Amoni atayamba kumenyana ndi Aisiraeli,+ akulu a ku Giliyadi anapita mwamsanga kukatenga Yefita kudziko la Tobu.+  Iwo anauza Yefita kuti: “Tiye ukakhale mtsogoleri wa gulu lathu lankhondo, ndipo tikamenyane ndi ana a Amoni.”  Koma Yefita anauza akulu+ a ku Giliyadiwo kuti: “Kodi si inu amene munadana nane ndi kundithamangitsa m’nyumba ya bambo anga?+ N’chifukwa chiyani tsopano mwabwera kwa ine pamene mwakumana ndi mavuto?”+  Pamenepo akulu a ku Giliyadi anayankha Yefita kuti: “Eya, n’chifukwa chake tsopano tabwerera+ kwa iwe. Choncho upite nafe kukamenyana ndi ana a Amoni, ndipo ukhale mtsogoleri wa anthu onse okhala ku Giliyadi.”+  Ndiyeno Yefita anauza akulu a ku Giliyadiwo kuti: “Ngati mukunditenga kuti tikamenyane ndi ana a Amoni, ndipo Yehova akakawapereka+ m’manja mwanga, ndidzakhala mtsogoleri wanu!” 10  Poyankha akulu a ku Giliyadi anauza Yefita kuti: “Yehova amve makambirano athuwa+ ndi kutiweruza ngati sitidzachita zogwirizana ndi mawu ako.”+ 11  Pamenepo Yefita anapita ndi akulu a ku Giliyadi, ndipo anthu anamuika kukhala mtsogoleri wawo komanso mtsogoleri wa gulu lankhondo.+ Ndiyeno Yefita ananena mawu ake onse pamaso pa Yehova+ ku Mizipa.+ 12  Kenako Yefita anatumiza mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni+ kuti: “Ndili nanu chiyani inu,+ kuti mubwere kudzamenyana nane m’dziko langa?” 13  Ndiyeno mfumu ya ana a Amoni inauza amithenga a Yefita kuti: “N’chifukwa chakuti Aisiraeli analanda dziko langa atatuluka mu Iguputo.+ Analanda dzikoli kuyambira ku Arinoni+ mpaka ku Yaboki ndi kukafikanso ku Yorodano.+ Tsopano undibwezere dzikoli mwamtendere.” 14  Koma Yefita anatumizanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni 15  ndipo anaiuza kuti: “Yefita wanena kuti, ‘Aisiraeli sanatenge dziko la Mowabu+ ndi dziko la ana a Amoni.+ 16  Chifukwa Aisiraeli atatuluka mu Iguputo anayenda kudutsa m’chipululu kukafika ku Nyanja Yofiira+ mpaka ku Kadesi.+ 17  Kenako anatumiza mithenga kwa mfumu ya Edomu+ kuti: “Tiloleni tidutse m’dziko lanu,” koma mfumu ya Edomu sinamvere. Anatumizanso mithenga kwa mfumu ya Mowabu,+ koma nayonso sinavomereze. Choncho Aisiraeli anapitiriza kukhala ku Kadesi.+ 18  Pamene anali kudutsa m’chipululu, anayenda molambalala dziko la Edomu+ ndi dziko la Mowabu, moti anadutsa chakum’mawa kwa dziko la Mowabu+ ndi kukamanga misasa m’chigawo cha Arinoni. Iwo sanadutse malire a Mowabu,+ chifukwa Arinoni ndiye anali malire a Mowabu.+ 19  “‘Kenako Aisiraeli anatumiza mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ya ku Hesiboni,+ kuti: “Tiloleni tidutse m’dziko lanu kupita kumalo athu.”+ 20  Koma Sihoni sanakhulupirire kuti Aisiraeli akufuna kungodutsa m’dziko lake. Choncho Sihoni anasonkhanitsa anthu ake onse pamodzi ndi kumanga misasa ku Yahazi+ n’kuyamba kumenyana ndi Aisiraeliwo.+ 21  Pamenepo Yehova Mulungu wa Aisiraeli anapereka Sihoni ndi anthu ake onse m’manja mwa Aisiraeli. Choncho anawagonjetsa ndi kutenga dziko lonse la Aamori okhala kumeneko.+ 22  Motero anatenga chigawo cha Aamori kuchokera ku Arinoni kukafika ku Yaboki ndiponso kuchokera kuchipululu kukafika ku Yorodano.+ 23  “‘Choncho ndi Yehova Mulungu wa Aisiraeli amene anagonjetsa Aamori pamaso pa anthu ake Aisiraeli,+ ndipo iwe ukufuna kuwagonjetsa. 24  Kodi aliyense amene mulungu wako Kemosi+ wakuchititsa kuti umugonjetse, si amene udzam’gonjetsa? Chotero aliyense amene Yehova Mulungu wathu wam’gonjetsa pamaso pathu ndi amenenso ife tidzam’gonjetsa.+ 25  Tsopano kodi iweyo wasiyana pati ndi Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu?+ Kodi iye anakwanitsa kulimbana ndi Isiraeli, kapena kuyesa kumenyana naye? 26  Pamene Aisiraeli anali kukhala ku Hesiboni ndi m’midzi yake yozungulira,+ ku Aroweli+ ndi m’midzi yake yozungulira ndi m’mizinda yonse ya m’gombe la Arinoni kwa zaka 300, n’chifukwa chiyani simunawalande mizindayo pa nthawi imeneyo?+ 27  Ndipotu ine sindinakuchimwire, koma iwe ukundilakwira pomenyana nane. Yehova amene ndi Woweruza,+ aweruze lero pakati pa ana a Isiraeli ndi ana a Amoni.’” 28  Koma mfumu ya ana a Amoni siinamvere mawu amene Yefita anaitumizira.+ 29  Tsopano mzimu wa Yehova unabwera pa Yefita+ ndipo anadutsa m’dera la Giliyadi, m’dera la Manase, ndi m’dera la Mizipe wa ku Giliyadi.+ Atadutsa m’dera la Mizipe wa ku Giliyadi anafika kwa ana a Amoni. 30  Ndiyeno Yefita analonjeza+ Yehova kuti: “Ngati mudzaperekadi ana a Amoni m’manja mwanga, 31  ine ndidzapereka kwa Yehova+ aliyense amene adzatuluka m’nyumba yanga kudzandichingamira pamene ndikubwera mwamtendere+ kuchokera kwa ana a Amoni. Ndidzam’pereka monga nsembe yopsereza.”+ 32  Zitatero Yefita anapita kwa ana a Amoni kukamenyana nawo ndipo Yehova anawapereka m’manja mwake. 33  Iye anakantha ana a Amoni kuyambira ku Aroweli mpaka kukafika ku Miniti,+ mizinda 20. Anawakantha koopsa mpaka kukafika ku Abele-kerami. Choncho ana a Amoni anagonja pamaso pa ana a Isiraeli. 34  Kenako Yefita anabwerera kwawo ku Mizipa.+ Atafika kumeneko anaona mwana wake wamkazi akubwera kudzam’chingamira, akuimba maseche ndi kuvina.+ Iye anali mwana yekhayo amene anali naye. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. 35  Atangomuona, anayamba kung’amba zovala zake+ ndi kunena kuti: “Kalanga ine mwana wanga! Wandiweramitsa ndi chisoni ndipo ine ndikukupitikitsa. Ndatsegula pakamwa panga pamaso pa Yehova, ndipo sindingathe kubweza mawu anga.”+ 36  Koma iye anati: “Bambo, ngati mwatsegula pakamwa panu pamaso pa Yehova, ndichitireni mogwirizana ndi zimene zatuluka pakamwa panu,+ chifukwa Yehova wakugwirirani ntchito yobwezera adani anu, ana a Amoni.” 37  Ndiyeno anapitiriza kuuza bambo akewo kuti: “Lolani izi zichitike kwa ine: Mundilole ndichoke kwa miyezi iwiri, ine pamodzi ndi atsikana anzanga, ndipite kumapiri, kukalirira unamwali wanga.”+ 38  Pamenepo Yefita anati: “Pita!” Choncho anamulola kupita kwa miyezi iwiri. Ndiyeno iye pamodzi ndi atsikana anzake anapita kumapiri, kukalirira unamwali wake. 39  Ndiyeno miyezi iwiri itatha anabwerera kwa bambo ake. Pamenepo bambo akewo anakwaniritsa lonjezo lawo pa iye.+ Ndipo mtsikanayo sanagonepo ndi mwamuna. Chotero mu Isiraeli munakhala chizolowezi chakuti, 40  chaka ndi chaka ana aakazi a mu Isiraeli anali kupita kukayamikira mwana wamkazi wa Yefita wa ku Giliyadi, maulendo anayi pa chaka.+

Mawu a M'munsi