Kalata Yaciwili ya Petulo 3:1-18
3 Okondedwa, iyi tsopano ndi kalata yanga yaciwili imene ndikukulembelani, ndipo mofanana ndi kalata yanga yoyamba, apanso ndikukulimbikitsani kuti muzigwilitsa nchito bwino luso lanu la kuganiza. Ndikutelo mwa kukukumbutsani zimene mukuzidziwa kale.
2 Ndikucita izi kuti mukumbukile mau amene aneneli oyela anakamba kale-kale,* ndi lamulo limene Ambuye komanso Mpulumutsi wathu anapeleka kupitila mwa atumwi.*
3 Coyamba dziwani izi, m’masiku otsiliza kudzakhala anthu onyoza amene azidzanyoza zinthu zabwino. Potsatila zilakolako zao,
4 iwo azidzakamba kuti: “Kodi kukhalapo* kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti? Taonani, kungocokela pamene makolo athu anagona mu imfa, zinthu zonse zikupitiliza kucitika ndendende ngati mmene zakhala zikucitikila kuyambila paciyambi ca cilengedwe.”
5 Anthuwa amanyalanyaza mwadala mfundo yakuti, kale-kale panali kumwamba ndi dziko lapansi limene linatuluka pamadzi ndipo linakhazikika pakati pa madziwo mwa mau a Mulungu.
6 Ndipo kudzela m’zinthu zimenezi, dziko la pa nthawiyo linaonongedwa pamene linamila m’madzi a cigumula.
7 Koma ndi mau a Mulungu omwewo, kumwamba ndi dziko lapansi zimene zilipo panopa azisungila moto, ndipo akuzisungabe mpaka pa tsiku laciweluzo komanso loononga anthu osaopa Mulungu.
8 Komabe okondedwa, musaiwale mfundo yakuti, kwa Yehova* tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi.
9 Yehova* sakucedwa kukwanilitsa lonjezo lake, ngati mmene anthu ena amaonela kuti akucedwa. Koma akuleza nanu mtima cifukwa sakufuna kuti munthu aliyense akaonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.
10 Komabe, tsiku la Yehova* lidzafika ngati kawalala, pamene kumwamba kudzacoka ndi mkokomo waukulu. Zinthu zidzatentha kwambili n’kusungunuka, ndipo dziko lapansi ndi nchito zake zidzaonekela poyela.
11 Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka motelo, ganizilani za mtundu wa anthu amene muyenela kukhala. Muyenela kukhala anthu oyela m’makhalidwe anu, ndipo muzicita nchito zoonetsa kuti ndinu odzipeleka kwa Mulungu,
12 pamene mukuyembekezela komanso kukumbukila* nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.* Pa tsikulo kumwamba kudzapsya ndi moto n’kuonongekelatu, ndipo zinthu zidzatentha kwambili n’kusungunuka.
13 Koma pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezela malinga ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala cilungamo.
14 Conco okondedwa, popeza mukuyembekezela zinthu zimenezi, citani khama kuti Mulungu akakupezeni opanda mawanga, opanda cilema, komanso muli mumtendele.
15 Cinanso, muziona kuti kuleza mtima kwa Ambuye wathu ndi cipulumutso, monga mmenenso m’bale wathu wokondedwa Paulo anakulembelani, malinga ndi nzelu zimene anapatsidwa.
16 Iye anafotokoza zimenezi ngati mmene amacitila m’makalata ake onse. Komabe m’makalata akewo muli zinthu zina zobvuta kuzimvetsetsa, zimene mbuli ndiponso anthu acikhulupililo cosalimba amapotoza, monga mmene amacitilanso ndi Malemba ena, ndipo kucita zimenezi kudzawaonongetsa.
17 Conco inu okondedwa, popeza mwadziwilatu zimenezi, cenjelani kuti musatengeke nao limodzi anthu amenewo cifukwa ca zolakwa za anthu ophwanya malamulo mpaka inu kugwedezeka n’kugwelatu.
18 Musatelo ai, koma muzicita zinthu zimene zingakuthandizeni kuti mupitilize kulandila cisomo ca Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, ndiponso kuti mumudziwe bwino kwambili. Kwa iye kukhale ulemelelo kuyambila panopa mpaka muyaya. Ameni.
Mau a m'Munsi
^ Kapena kuti, “aneneli oyela anakambilatu.”
^ Kucokela ku Cigiriki, “mwa atumwi anu.”
^ Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “kufunitsitsa.”
^ Onani Zakumapeto A5.

