Kalata Yaciwili ya Petulo 1:1-21
1 Ndine Simoni Petulo, kapolo komanso mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulembela anthu amene apeza cikhulupililo camtengo wapatali cofanana ndi cathu kudzela m’cilungamo ca Mulungu wathu komanso ca Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.
2 Cisomo ndi mtendele zionjezeke kwa inu pokhala ndi cidziwitso colondola ca Mulungu komanso ca Yesu Ambuye wathu.
3 Mwa mphamvu zake, Mulungu watipatsa kwaulele zonse zofunikila kuti tikhale ndi moyo, komanso kuti tikhale odzipeleka kwa iye pokhala ndi cidziwitso colondola cokhudza Mulungu, amene anatiitana kudzela mu ulemelelo ndi ubwino wake.
4 Kudzela m’zinthu zimenezi, iye watipatsa malonjezo amtengo wapatali komanso odalilika kwambili, kuti mwa malonjezo amenewa, mukhale ndi ulemelelo umene Mulungu ali nao. Watelo cifukwa tinasiya kucita makhalidwe oipa am’dzikoli amene amabwela cifukwa colakalaka zinthu zoipa.
5 Cifukwa ca zimenezi, yesetsani mwakhama kuti pa cikhulupililo canu muonjezelepo ubwino, pa ubwino muonjezelepo cidziwitso,
6 pa cidziwitso kudziletsa, pa kudziletsa kupilila, pa kupilila kudzipeleka kwa Mulungu,
7 pa kudzipeleka kwa Mulungu cikondi ca pa abale, ndipo pa cikondi ca pa abale, muonjezelepo cikondi.
8 Ngati zinthu zimenezi zili mwa inu ndipo n’zosefukila, zidzakuthandizani kuti musakhale ozilala kapena osabala zipatso pa nkhani yomudziwa molondola Ambuye wathu Yesu Khristu.
9 Munthu amene alibe makhalidwe amenewa ndi wakhungu, watseka maso ake kuti asaone kuwala, ndipo waiwala kuti anayeletsedwa ku macimo omwe anali kucita kale-kale.
10 Conco abale, citani khama kwambili ndi kutsimikizila kuti ndinu okhulupilika, kuti musakaphonye mwai wokhala pakati pa anthu amene Mulungu anawaitana ndi kuwasankha. Mukapitiliza kucita zimenezi, simudzalephela ngakhale pang’ono.
11 Ndipo mwakutelo, adzakupatsani ufulu wonse waulemelelo mu Ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.
12 Pa cifukwa cimeneci, ndikufuna kuti ndizikukumbutsani zinthu zimenezi nthawi zonse, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu ozika mizu m’coonadi cimene cili mwa inu.
13 Conco ndikuona kuti ndi bwino kuti ndizikukumbutsa zinthu zimenezi pamene ndikali mu tenti* yangayi,
14 podziwa kuti tenti yangayi yatsala pang’ono kupasulidwa monga mmene Ambuye wathu Yesu Khristu anandiuzila.
15 Nthawi zonse ndiziyesetsa kukukumbutsani kuti ndikacoka muzitha kukumbukila* nokha zinthu zimenezi.
16 Pokudziwitsani za mphamvu za Ambuye wathu Yesu Khristu komanso za kukhalapo* kwake, sitinasimbe nkhani zabodza zimene anthu amapeka mocenjela. Koma tinakuuzani za ulemelelo wake umene tinacita kuuona ndi maso athu.
17 Pakuti iye analandila ulemu ndi ulemelelo kucokela kwa Mulungu Atate, pomwe mau anamveka kucokela mu ulemelelo waukulu kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.”
18 Inde, tinamva mau amenewa kucokela kumwamba pamene tinali naye limodzi m’phili loyela.
19 Conco, mau aulosi akhala odalilika kwambili, ndipo mukucita bwino kumawayang’anitsitsa ngati nyale imene ikuwala mu mdima (mpaka mbandakuca, nthanda* itatuluka) m’mitima yanu.
20 Inu mukuidziwa bwino mfundo yakuti, palibe ulosi wa m’Malemba umene umacokela m’maganizo a munthu.
21 Pakuti ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mau ocokela kwa Mulungu motsogoleledwa* ndi mzimu woyela.
Mau a m'Munsi
^ Kapena kuti, “mu tenti langali,” kutanthauza thupi lake la padziko lapansi. Mauwa amatanthauza malo amene munthu akukhala mongoyembekezela, ndipo Petulo anawagwilitsa nchito mophiphilitsa ponena za thupi lake.
^ Kapena kuti, “kuchula.”
^ Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ “Nthanda” ndi nyenyezi yomalizila kutuluka imene imaonekela dzuwa likangotsala pang’ono kutuluka.
^ Kucokela ku Cigiriki, “motengedwa, mokankhidwa.”

