Kalata Yaciwili ya Petulo 2:1-22

  • Aphunzitsi abodza adzaonekela (1-3)

  • Aphunzitsi onyenga sadzalephela kuweluzidwa (4-10a)

    • Angelo anaponyedwa mu Tatarasi (4)

    • Cigumula; Sodomu ndi Gomora (5-7)

  • Mmene tingadziwile aphunzitsi onyenga (10b-22)

2  Komabe pakati pa anthuwo, panali aneneli onyenga, monga mmene pakati panu padzakhalilanso aphunzitsi onyenga. Anthu amenewa adzayambitsa mwacinsinsi timagulu toononga tampatuko, ndipo adzakana ngakhale Ambuye wao amene anawagula. Pocita zimenezi, iwo adzadzibweletsela okha cionongeko camwamsanga. 2  Kuonjezela pamenepo, ambili adzatengela khalidwe lopanda manyazi* la aphunzitsi onyengawo. Ndipo cifukwa ca iwo anthu adzayamba kulankhula monyoza njila ya coonadi. 3  Komanso cifukwa ca dyela, adzagwilitsa nchito mau acinyengo, kuti akudyeleni masuku pamutu. Koma cilango cao cimene Mulungu anakonza kalelo kuti adzawapatse cikubwela mofulumila, ndipo cionongeko cao cidzafika ndithu. 4  Paja Mulungu sanalekelele angelo amene anacimwa aja osawapatsa cilango. Koma anawaponya mu Tatalasi,* anawamanga mumdima wandiweyani poyembekezela ciweluzo. 5  Ndipo Mulungu sanalekelele dziko lakale lija osalipatsa cilango, koma anapulumutsa Nowa mlaliki wacilungamo, limodzi ndi anthu enanso 7, pamene anabweletsa cigumula padziko la anthu osaopa Mulungu. 6  Anaononganso mizinda ya Sodomu ndi Gomora, mwa kuinyeketsa ndi moto. Anatelo kuti likhale cenjezo kwa anthu osaopa Mulungu, pa zimene zidzawacitikila m’tsogolo. 7  Koma anapulumutsa munthu wolungama Loti, amene anali kubvutika kwambili mumtima cifukwa ca khalidwe lopanda manyazi* limene anthu ophwanya malamulo anali kucita. 8  Tsiku ndi tsiku, munthu wolungamayu anali kubvutika kwambili mumtima cifukwa ca zoipa zimene anali kuona ndi kumva pakati pa anthu oipawo osamvela malamulo. 9  Conco zimenezi zikuonetsa kuti Yehova* amadziwa kupulumutsa anthu amene ndi odzipeleka kwa iye akakhala pa mayeselo. Koma anthu osalungama amawasungila tsiku la ciweluzo kuti adzawaononge, 10  maka-maka anthu amene amafuna-funa kuipitsa matupi a anthu ena, ndiponso amene amanyoza ulamulilo. Anthu amenewa saopa ciliconse komanso amamva zao zokha. Iwo sacita mantha kulankhula monyoza aja amene ali ndi ulemelelo. 11  Koma ngakhale kuti angelo ndi amphamvu komanso anyonga kwambili, saneneza aphunzitsi onyengawo ndi mau onyoza, cifukwa angelowo amalemekeza Yehova.* 12  Ndipo anthu amenewa amalankhula monyoza za zinthu zimene sakuzidziwa. Iwo ali ngati nyama zomwe ndi zopanda nzelu zimene zimangocita zinthu mwacibadwa, komanso zimabadwa kuti zigwidwe ndi kuonongedwa. Anthu amenewa adzaonongedwa cifukwa ca njila zao zoipa, 13  ndipo akukumana ndi mabvuto monga mphoto ya njila zao zoipa. Iwo amaona kuti kudyelela moyo ngakhale masana, n’kosangalatsa. Anthuwa ndi mawanga ndipo ndi litsilo lothimbilila pakati panu. Akakhala nanu pamadyelelo, amakonda kusoceletsa anzao ndi ziphunzitso zonyenga. 14  Maso ao ndi odzala ndi cigololo komanso amalephela kupewa chimo. Ndipo amakopa anthu acikhulupililo cosalimba. Ali ndi mtima wophunzitsidwa dyela. Iwo ndi ana otembeleledwa. 15  Ndi osocela cifukwa anasiya njila yoongoka. Atsatila njila ya Balamu mwana wa Beoli, amene anakonda mphoto ya nchito zoipa, 16  koma anamudzudzula cifukwa ca kulakwa kwake. Bulu amene sakamba anakamba ngati munthu, n’kulepheletsa mneneliyo kucita zamisala. 17  Amenewa ndi akasupe opanda madzi ndipo ndi nkhungu yotengeka ndi mphepo yamkuntho, komanso anawasungila mdima wandiweyani. 18  Amalankhula mau odzitukumula opanda pake. Ndipo mwa kulimbikitsa zilakolako za thupi ndi khalidwe lopanda manyazi,* amanyengelela anthu amene angothawa kumene kwa anthu ocita zoipa. 19  Ngakhale kuti akuwalonjeza ufulu, eni akewo ndi akapolo a khalidwe loipa. Cifukwa ngati munthu wagonjetsa mnzake, wogonjayo amakhala kapolo wa amene wamugonjetsayo. 20  Ndithudi, ngati anapulumuka ku zodetsa za dzikoli cifukwa codziwa molondola Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, koma iwo n’kuyambanso kucita zinthu zomwe zija mpaka kugonja, makhalidwe ao amakhala oipa kwambili kuposa poyamba. 21  Zikanakhala bwino akanapanda kudziwa molondola njila ya cilungamo, kusiyana n’kuidziwa bwino-bwino kenaka n’kupatuka pa malamulo oyela omwe analandila. 22  Zimene zawacitikila, n’zimene mwambi woona uja umakamba kuti: “Galu wabwelela ku masanzi ake, ndipo nkhumba imene inasambitsidwa yapita kukakunkhulikanso m’matope.”

Mau a m'Munsi

M’Cigiriki, a·selʹgei·a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.
“Tatalasi” ndi mkhalidwe wonyozeka wofanana ndi kukhala m’ndende. Uwu ndiwo mkhalidwe umene Mulungu anaikamo angelo osamvela m’nthawi ya Nowa. Onani Matanthauzo a Mau Ena.
M’Cigiriki, a·selʹgei·a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.
M’Cigiriki, a·selʹgei·a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.