Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anauza Mulungu Zakukhosi Kwake

Anauza Mulungu Zakukhosi Kwake

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Anauza Mulungu Zakukhosi Kwake

PANTHAWI ina Hana anali kalikiliki kukonzekera ulendo ndipo zimenezi zinathandiza kuti aiwaleko mavuto ake. Ulendowu unali wosangalatsa kwambiri. Chaka chilichonse, mwamuna wake Elikana ankakonda kupita ndi banja lake lonse kukalambira kuchihema ku Silo. Yehova ankafuna kuti zochitika zimenezi zizikhala zosangalatsa. (Deuteronomo 16:15) Ndipo ziyenera kuti Hana kuyambira ali mwana wamng’ono ankasangalala kukachita nawo misonkhano imeneyi. Koma zinthu pamoyo wake zinali zisakuyenda bwino.

Hana anali ndi mwayi kuti anali ndi mwamuna yemwe ankamukonda kwambiri. Koma ngakhale kuti zinthu zinali choncho, Elikana analinso ndi mkazi wina, dzina lake Penina. Zikuoneka kuti mkazi ameneyu ankachita zilizonse zimene angathe kuti azisowetsa Hana mtendere. Penina anapeza njira yomupweteketsera mtima Hana, ngakhale pazochitika zapadera zapachaka zimenezi. Kodi ankachita bwanji zimenezi? Ndipo funso lofunika kwambiri ndi lakuti, kodi kukhulupirira Yehova kunamuthandiza bwanji Hana kupirira mavuto amene anali kuoneka ngati ovuta kuwapirira? Ngati nanunso mukukumana ndi mavuto amene amakuchititsani kuti musasangalale ndi moyo, nkhani ya Hana ingakuthandizeni kwambiri.

‘Kodi N’chifukwa Chiyani Mtima Wako Ukuwawa?’

Baibulo limasonyeza kuti Hana anali ndi mavuto aakulu awiri. Panali zochepa zimene akanachita ndi vuto loyambalo, koma pa vuto lachiwirilo, panalibiretu zimene akanachita. Vuto loyamba linali lakuti Hana anakwatiwa ndi mwamuna wamitala, ndipo mkazi mnzake ankadana naye. Vuto lachiwiri linali lakuti iye anali wosabereka. Zimenezi zimakhala zokhumudwitsa kwa mkazi amene akufuna kukhala ndi ana. Ndipo m’nthawi ya Hana komanso malinga ndi chikhalidwe cha kwawoko, kukhala wosabereka kunali chinthu chopweteka kwabasi. Banja lililonse linkafuna kukhala ndi ana kuti dzina la banjalo lisafe. Kukhala wosabereka kunali kochititsa manyazi komanso kunkachititsa kuti munthu azinyozedwa kwambiri.

N’kutheka kuti Hana akanapirira vuto lakelo zikanakhala kuti Penina sankamuvutitsa. Mitala siyabwino chifukwa kawirikawiri m’banja lamitala mumakhala kudana, kukangana, ndi kupweteketsana mtima. Poyambirira, Mulungu anayambitsa banja la mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi. Choncho, mitala inali yosiyana kwambiri ndi zimene Mulungu anayambitsa m’munda wa Edeni. * (Genesis 2:24) Baibulo limasonyeza kuti mitala siyabwino, ndipo nkhani yokhudza zimene zinkachitika m’banja la Elikana ndi umboni wabwino kwambiri wa zimenezi.

Elikana ankamukonda kwambiri Hana. Ayuda amakhulupirira kuti Hana anali mkazi woyamba ndipo patapita zaka m’pamene Elikana anakwatira Penina. Mulimonse mmene zinalili, mfundo ndi yakuti Penina ankamuchitira nsanje kwambiri Hana, ndipo anali ndi njira zambiri zoti mnzakeyo azisowa mtendere. Nkhani yobereka ndi imene Penina ankakonda kumunyozera nayo Hana. Penina atabereka ana ambiri m’pamenenso ankadziona kuti ndi wapamwamba kwambiri. M’malo momumvera chisoni mkazi mnzakeyo chifukwa anali wosabereka, Penina anapezerapo mwayi wosowetsa Hana mtendere. Baibulo limanena kuti Penina ankavutitsa Hana kwambiri pofuna kuti “amuwawitse mtima.” (1 Samueli 1:6) Ndipo Penina ankachita dala zimenezi. Cholinga chake chinali kum’pweteketsa mtima Hana ndipo ndi zimene zinachitikadi.

Zikuoneka kuti nthawi imene Penina ankakonda kuvutitsa Hana, inali nthawi yopita ku Silo chaka chilichonse. Elikana ankapatsa ‘ana onse a Penina, aamuna ndi aakazi,’ omwe anali ambiri, magawo a nsembe zoperekedwa kwa Yehova. Koma Hana yemwe anali wosabereka, ankangom’patsa zake zokha basi. Penina ankachita zonyada kwambiri kwa Hana ndipo zimenezi zinkamukumbutsa vuto lake losabereka. Chifukwa cha zimenezi Hana anakhumudwa kwambiri moti ankangolira ndipo sankadya chakudya. Elikana anazindikira kuti Hana mkazi wake wokondedwa wakhumudwa ndipo sakudya. Choncho anayesetsa kuti amulimbikitse. Iye anamufunsa kuti: “Hana, umaliriranji? Ndipo umakaniranji kudya? Ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindili wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?”​—1 Samueli 1:4-8.

Elikana anazindikira kuti Hana ndi wokhumudwa chifukwa chakuti ndi wosabereka. Hana ayenera kuti anasangalala kuona kuti mwamuna wake amamukonda. * Koma Elikana sananene chilichonse chokhudza zoipa zimene Penina anali kumuchitira Hana, ndipo nkhaniyo siisonyeza kuti Hana anauza Elikana zoipa zimene Penina anali kumuchitira. Mwina Hana anaona kuti kumunenera Penina kukanangowonjezera mavuto ake. Koma kodi Elikana akanathetsa nkhaniyi? Kodi Hana akanamunenera Penina sizikanachititsa kuti Peninayo azidana kwambiri ndi Hana? Ndipo kodi zimenezi sizikanachititsa kuti ana ndiponso antchito a Penina azidana nayenso kwambiri? Zimenezi zikanapangitsa Hana kuti azingokhala ngati mlendo panyumba pake pomwe.

Kaya Elikana ankadziwa zonse zimene Penina ankachitira Hana kapena ayi, Yehova Mulungu ankaona zonsezo. Mawu ake amafotokoza nkhani yonse ndipo zimenezi ndi chenjezo kwa onse amene amachitira ena nsanje ndi zinthu zina zoipa zooneka ngati zazing’ono. Komanso, mofanana ndi Hana, anthu osalakwa ndiponso okonda mtendere amalimbikitsidwa podziwa kuti Mulungu yemwe ndi wachilungamo, amathetsa mavuto panthawi imene iye wasankha komanso m’njira imene iye waona kuti ndi yoyenera. (Deuteronomo 32:4) Hana ayenera kuti ankadziwa bwino zimenezi, chifukwa anapempha Yehova kuti amuthandize.

Sanakhalenso Wachisoni’

M’mamawa tsiku la ulendoli, banja lonse la Elikana, ndi ana omwe, linali pakalikiliki kukonzekera ulendo. Banjali limene linali lalikulu linali kukonzekera kuyenda ulendo wa makilomita oposa 30 wopita ku Silo, kudutsa m’mapiri a ku Efraimu. * Kwa munthu woyenda pansi, ulendowu unali wa tsiku limodzi kapena masiku awiri. Hana ankadziwa kuti mkazi mnzakeyo azimunyoza pa ulendowo, koma Hana anapitabe. Choncho, iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu olambira Mulungu masiku ano. Si bwino kuti khalidwe loipa la anthu ena litilepheretse kulambira Mulungu. Ngati titasiya kulambira Mulungu, ndiye kuti sitingalandire madalitso amene angatithandize kupirira mavuto.

Atayenda ulendo wautali wodutsa m’mapiri, iwo anatsala pang’ono kufika ku Silo, ndipo anauona mzindawo, womwe unali paphiri lozunguliridwa ndi mapiri ena akuluakulu. Akuyandikira, Hana ayenera kuti ankaganizira kwambiri zimene anakonzekera kukamuuza Yehova. Banjali litafika kumeneko, linayamba ladya chakudya. Kenako Hana anachokapo pagululo n’kukalowa kuchihema cha Yehova. Eli, yemwe anali Mkulu wa Ansembe, anali komweko, ndipo anakhala pafupi ndi khomo la kachisi. Koma Hana ankaganizira za Mulungu wake basi. Iye anadziwa kuti kuchihemako Mulungu akamva pemphero lake. Iye ankadziwa kuti mwina palibe amene ankamvetsa mavuto amene anali nawo, koma ankadziwa kuti Atate wake wakumwamba ankamvetsa. Pamenepa chisoni chake chinakula ndipo anayamba kulira.

Hana anayamba kulankhula ndi Yehova cha mumtima, uku akusisima. Milomo yake imanjenjemera pofotokoza mavuto ake. Iye anapemphera kwa nthawi yaitali, kuuza Atate wake wakumwamba zakukhosi kwake. Koma sikuti iye anangouza Mulungu kuti akufunitsitsa atakhala ndi mwana. Hana ankafunitsitsa kuti Mulungu amudalitse. Komanso iyeyo anali wokonzeka kupatsa Mulungu chilichonse. Choncho Hana analonjeza Mulungu kuti akadzabereka mwana wamwamuna, adzamupereka kuti akatumikire Yehova kukachisi.​—1 Samueli 1:9-11.

Pamenepa Hana anapereka chitsanzo chabwino kwa atumiki onse a Mulungu pa nkhani ya pemphero. Yehova amafuna kuti atumiki ake azipemphera kwa iye momasuka, osakayikira chilichonse. Iye amafuna kuti anthu azimuuza mavuto awo onse monga mmene mwana amachitira popempha chinthu kwa kholo lake limene limamukonda. (Salmo 62:8; 1 Atesalonika 5:17) Mtumwi Petulo anauziridwa kulemba mawu olimbikitsa otsatirawa okhudza mapemphero athu kwa Yehova: ‘M’tulireni nkhawa zanu zonse, pakuti amasamala za inu.’​—1 Petulo 5:7.

Yehova amamva chisoni kuposa mmene anthu amachitira. Hana akulira popemphera, anamva munthu akulankhula. Munthuyo anali Eli, mkulu wa ansembe, yemwe amaona zimene Hana amachita. Iye anati: “Udzaleka liti kuledzera? Chotsa vinyo wako.” Eli anali ataona kuti milomo ya Hana ikunjenjemera, akusisima ndiponso amaoneka kuti akuvutika kwambiri maganizo. M’malo momufunsa kuti watani, anangofikira kumunena kuti waledzera.​—1 Samueli 1:12-14.

Hana ayenera kuti zimenezi zinamuwawa kwambiri, poona kuti nthawi imene amavutika maganizo choncho, munthu wina, wa udindo wake, anangofikira kumunena zinthu zopanda umboni. Pamenepanso, Hana anasonyeza chitsanzo chabwino cha chikhulupiriro. Iye sanalole kuti aleke kulambira Yehova chifukwa chakuti munthu wina wamulakwira. Iye anamuyankha Eli mwaulemu ndipo anamufotokozera vuto lake. Eli anayankha, mwina momva chisoni, kuti: “Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israyeli akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye.”​—1 Samueli 1:15-17.

Kodi zinthu zinamuyendera bwanji Hana atauza Yehova zakukhosi kwake ndi kumulambira kuchihema? Baibulo limati: “Mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni.” (1 Samueli 1:18) Hana atauza Yehova nkhawa zake anapeza mtendere mumtima. Zinali ngati ananyamula katundu wolemera, ndiyeno watulira Atate wakumwamba amene ndi wamphamvu kwambiri kuposa iye. (Salmo 55:22) Kodi pali vuto limene Mulungu angalephere kulisenza? Ayi, palibe ngakhale limodzi.

Tikaona kuti mavuto atikulira, tifunika kutsatira chitsanzo cha Hana. Tiyenera kulankhula momasuka kwa Mulungu amene Baibulo limamutchula kuti “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Tikamapemphera kwa Mulungu tili ndi chikhulupiriro, nafenso tidzaona kuti nkhawa zathu zatha ndipo tapeza “mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira.”​—Afilipi 4:6, 7.

“Palibenso Thanthwe Longa Mulungu Wathu”

M’mawa mwake, Hana anapitanso kuchihema pamodzi ndi Elikana. Hana ayenera kuti anamuuza mwamuna wake Elikana za zimene anapempha komanso zimene analonjeza Mulungu. Mwina iye anachita zimenezi chifukwa Chilamulo cha Mose chinkanena kuti mwamuna anali ndi ufulu wofafaniza lonjezo la mkazi wake, ngati mkaziyo walonjeza Mulungu zinthu zinazake asanapemphe mwamuna wake. (Numeri 30:10-15) Koma mwamuna wokhulupirika ameneyu sanachite zimenezo. M’malomwake, iyeyo ndi Hana analambira Yehova limodzi kuchihema asananyamuke ulendo wobwerera kwawo.

Kodi Penina anazindikira liti kuti Hana sakukhumudwanso ndi zimene iye amamuchitira? Baibulo silinena, koma mawu akuti ‘sanakhalenso wachisoni’ amasonyeza kuti atangopemphera, Hana anakhalanso munthu wosangalala. Mulimonse mmene zinalili, Penina posakhalitsa anazindikira kuti zochita zake zofuna kukwiyitsa Hana sizikugwiranso ntchito. Kuyambira pamenepa Baibulo silitchulanso dzina la Penina.

Pamene miyezi inali kupita, Hana anayamba kuonekeratu kuti ali ndi mtendere wamaganizo chifukwa anali ndi pakati. Ngakhale kuti anali wosangalala, Hana sanaiwale m’pang’ono pomwe kumene madalitso amenewo anachokera. Mwanayo atabadwa, anamupatsa dzina lakuti Samueli, limene limatanthauza kuti “Dzina la Mulungu.” Zikuoneka kuti anamupatsa dzina limeneli chifukwa chakuti Hana anapempha Mulungu. Samueli atabadwa, Hana sanapite limodzi ndi Elikana komanso banja lake ku Silo kwa zaka zitatu, kufikira mwanayo atasiya kuyamwa. Kenako anayamba kukonzekera tsiku limene adzasiyane ndi mwana wake wokondedwa kwambiriyo.

Kusiyana ndi mwana wake kunali kovuta. Ndi zoona kuti Hana amadziwa kuti Samueli akasamalidwa bwino ku Silo ndi amayi ena amene anali kutumikira kuchihemako. Komabe mwanayo anali akadali wamng’ono ndipo palibe mayi amene angakonde kusiyana ndi mwana wake wamng’ono kwa zaka zambiri. Ngakhale zinali choncho, Hana ndi mwamuna wake anakapereka mwana wawoyo kuchihema mosangalala. Atafika kuchihemako, anapereka nsembe kwa Mulungu komanso anapereka Samueli kwa Eli. Pomuperekapo, iwo anakumbutsa Eli za lonjezo limene Hana analonjeza Yehova zaka zingapo zapitazo.

Kenako Hana anapemphera kwa Mulungu ndipo Mulungu anaona kuti ndi bwino kuti pempheroli likhale m’Mawu ake ouziridwa. Mukamawerenga mawu a Hana a pa 1 Samueli 2:1-10, mungathe kuona chikhulupiriro chimene anali nacho pa zonse zimene ananena. Iye anatamanda Yehova chifukwa chakuti amagwiritsa ntchito mphamvu zake modabwitsa, komanso chifukwa chotsitsa anthu odzikweza. Anatamandanso Yehova chifukwa chothandiza anthu oponderezedwa, komanso chifukwa cha mphamvu zake zotha kuchotsa moyo kapena kuukitsa akufa. Iye anatamanda Atate wake wakumwamba chifukwa chakuti ndi woyera mwapadera, wolungama ndiponso wokhulupirika. M’pake kuti Hana ananena kuti: “Palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ndi wodalirika kwambiri ndipo sasintha. Choncho, anthu onse oponderezedwa angathawire kwa iye ndipo adzawathandiza.

Ndithudi Samueli anali ndi mwayi kwambiri chifukwa mayi ake anali kukhulupirira kwambiri Yehova. Ngakhale kuti Samueli akukula sankawaona pafupipafupi mayi ake, iye sankaona kuti amuiwala. Chaka chilichonse, Hana ankapita ku Silo atatenga chovala chimene anasokera Samueli choti azikavala potumikira kuchihema. Zimenezi zinkasonyeza kuti Hana anali kumukonda kwambiri mwana wakeyo. (1 Samueli 2:19) Tingathe kumuona Hana m’maganizo mwathu akuveka mwana wakeyo chovala chatsopanocho, kuchiwongolawongola, n’kumamuyang’ana mosangalala, uku akumulankhula mawu olimbikitsa ndiponso osonyeza kuti amamukonda. Samueli anali ndi mwayi kukhala ndi mayi ngati amenewa. Atakula anakhala munthu wodalirika kwa makolo ake ndiponso kwa mtundu wonse wa Isiraeli.

Hana nayenso sanaiwalidwe ndi Yehova. Anamudalitsa ndipo anaberekanso ana ena asanu ndi mwamuna wake Elikana. (1 Samueli 2:21) Komabe mwina Hana anadalitsidwa kwambiri chifukwa cha ubwenzi wolimba umene anali nawo ndi Atate wake, Yehova. Chaka chilichonse, ubwenzi umenewu unkalimbiralimbira. Inunso mungakhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ngati mutatsanzira chikhulupiriro cha Hana.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Kuti mudziwe chifukwa chimene Mulungu kwakanthawi analolera anthu ake kukwatira mitala, onani nkhani yakuti, “Kodi Mulungu Amavomereza Mitala?” patsamba 30, mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2009.

^ ndime 10 Ngakhale kuti Baibulo limanena kuti Yehova ‘anatseka mimba ya Hana,’ palibe umboni wosonyeza kuti Mulungu sankasangalala ndi Hana, yemwe anali mkazi wokhulupirika komanso wodzichepetsa. (1 Samueli 1:5) Baibulo nthawi zina limanena kuti Mulungu wachititsa chinachake, koma kwenikweni amakhala kuti wangolola kuti zichitike.

^ ndime 13 Mtunda umenewu tikutengera kuti mwina kwawo kwa Elikana kunali ku Rama, komwe m’nthawi ya Yesu kunkadziwika ndi dzina lakuti Arimateya.

[Bokosi patsamba 17]

Mapemphero Awiri Ogwira Mtima

Pali zinthu zingapo zochititsa chidwi m’mapemphero awiri a Hana, olembedwa pa 1 Samueli 1:11 ndi pa 1 Samueli 2:1-10. Zina mwa zinthu zimenezo ndi izi:

▪ Hana anapemphera pemphero loyamba kwa “Yehova wa makamu.” M’Baibulo lonse, iye ndi munthu woyamba kugwidwa mawu akugwiritsa ntchito dzina laulemu limeneli. Dzinali limapezeka maulendo 252 m’Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu. Yehova amatchulidwa ndi dzina limeneli chifukwa ali ndi khamu lalikulu kwambiri la ana ake auzimu.

▪ Hana anapemphera pemphero lake lachiwiri pamene iyeyo ndi Elikana anapereka mwana wawo Samueli kuti azikatumikira Mulungu ku Silo, osati panthawi imene Samueli anabadwa. Zimenezi zikusonyeza kuti Hana anasangalala kwambiri chifukwa chakuti Yehova anamudalitsa, osati chifukwa chakuti mkazi mnzake Penina anayamba kusowa chonena poona kuti Hana wayamba kubereka.

▪ Ponena kuti, “Nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova,” Hana ayenera kuti anali kudzifanizira ndi ng’ombe, imene ndi nyama yamphamvu kwambiri imene anthu amaigwiritsa ntchito zosiyanasiyana komanso imene ndi yoopsa chifukwa cha nyanga zake. M’mawu ena, Hana amati: ‘Inu Yehova, mwandipatsa mphamvu.’​—1 Samueli 2:1.

▪ Mawu a Hana onena za “wodzozedwa” wa Mulungu anali ulosi. Mawu amenewa ndi ofanana ndi enanso akuti “mesiya,” ndipo m’Baibulo lonse, Hana ndi munthu woyamba kugwiritsa ntchito mawu amenewa ponena za mfumu yodzozedwa ya m’tsogolo.​—1 Samueli 2:10.

▪ Patapita zaka pafupifupi 1,000, Mariya, mayi ake a Yesu, anatchula ena mwa mawu a Hana pamene anali kutamanda Yehova.​—Luka 1:46-55.

[Chithunzi patsamba 16]

Hana ankavutika kwambiri mumtima chifukwa chakuti anali wosabereka, ndipo Penina ankachita chilichonse kuti Hana asowe mtendere

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Hana sanakhumudwe ngakhale kuti Eli anamuganizira zolakwa

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi mungatsanzire chitsanzo cha Hana chopemphera ndi mtima wonse?