Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Kuti Mupeze Anzanu Enieni

Zimene Mungachite Kuti Mupeze Anzanu Enieni

Zoti Achinyamata Achite

Zimene Mungachite Kuti Mupeze Anzanu Enieni

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthuwo akumvera.

Anthu a munkhaniyi: Jonatani, Davide, ndi Sauli

Mwachidule: Davide atapha Goliati, Jonatani anakhala mnzake weniweni wa Davide.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI 1 SAMUELI 17:57–18:11; 19:1; 20:1-17, 41, 42.

Kodi mukuganiza kuti Sauli ankaoneka bwanji? (Zokuthandizani: Onani 1 Samueli 10:20-23.)

․․․․․

Davide ayenera kuti anali mnyamata nthawi imene anakumana ndi Jonatani. Kodi mukuganiza kuti Davide ankaoneka bwanji? (Zokuthandizani: Onani 1 Samueli 16:12, 13.)

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Davide ndi Jonatani anamva bwanji akusiyana ndipo mawu awo ankatuluka bwanji, malinga ndi zimene zili kumapeto kwa 1 Samueli chaputala 20?

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

Nkhaniyi imanena kuti “Jonatani anam’konda [Davide] monga moyo wa iye yekha.” (1 Samueli 18:1) Baibulo lina limati, “Davide ndi Jonatani anakhala mabwenzi apamtima.” (Contemporary English Version) Kodi Davide anali ndi makhalidwe abwino ati amene anachititsa Jonatani kumukonda? (Onani 1 Samueli 17:45, 46.)

․․․․․

Jonatani anali wamkulu kwa Davide ndi zaka pafupifupi 30. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chinapangitsa kuti akhale “mabwenzi apamtima” ngakhale kuti zaka zawo zinali zosiyana kwambiri?

․․․․․

Kodi mnzanu weniweni amachita zinthu monga ziti, malinga ndi nkhani yosangalatsa imeneyi? (Zokuthandizani: Werengani Miyambo 17:17; 18:24.)

․․․․․

N’chifukwa chiyani Jonatani anali wokhulupirika kwambiri kwa Davide kuposa kwa bambo ake?

․․․․․

3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA  . . .

Anzanu.

․․․․․

Kukhulupirika.

․․․․․

Kucheza ndi anthu akuluakulu.

․․․․․

Kodi mungachite chiyani kuti mukhale ndi anzanu abwino?

․․․․․

4 KODI NDI MFUNDO ZITI M’NKHANIYI ZIMENE ZAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

NGATI MULIBE BAIBULO, MUNGAWERENGE LA PA INTANETI PA WEBUSAITI YATHU YA www.jw.org.