Pitani ku nkhani yake

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo—Amuna ndi Akazi Otchulidwa M’Baibulo

Kulengedwa kwa Zinthu Mpaka Nthawi ya Chigumula

Abele​—“Ngakhale Kuti Anafa, Iye Akulankhulabe”

Kodi tingaphunzirepo chiyani pa nkhani ya Abele, ngakhale kuti Baibulo silifotokoza zambiri zokhudza iyeyo komanso chikhulupiriro chake?

Inoki: ‘Mulungu Anakondwera Naye’

Ngati mumasamalira banja kapena zimakuvutani kuti muzichita zinthu molimba mtima, mukhoza kuphunzira zambiri pa chitsanzo cha Inoki.

Nowa—“Anayenda Ndi Mulungu Woona”

Kodi Nowa ndi mkazi wake anakumana ndi mavuto otani polera ana awo? Kodi anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro pomanga chingalawa?

Anapulumutsidwa “Pamodzi ndi Anthu Ena 7”

Kodi Nowa ndi banja lake anapulumuka bwanji chigumula chomwe chinachitika padziko lonse lapansi?

The Flood to the Exodus

Abulahamu​—“Tate wa Onse Okhala ndi Chikhulupiriro”

Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro? Kodi mukufuna kutsanzira Abulahamu m’njira ziti?

Sara: “Ndiwe Mkazi Wokongola”

Ali ku Iguputo, akalonga a Farao anaona kuti Sara anali mkazi wokongola. Ndiye kodi mukuganiza kuti zinatha bwanji?

Sara—Yehova Anamutchula Kuti “Mfumukazi”

N’chifukwa chiyani dzina latsopanoli linali lomuyenera?

Rabeka: “Inde Ndipita”

Rabeka anali ndi chikhulupiriro komanso makhalidwe ena abwino kwambiri.

“Tamverani Maloto Amene Ine Ndinalota”

Mabanja ambiri omwe muli makolo ndi ana opeza angaphunzire zambiri pa zimene zinkachitika m’banja lomwe Yosefe anakulira.

“Ndingachitirenji Choipa Chachikulu Chonchi N’kuchimwira Mulungu?”

Kodi Yosefe anatha bwanji kukana zofuna za mkazi wa Potifara zoti agone naye?

“Kodi Mulungu Sindiye Amamasulira Maloto?”

Kodi n’chiyani chinathandiza Yosefe kuti amasulire molimba mtima maloto a mkulu wa ophika mikate, a woperekera chikho komanso a mfumu ya ku Iguputo? Kodi zinatheka bwanji kuti Yosefe yemwe anali mkaidi apezeke kuti ndi wachiwiri kwa mfumu tsiku limodzi lokha?

“Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”

Ngati abale anu amakuchitirani nsanje, kukudani kapena kuchita zinthu zina zosakhulupirika, nkhani ya Yosefe ingakuthandizeni.

Yobu—“Sindidzasiya Kukhala Ndi Mtima Wosagawanika.”

Kodi nkhani ya Yobu ingatithandize bwanji tikakumana ndi mavuto kapena mayesero omwe angayese chikhulupiriro chathu?

Yobu​—Yehova Anamuchotsera Ululu

Satana amanyansidwa kwambiri akaona kuti tikukhalabe okhulupirika ngati Yobu koma Yehova amasangalala nazo kwambiri.

Aisiraeli Akuchoka ku Iguputo Mpaka Atakhala ndi Mfumu Yoyamba

‘Anaonedwa Ngati Wolungama Chifukwa cha Ntchito Zake’

Kodi nkhani ya Rahabi ikusonyeza bwanji kuti tonsefe ndife ofunika kwa Yehova? Kodi tingaphunzire chiyani pa chikhulupiriro chake?

“Ine Ndinauka Monga Mayi mu Isiraeli”

Kodi tingaphunzire chiyani zokhudza kulimba mtima komanso chikhulupiriro pa nkhani ya m’Baibulo yonena za Debora

Rute​—“Kumene Inu Mupite Inenso Ndipita Komweko”

N’chiyani chinachititsa Rute kulolera kusiyana ndi anthu a kwawo komanso dziko la kwawo? Kodi Rute anasonyeza makhalidwe abwino ati omwe anachititsa kuti Yehova azimukonda kwambiri?

Rute​—Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”

N’chifukwa chiyani tinganene kuti ukwati wa Rute ndi Boazi unali wapadera? Kodi chitsanzo cha Rute ndi Naomi chikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya banja?

Hana—Anapemphera Kuchokera Pansi pa Mtima

Hana anakwanitsa kupirira mavuto aakulu kwambiri chifukwa chakuti ankakhulupirira Yehova.

Samueli—“Anapitiriza Kukula, Akukondedwa Ndi Yehova”

N’chifukwa chiyani tinganene kuti Samueli analeredwa mwapadera? N’chiyani chinkalimbikitsa chikhulupiriro chake pamene anali kuchihema?

Samueli—Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Kuti Anakumana ndi Mavuto

Tonsefe nthawi zina timakhumudwa komanso timakumana ndi mavuto amene angasokoneze chikhulupiriro chathu. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Samueli?

Aisiraeli Atakhala ndi Mfumu Yoyamba Mpaka Pamene Yesu Anabadwa

“Palibe Chimene Chingalepheretse Yehova”

Yonatani ndi mnyamata wake anamenya nkhondo ndi gulu la adani ndipo anapambana. Zimene anachitazi n’zosaiwalika.

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

N’chiyani chinathandiza Davide kuti aphe Goliyati? Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani ya Davide?

“Anagwirizana Kwambiri”

Kodi zinatheka bwanji kuti anthu osiyana kwambiri chikhalidwe ndi msinkhu ayambe kugwirizana kwambiri? Kodi chitsanzo chawo chingatithandize bwanji kupeza anzathu abwino?

Abigayeli—Anachita Zinthu Mwanzeru

Kodi tingaphunzirepo zotani pa mavuto a banja amene Abigayeli anakumana nawo?

Eliya—Sanasunthike pa Kulambira Koona

Kodi tingatsanzire bwanji Eliya tikamalankhula ndi anthu amene amatsutsa zimene Baibulo limaphunzitsa?

Eliya—Anali Watcheru Ndiponso Anadikira

Kodi Eliya anasonyeza bwanji kuti ankakonda kupemphera pamene ankadikira Yehova kuti akwaniritse lonjezo lake?

Eliya—Analimbikitsidwa ndi Mulungu Wake

N’chiyani chinachititsa Eliya kukhumudwa mpaka kufika popempha kuti afe?

Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Kuti Ena Ankachita Zinthu Zopanda Chilungamo

Kodi inuyo munayamba mwachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo? Kodi mumafuna Mulungu atathetsa zinthu zopanda chilungamo? Werengani nkhaniyi kuti muone mmene mungatsanzirire chikhulupiriro cha Eliya.

Eliya​—Anapirira Mpaka Pamapeto

Eliya anakhalabe wokhulupirika ndipo anakwanitsa kupirira. Chitsanzo chake chingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu tikakumana ndi mavuto.

Yona—Anaphunzira pa Zolakwa Zake

Kodi mungamvetse chifukwa chake Yona ankaopa kugwira ntchito imene Mulungu anamupatsa? Nkhani ya Yona ikutiphunzitse zambiri zokhudza kuleza mtima ndiponso chifundo cha Yehova.

Yona—Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo

Kodi nkhani ya Yona ingatithandize bwanji kudzifufuza?

Esitere—Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

Kuti munthu asonyeze chikondi chololera kuvutikira ena, ayenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kukhala wolimba mtima ngati Esitere.

Esitere—Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena

Kodi Esitere anadzipereka bwanji potumikira Yehova komanso pothandiza anthu ake?

Yesu Atabadwa Mpaka Pamene Atumwi Anafa

Mariya—“Ndinetu Kapolo wa Yehova!”

Kodi zimene Mariya ananena kwa Gabirieli zimasonyeza chiyani chokhudza chikhulupiriro cha Mariya? Kodi Mariya anasonyeza makhalidwe ena ati?

Mariya—‘Anaganizira Tanthauzo la Mawu Onsewo Mumtima Mwake’

Zimene Mariya anaona ndiponso kumva ali ku Betelehemu zinamuthandiza kukhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova.

Sanafooke Chifukwa cha Chisoni

Chitsanzo cha Mariya, mayi a Yesu, chingakuthandizeni ngati mukumva chisoni kwambiri chifukwa cha imfa ya munthu wina.

Yosefe—Ankasamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika

Kodi Yosefe anateteza banja lake m’njira ziti? N’chifukwa chiyani anatenga Mariya ndi Yesu n’kupita nawo ku Iguputo?

Marita—“Ndimakhulupirira”

Kodi Marita anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro ngakhale pamene anali ndi chisoni?

Mariya Mmagadala—“Ambuye Ndawaona Ine.”

Mariya Mmagadala yemwe anali ndi chikhulupiriro cholimba, anali ophunzira woyamba kumuona Yesu ataukitsidwa. Iye anapatsidwa mwayi woti auze ena uthenga wabwinowu.

Petulo—Anathetsa Mantha Ndiponso Mtima Wokayikira

Nthawi zina kukayikira zinthu kumakhala koipa kwambiri. Koma Petulo anathetsa mantha komanso mtima wokayikira potsatira chitsanzo cha Yesu.

Petulo—Anakhalabe Wokhulupirika pa Nthawi Yovuta

Kodi chikhulupiriro cha Petulo ndiponso kukhulupirika kwake zinamuthandiza bwanji kuti atsatire uphungu umene Yesu anam’patsa?

Petulo—Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kufunika Kokhala Wokhululuka

Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani Petulo pa nkhani ya kukhululuka? Kodi Yesu anachita chiyani posonyeza kuti anakhululukira Petulo?

“Mwana Wanga Wokondedwa Ndi Wokhulupirika Mwa Ambuye”

Kodi n’chiyani chinathandiza Timoteyo kukhala Mkhristu wolimba mtima ngakhale kuti poyamba anali wamanyazi?