Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chifukwa Chiyani Yesu Sankalowerera Ndale?

Kodi N’chifukwa Chiyani Yesu Sankalowerera Ndale?

Kodi N’chifukwa Chiyani Yesu Sankalowerera Ndale?

TSIKU lina madzulo, m’chaka cha 32 C.E., Yesu anadabwitsa anthu masauzande ambiri pochita zozizwitsa komanso pophunzitsa Mawu a Mulungu. Apa n’kuti Yesu, amene anali Mesiya wolonjezedwa, atatchuka kale chifukwa chochiritsa odwala ndi kuukitsa akufa. Patsikuli, anagawa m’magulumagulu anthu amene ankamulondola, n’kupemphera kwa Yehova ndi kuwapatsa chakudya onsewo. Atatha, anatolera chakudya chotsala kuti pasawonongeke kalikonse. Kodi anthuwo ataona zimenezi anachita chiyani?​—Yohane 6:1-13.

Anthuwo ataona zozizwitsa zimene Yesu anachita, luso lake lotsogolera gulu lalikulu la anthu komanso poona kuti anawapatsa chakudya, anaganiza kuti iye angakhale mfumu yabwino kwambiri. (Yohane 6:14) Sizodabwitsa kuti anthuwo anaganiza zimenezi. Musaiwale kuti iwo ankafuna wolamulira wabwino komanso wodziwa kusamalira anthu chifukwa chakuti ankalamuliridwa ndi anthu ankhanza a dziko lina. Choncho anayamba kukakamiza Yesu kuti alowe ndale. Ndiye tiyeni tione zimene Yesu anachita.

Lemba la Yohane 6:15 limati: “Yesu atadziwa kuti iwo akufuna kum’gwira kuti amulonge ufumu, anachoka ndi kupitanso kuphiri yekhayekha.” Pamenepa Yesu anasonyezeratu kuti sakufuna kukhala mfumu. Anakaniratu kulowa ndale ndipo sanasinthe maganizo ake. Ananena kuti otsatira ake ayeneranso kuchita zomwezo. (Yohane 17:16) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anakana kulowa ndale?

Chifukwa Chake Yesu Anakana Kulowa Ndale

Yesu anakana kulowa ndale chifukwa cha zimene Malemba amanena. Nazi mfundo ziwiri zokha za m’Malemba.

“Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Izi ndi zimene Baibulo limanena pofotokoza zimene zakhala zikuchitika anthu akamalamulirana. Musaiwale kuti Yesu anakhala kumwamba nthawi yaitali asanakhale munthu padziko lapansi. (Yohane 17:5) Choncho ankadziwa kuti munthu, kaya akhale ndi zolinga zabwino chotani, sangathe kukwaniritsa bwinobwino zimene aliyense amafuna, komanso Mulungu sanalenge munthu ndi mphamvu yochita zimenezo. (Yeremiya 10:23) Yesu ankadziwa kuti si maboma a anthu amene adzathetse mavuto a anthu.

“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Kodi mawu amenewa akukudabwitsani? Anthu ambiri amadabwa akamva mawu amenewa chifukwa amaona kuti pali anthu ena abwino amene amalowa ndale n’cholinga chabwino, choti akonze zinthu ndiponso kuti dzikoli likhale labwino. Koma ngakhale olamulira abwino atayesetsa bwanji, sangapewe mphamvu ya munthu amene Yesu anamutchula kuti “wolamulira wa dzikoli.” (Yohane 12:31; 14:30) N’chifukwa chake Yesu anauza wandale wina kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Yesu ankayembekezera kukhala Wolamulira wa boma lakumwamba limene Mulungu analikhazikitsa. Yesu akanalowa ndale padziko lapansi, akanakhala wosakhulupirika ku boma la Atate wake lakumwamba.

Ndiyeno kodi Yesu anaphunzitsa kuti otsatira ake asamamvere maboma? Ayi. Iye anawaphunzitsa kumvera Mulungu komanso kumvera maboma pa zinthu zoyenera.

Yesu Ankalemekeza Boma

Panthawi ina Yesu akuphunzitsa m’kachisi, anthu omutsutsa anayesa kumukola pomufunsa ngati anthu ayenera kumakhoma misonkho. Ngati Yesu akanakana, bwenzi anthuwo akuti ndi woukira boma ndipo mwina zikanachititsa anthu amene anatopa ndi ulamuliro wankhanza wa Aroma kuti ayambe kuukira boma. Komanso Yesu akanavomera, anthu ambiri akanaganiza kuti iye akugwirizana ndi nkhanza za Aroma. Yesu anawayankha bwino kwambiri, chifukwa anati: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.” (Luka 20:21-25) Zimenezi zikusonyeza kuti otsatira ake ayenera kumvera Mulungu, komanso ayenera kumvera Kaisara, kapena kuti anthu olamulira.

Maboma amathandiza kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo. Amafuna kuti anthu akhale oona mtima, azikhoma misonkho ndiponso azimvera malamulo. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pankhani ‘yopereka kwa Kaisara za Kaisara’? Yesu analeredwa ndi makolo omvera malamulo ndipo iwo ankamvera malamulo ngakhale pamene zinali zovuta kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, Yosefe ananyamuka ndi mkazi wake Mariya ali ndi pakati, ndipo anayenda mtunda wamakilomita pafupifupi 150 kupita ku Betelehemu chifukwa chakuti boma la Roma linalamula kuti anthu abwerere kwawo kuti akachite kalembera. (Luka 2:1-5) Mofanana ndi makolo akewo, Yesu ankamvera malamulo a boma. Iye anafika pokhoma misonkho ngakhale kuti samayenera kukhoma. (Mateyo 17:24-27) Iye ankakhalanso wosamala kuti asagwiritse ntchito mphamvu zake molakwa n’kumalowerera m’nkhani zandale. (Luka 12:13, 14) Yesu ankalemekeza boma ngakhale kuti ankakana kulowa nawo ndale. Nangano, kodi Yesu ankatanthauzanji pamene ananena kuti perekani “za Mulungu kwa Mulungu”?

Mmene Yesu Anaperekera “za Mulungu kwa Mulungu”

Nthawi ina, Yesu anafunsidwa kuti atchule lamulo lalikulu kwambiri pa malamulo onse amene Mulungu anapatsa anthu. Yesu anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu koposa komanso loyamba. Lachiwiri, lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.’” (Mateyo 22:37-39) Yesu anaphunzitsa kuti tikafika pa nkhani yopereka “za Mulungu kwa Mulungu,” chinthu choyamba chimene tiyenera kupatsa Mulungu n’chikondi. Zimenezi zimaphatikizapo kumumvera ndi mtima wonse.

Kodi chikondi chimenechi tingachigawe? Kodi tingakhale okhulupirika kwa Yehova Mulungu ndi boma lake lakumwamba komanso n’kukhala wokhulupirika ku maboma a anthu? Yesu ananena kuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri; pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo.” (Mateyo 6:24) Pamenepa Yesu amanena zoti sitingakonde Mulungu ndi chuma. Mosakayikira iye amaona kuti mfundo yomweyo ikugwiranso ntchito pa nkhani yolowerera ndale. Otsatira ake oyambirira ankaonanso chimodzimodzi.

Zolembedwa zakale kwambiri zimasonyeza kuti otsatira a Yesu akalekale sankalowerera ndale. Chifukwa chakuti ankalambira Mulungu yekhayo amene Khristu ankamulambira, iwo ankakana kukonda ufumu wa Roma ndi mfumu yake, mmene angakondere Mulungu. Iwo anakananso kulowa usilikali komanso kukhala ndi udindo wandale. Chifukwa cha zimenezi, iwo anazunzidwa m’njira zosiyanasiyana. Adani awo ankanena kuti iwo amadana ndi anthu anzawo. Kodi zimenezi zinali zoona?

Akhristu Oona Amakonda Anthu Ena

Kumbukirani zimene Yesu ananena kuti ndi lamulo lalikulu kwambiri pa malamulo a Mulungu. Iye anati: “Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.” Palibe wotsatira Khristu aliyense amene ayenera kumadana ndi anthu anzake. Yesu ankakonda anthu, ankawathandiza ndipo ankawapatsanso zinthu zofunika kwambiri pa moyo.​—Maliko 5:25-34; Yohane 2:1-10.

Koma kodi Yesu ankadziwika kwambiri ndi chiyani? Anthu ankadziwa kuti Yesu anali Wochiritsa komanso Woukitsa Akufa, koma sankamudziwa ndi maina amenewa. Iwo ankamutcha kuti Mphunzitsi, ndipo mpakedi. (Yohane 1:38; 13:13) Yesu anafotokoza kuti cholinga chake chenicheni chimene anabwerera padziko lapansi chinali kuphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu.​—Luka 4:43.

N’chifukwa chake otsatira oona a Khristu amagwira mwakhama ntchito imene Mbuye wawo anagwira ali padziko lapansi, yophunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Yesu Khristu analamula Akhristu onse oona kuti aziphunzitsa anthu padziko lonse za nkhani imeneyi. (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Boma lakumwamba lopanda choipa chilichonse limeneli, lidzalamulira mwachikondi zonse zimene Mulungu analenga. Lidzakwaniritsa chifuniro cha Mulungu ndipo lidzachotsanso mavuto ndi imfa. (Mateyo 6:9, 10; Chivumbulutso 21:3, 4) N’zosadabwitsa kuti Baibulo limanena kuti zimene Yesu ankaphunzitsa ndi “uthenga wabwino.”​—Luka 8:1.

Choncho kodi mukufunitsitsa kudziwa amene ali otsatira enieni a Yesu Khristu masiku ano? Ngati mukutero, kodi mungawadziwe bwanji? Kodi mukuganiza kuti amalowerera ndale? Kapena kodi iwo akugwira ntchito yofanana ndi imene Yesu ankagwira, yolalikira ndi kuphunzitsa za Ufumu wa Mulungu?

Ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu ndi mmene ungakuthandizireni pa moyo wanu panopa, lankhulani ndi a Mboni za Yehova a kwanuko kapena mufufuze pa adiresi ya Mboni za Yehova ya pa Intaneti iyi: www.jw.org.

[Bokosi/​Zithunzi pamasamba 24, 25]

Kodi a Mboni za Yehova Amathandiza pa Nkhani Zachitukuko?

A Mboni za Yehova salowerera ndale. Komabe, iwo amayesetsa kuthandiza anthu a mitundu ndi a zikhalidwe zosiyanasiyana a m’dera lawo. Taganizirani zina zimene amachita:

▪ A Mboni za Yehova ndi gulu la anthu odzipereka oposa 7 miliyoni amene chaka chilichonse amathera maola oposa 1.5 biliyoni pophunzitsa anthu Baibulo. Iwo amathandizanso anthu mmene angaligwiritsirire ntchito Baibulo pothetsa makhalidwe awo oipa, kuti akhale ndi mabanja abwino komanso moyo wabwino.

▪ A Mboni za Yehova amasindikiza ndi kugawira mabuku kwaulere m’zilankhulo zoposa 500. Zina mwa zilankhulo zimenezi zilibenso mabuku ena koma a Mboni za Yehova okhawo basi.

▪ Iwo ali ndi pulogalamu yophunzitsa anthu kulankhula mwaluso imene yathandiza anthu mamiliyoni ambiri kudziwa kulankhula mogwira mtima komanso momveka kwa anthu osiyanasiyana.

▪ Iwo ali ndi makalasi ophunzitsa anthu kulemba ndi kuwerenga ndipo athandiza anthu masauzande ambiri padziko lonse lapansi kudziwa kulemba ndi kuwerenga.

▪ A Mboni za Yehova ali ndi magulu oposa 400 padziko lonse othandiza pa ntchito yomanga. Magulu amenewa aphunzitsa anthu odzipereka ntchito zomanga kuti athe kumanga malo ophunziriramo Baibulo. Pa zaka 10 zapitazi, iwo amanga nyumba zoposa 20,000 zolambiriramo zotchedwa Nyumba za Ufumu.

▪ Padziko lonse, a Mboni za Yehova amathandiza a Mboni anzawo komanso anthu ena amene agweredwa masoka achilengedwe. Mwachitsanzo, mvula yamkuntho itawononga nyumba zambiri ku United States pa zaka ziwiri zapitazi, a Mboni anamanganso Nyumba za Ufumu zoposa 90 komanso nyumba za anthu zokwana 5,500.

[Chithunzi patsamba 23]

Anthu atakakamiza Yesu kuti alowe ndale, iye ‘anachoka ndi kupita kuphiri yekhayekha’