Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo 7 Zimene Zingakuthandizeni Kuti Mupindule ndi Kuwerenga Baibulo

Mfundo 7 Zimene Zingakuthandizeni Kuti Mupindule ndi Kuwerenga Baibulo

Mfundo 7 Zimene Zingakuthandizeni Kuti Mupindule ndi Kuwerenga Baibulo

“Baibulo ndi buku limene lagulidwa kwambiri kuyambira kale komanso limene likugulidwabe kwambiri chaka chilichonse.”​—MAGAZINI YA TIME.

Woimba wina wotchuka wa ku England anati: “Nthawi zina ndimawerenga Baibulo, koma ndimaona kuti nkhani zake ndi zotopetsa kwabasi.”​—KEITH, WOIMBA WOTCHUKA WA KU ENGLAND.

N’ZODABWITSA kuti anthu ambiri ali ndi Baibulo koma saliwerenga chifukwa siliwasangalatsa. Ngakhale zili choncho, pali anthu ena amene amaona kuti kuwerenga Baibulo n’kofunika kwambiri. Mwachitsanzo, mayi wina, dzina lake Nancy, ananena kuti: “Kuyambira pamene ndinayamba kuwerenga Baibulo m’mawa uliwonse komanso kuganizira zimene ndawerengazo, ndimakhala wokonzeka kuthana ndi vuto lililonse limene ndingakumane nalo pa tsikulo. Matenda anga ovutika maganizo achepako chifukwa chowerenga Baibulo, kusiyana ndi zinthu zina zimene ndakhala ndikuchita kwa zaka 35 pofuna kuthana ndi matendawa.”

Ngati simunawerengepo Baibulo, kodi mumadabwa kumva kuti ena limawathandiza? Ngati mumaliwerenga, kodi mukufuna kuti lizikupindulitsani kwambiri? Ngati mukufuna kupindula nalo, yesani mfundo 7 zotsatirazi.

Mfundo 1​—Muziliwerenga ndi cholinga chabwino

▪ Mwina mumawerenga Baibulo chifukwa ndi buku labwino kapena chifukwa choti timauzidwa kuti tiziliwerenga. Mwinanso mumaliwerenga chifukwa chakuti mumafuna kuti lizikutsogolerani m’dziko lovutali. Komabe mudzapindula ngati mumaliwerenga n’cholinga choti mudziwe zoona zake za Mulungu. Komanso mudzapindula kwambiri ngati mumaliwerenga ndi cholinga choti mudziwe mmene uthenga wake ungakuthandizireni pa moyo wanu.

Malemba amayerekezera Baibulo ndi galasi lodziyang’anira ndipo zimenezi zimasonyeza kuti tiyenera kuliwerenga ndi cholinga chabwino. Baibulo limati: “Ngati munthu ali wongomva mawu, koma wosachita, ali ngati munthu wodziyang’anira nkhope yake yachibadwa pa kalilole. Pakuti amadziyang’ana yekha, koma akachokapo, nthawi yomweyo amaiwala mmene akuonekera. Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro laufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.”​—Yakobe 1:23-25.

Munthu wa m’fanizoli anadziyang’anira pagalasi koma sanadzikonze. Mwina anadziyang’ana mofulumira, kapena sanafune kudzikonza. Mofanana ndi zimenezi, Baibulo sitingapindule kwenikweni ngati timaliwerenga modumphadumpha kapena ngati sitichita zimene tawerengazo. Koma tingapindule kwambiri ngati timawerenga Baibulo ndi cholinga chakuti ‘tizichita’ zimene timawerengazo. Ndiponso tingapindule ngati timafuna kuti tiziganiza ndi kuchita zinthu ngati Mulungu.

Mfundo 2​—Muziwerenga Baibulo labwino

▪ Mwina m’chilankhulo chanu muli ndi mabaibulo ambiri oti musankhepo limene muziwerenga. Ngakhale kuti mungapindule ndi kuwerenga Mawu a Mulungu m’Baibulo lina lililonse, m’mabaibulo ena muli mawu achikale kapena ovuta kumva. (Machitidwe 4:13) Komanso mabaibulo ena amasintha uthenga wa Mawu a Mulungu chifukwa chotsatira kwambiri miyambo ya anthu. Mwachitsanzo, monga mmene taonera m’nkhani zoyambirira za m’magazini ino, anthu ena achotsa dzina la Mulungu lakuti Yehova, ndipo aikamo mayina ena omulemekezera monga “Mulungu” kapena “Ambuye.” Choncho, posankha Baibulo loti muziwerenga pezani limene linalembedwa mosavuta kumva komanso limene silingakutopetseni powerenga.

Anthu ambiri padziko lonse amaona kuti Baibulo la New World Translation ndi losavuta kuwerenga ndiponso silitopetsa. * Ganizirani za bambo wina wachikulire wa ku Bulgaria. Iye atapita ku msonkhano wa Mboni za Yehova anapatsidwa Baibulo la New World Translation. Patapita nthawi, iye anati: “Ndakhala ndikuwerenga Baibulo kwa zaka zambiri koma sindinawerengepo Baibulo losavuta kumva ndiponso limene uthenga wake ndi wogwira mtima ngati limeneli.”

Mfundo 3​—Muzipemphera

▪ Mungamvetse kwambiri Baibulo ngati mutapempha kaye Wolemba wake kuti akuthandizeni. Zimenezi ndi zimene anachita wamasalmo amene anati: “Munditsegulire maso, kuti ndipenye zodabwitsa za m’chilamulo chanu.” (Salmo 119:18) Nthawi zonse powerenga Malemba, muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni kumvetsa Mawu ake. Mukhozanso kumuthokoza pokupatsani Baibulo, chifukwa popanda Baibulo sitikanatha kumudziwa Mulungu.​—Salmo 119:62.

Kodi Mulungu amamva mapemphero otero? Taganizirani zimene zinachitikira atsikana awiri apachibale a ku Uruguay. Iwo anadabwa kwambiri ndi zimene anawerenga pa Danieli 2:44 ndipo anapempha Mulungu kuti atumize munthu kuti awathandize kumvetsa vesili. Baibulo lawo lili chitsegulire, anthu awiri a Mboni za Yehova anafika pakhomopo n’kuwerenga lemba lija, limene atsikanawo amafuna kuti alimvetse. Ndipo anafotokoza kuti lembalo likunena zoti maboma a anthu adzalowedwa m’malo ndi Ufumu wa Mulungu. * Atsikanawo sanakayike n’komwe kuti Mulungu wayankha pemphero lawo.

Mfundo 4​—Muziliwerenga tsiku lililonse

▪ Kampani ina yopanga mabuku inanena kuti, “anthu ambiri anagula mabaibulo” zigawenga zitagwetsa nyumba ku United States pa September 11, 2001. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ambiri amakonda kuwerenga Mawu a Mulungu panthawi ya mavuto. Komabe, Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziliwerenga tsiku lililonse, popeza limanena kuti: “Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.”​—Yoswa 1:8.

Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse n’kofunika. Tingakuyerekezere ndi munthu wodwala matenda a mtima amene afunika kudya zakudya zinazake zomuthandiza kuti achepetse vuto lakelo. Kodi chakudya chimenechi chingamuthandize ngati atamadya nthawi yokhayo imene mtima wayamba kupweteka? Ayi, ndithu. Kuti zimuyendere, iye amafunika kuti azidya chakudya chimenechi nthawi zonse. N’chimodzimodzinso ndi Baibulo. Kuliwerenga tsiku lililonse kudzakuthandizani ‘kukometsa njira yanu,’ kapena kuti kudzakuthandizani kuti zinthu zizikuyenderani bwino.

Mfundo 5​—Muzigwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana

▪ Kuwerenga Baibulo kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso n’kothandiza, koma pali njira zinanso zimene zingakuthandizeni, monga izi:

Werengani nkhani ya munthu mmodzi. Werengani machaputala onse kapena mabuku amene amanena za mtumiki winawake wa Mulungu. Mwachitsanzo:

Yosefe: Genesis 37-50.

Rute: Rute 1-3.

Yesu: Mateyu 1-28; Maliko 1-16; Luka 1-24; Yohane 1-21. *

Werengani nkhani imodzi. Werengani malemba amene akugwirizana ndi nkhaniyo. Mwachitsanzo, fufuzani nkhani zokhudza pemphero, kenako werengani zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyo komanso werengani ena mwa mapemphero ambirimbiri olembedwa m’Baibulo. *

Werengani motulutsa mawu. Mungapindule kwambiri ngati mumawerenga Baibulo motulutsa mawu. (Chivumbulutso 1:3) Mwinanso mungachite zimenezi monga banja, n’kumasinthana ndime kapena kugawana mawu a anthu opezeka mu nkhaniyo. Ena amakonda kumamvetsera matepi kapena ma CD a Baibulo. Mayi wina anati: “Poyamba zinkandivuta kuwerenga Baibulo, choncho ndinayamba ndi kumvetsera matepi a Baibulo. Pano ndimaona kuti kuwerenga Baibulo n’kokoma kuposa kuwerenga mabuku ankhani wamba.”

Mfundo 6​—Muziganizira zimene mukuwerenga

▪ Chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zotangwanitsa, anthu ambiri amalephera kupeza nthawi yoganizira zinthu zimene akuwerenga. Komabe, monga mmene chakudya chimayenera kugayika kuti chigwire bwino ntchito m’thupi, tiyenera kuganizira kwambiri zimene tawerenga m’Baibulo kuti tipindule. Timachita zimenezi mwa kudzikumbutsa zimene tawerenga ndi kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi nkhaniyi ikundiphunzitsa chiyani za Yehova Mulungu? Kodi zimenezi zingandithandize bwanji? Kodi mfundo zimenezi ndingathandizire bwanji anthu ena?’

Kuchita zimenezi kumathandiza kuti uthenga wa m’Baibulo utigwire mtima ndiponso kuti tizisangalala kwambiri tikamawerenga Mawu a Mulungu. Lemba la Salmo 119:97 limati: “Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.” Amene analemba Salmo limeneli ankaganizira Malemba tsiku lonse. Kuchita zimenezi kunamuthandiza kukonda kwambiri zimene ankaphunzira.

Mfundo 7​—Pemphani wina kuti akuthandizeni kulimvetsa

▪ Mulungu sayembekezera kuti tingamvetse tokha Mawu ake. Ngakhale Baibulo limanena kuti lili ndi “zinthu zina zovuta kuzimvetsa.” (2 Petulo 3:16) Buku la Machitidwe limafotokoza za munthu wina waudindo waukulu wa ku Itopiya amene sanamvetse zimene amawerenga m’Baibulo. Mulungu anatumiza mtumiki wake kuti akamuthandize, ndipo munthuyo “anapitiriza ulendo wake akusangalala.”​—Machitidwe 8:26-39.

Inunso mungapindule kwambiri ndi kuwerenga Baibulo mutapempha ena kuti akuthandizeni kumvetsa zimene mukuwerengazo. Pemphani a Mboni za Yehova a m’dera lanu, kapena mungalembe kalata ku adiresi imene ili patsamba 4 la magazini ino, kuti wina adzayambe kuphunzira nanu Baibulo kwaulere.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Baibulo la New World Translation, limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Baibulo limeneli lilipo m’Chichewa kuyambira Mateyo mpaka Chivumbulutso, ndipo limatchedwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu. Padziko lonse, Baibulo la New World Translation limapezeka lonse kapena mbali yake chabe m’zilankhulo 83. Baibulo limeneli likupezekanso pa Intaneti m’zinenero 17 pa adiresi iyi: www.jw.org.

^ ndime 15 Kuti mumve zambiri za Ufumu wa Mulungu ndiponso zimene udzachite, onani mutu 8 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 24 Ngati mwangoyamba kumene kuwerenga Baibulo, mungachite bwino kuyamba ndi buku la Maliko limene limafotokoza mwachidule zochita za Yesu.

^ ndime 25 Buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lathandiza anthu ambiri kuphunzira Baibulo motsatira nkhani imodzi m’chaputala chilichonse cha m’bukuli. Mwachitsanzo, Chaputala 17 chimafotokoza zimene Malemba amanena pa nkhani ya pemphero.