Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zikuchititsa Kuti Anthu Asalidziwe Dzina la Mulungu

Zimene Zikuchititsa Kuti Anthu Asalidziwe Dzina la Mulungu

PALI munthu winawake woipa amene akufuna kukulepheretsani kudziwa dzina la Mulungu lakuti Yehova komanso akufuna kuti musakhale naye paubwenzi wabwino. Kodi munthu woipa ameneyu ndani? Baibulo limafotokoza kuti: “Mulungu wa dongosolo lino la zinthu wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira.” Mulungu wa dziko loipali ndi Satana Mdyerekezi. Iye akufuna kuti mukhalebe mu mdima kuti “ulemerero wa kudziwa za Mulungu” usawale mumtima mwanu. Satana sakufuna kuti mum’dziwe bwino Yehova. Koma, kodi iye amachititsa bwanji khungu maganizo a anthu?​—2 Akorinto 4:4-6.

Satana amagwiritsa ntchito chipembedzo chonyenga pofuna kulepheretsa anthu kudziwa dzina la Mulungu. Mwachitsanzo, kalekale Ayuda ena anapewa kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu mwadala ngakhale kuti ankadziwa kuti Malemba amanena kuti iwo anafunika kuligwiritsa ntchito. Zikuoneka kuti m’nthawi ya atumwi, Ayuda amene ankawerengera anthu ena Malemba Opatulika, anauzidwa kuti akafika pamene pali dzina la Mulungu asamalitchule koma azingotchula dzina lomulemekezera lakuti ʼAdho·naiʹ, kutanthauza “Ambuye.” Mosakayikira, zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri asakhale paubwenzi ndi Mulungu ndiponso kuti ambiri asalandire madalitso amene amabwera chifukwa chokhala paubwenzi umenewu. Nanga bwanji Yesu? Kodi dzina la Mulungu lakuti Yehova ankaliona bwanji?

Yesu ndi Otsatira Ake Ankauza Ena Dzina la Mulungu

Yesu anauza Atate ake m’pemphero kuti: “Dzina lanu ndalidziwitsa . . . ndipo ndidzalidziwitsabe.” (Yohane 17:26) Mosakayikira Yesu anatchula dzina la Mulungu kambirimbiri powerenga, pogwira mawu kapena pofotokoza Malemba Achiheberi amene anali ndi dzina lofunika kwambiri limeneli. Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu ankagwiritsa ntchito dzina la Mulungu momasuka monga ankachitira aneneri onse amene analipo Yesuyo asanadzabadwe. Mwina Ayuda ena ankapewa kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu panthawi ya Yesu, koma iye sanachite nawo zimenezo. Yesu anatsutsa mwamphamvu atsogoleri achipembedzo powauza kuti: “Mwasandutsa mawu a Mulungu kukhala opanda pake chifukwa cha mwambo wanu.”​—Mateyo 15:6.

Yesu anapereka chitsanzo chabwino chouza ena dzina la Mulungu

Yesu atamwalira ndiponso kuukitsidwa, otsatira ake okhulupirika anapitirizabe kuuza anthu ena dzina la Mulungu. (Onani bokosi lakuti,  “Kodi Akhristu Oyambirira Ankatchula Dzina la Mulungu?”) Pa tsiku la Pentekoste, m’chaka cha 33 C.E., mpingo wachikhristu unakhazikitsidwa. Pa tsikuli mtumwi Petulo anagwira mawu a ulosi wa Yoweli ndipo anauza khamu la Ayuda ndi anthu amene analowa Chiyuda kuti: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Machitidwe 2:21; Yoweli 2:32) Akhristu oyambirirawo anathandiza anthu amitundu yambiri kulidziwa bwino dzina la Mulungu lakuti Yehova. N’chifukwa chake pamsonkhano wa atumwi ndi akulu, umene unachitikira ku Yerusalemu, wophunzira Yakobe anati: “Mulungu anacheukira amitundu . . . kuti mwa iwo atengemo anthu a dzina lake.”​—Machitidwe 15:14.

Ngakhale zinali choncho, mdani wa dzina la Mulungu anapitirizabe kuyesetsa kuti alithetseretu. Atumwi atamwalira, Satana anayambitsa mpatuko nthawi yomweyo. (Mateyo 13:38, 39; 2 Petulo 2:1) Mwachitsanzo, munthu wina wolemba mabuku achikhristu, dzina lake Justin Martyr, anabadwa cha panthawi imene Yohane, amene anali mtumwi womalizira, anamwalira. Ngakhale zinali choncho, iye ankakonda kulemba kuti Mulungu amene amatipatsa zinthu zimene timafunikira ndi “Mulungu wopanda dzina lake lenileni.”

Pali umboni wosonyeza kuti pamene Akhristu ampatuko ankakopera Malemba Achigiriki Achikhristu anachotsamo dzina la Mulungu lakuti Yehova, n’kumaikamo dzina lachigiriki lomulemekezera lakuti Kyʹri·os, kutanthauza “Ambuye.” Anachitanso zomwezi ndi Malemba Achiheberi. Popeza sankatchula dzina la Mulungu mokweza powerenga Malemba, alembi achiyuda amene anali ampatuko, anachotsa dzina la Mulungu m’Malemba Achiheberi m’malo okwana 130 n’kuikamo dzina laulemu lakuti ʼAdho·naiʹ. Nayenso Jerome amene anamaliza kumasulira Baibulo lotchuka lachilatini lotchedwa Vulgate mu 405 C.E., anachotsa dzina lenileni la Mulungu m’Baibulo limeneli.

Zimene Anthu Akuchita Pofuna Kuthetseratu Dzina la Mulungu

Masiku ano, akatswiri a maphunziro akudziwa kuti dzina la Mulungu lakuti Yehova limapezeka pafupifupi maulendo 7,000 m’Baibulo. Choncho, m’mabaibulo ena amene anthu ambiri amagwiritsa ntchito monga Baibulo la Akatolika la Jerusalem Bible ndi linanso la Akatolika lachisipanishi la La Biblia Latinoamérica komanso Baibulo lina lotchuka lachisipanishi la Reina-Valera, mumapezeka dzina lenileni la Mulungu kambirimbiri. M’mabaibulo ena dzina la Mulungu amalilemba kuti “Yahweh.”

Chomvetsa chisoni n’chakuti matchalitchi ambiri amene amapereka ndalama kuti anthu amasulire mabaibulo amakakamiza omasulirawo kuti asalembemo dzina la Mulungu. Mwachitsanzo, kalata yochokera ku Vatican ya pa June 29, 2008, yopita kwa mapulezidenti a mabungwe a mabishopu achikatolika, inati: “M’zaka zaposachedwapa anthu ena ayambanso kumatchula dzina lenileni la Mulungu wa Isiraeli.” Kenako kalatayi inachenjeza mosapita m’mbali kuti: “Dzina la Mulungu . . . silofunika kuligwiritsa ntchito kapena kulitchula.” Ndiyeno inanenanso kuti: “Pomasulira mabaibulo m’zilankhulo za masiku ano, . . . pamene pali zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu pazilembedwa mayina omulemekezera akuti Adonai kapena Kyrios, omwe amatanthauza kuti ‘Ambuye.’” Apa n’zoonekeratu kuti cholinga cha malangizo amene anachokera ku Vatican amenewa n’kuthetseratu dzina la Mulungu.

Matchalitchi enanso salemekeza dzina lenileni la Mulungu lakuti Yehova. Munthu wina wolankhula m’malo mwa bungwe limene linkamasulira Baibulo lachipolotesitanti la New International Version, limene linatuluka mu Chingelezi m’chaka cha 1978, analemba kuti: “Yehova ndiye dzina lenileni la Mulungu ndipo tinayeneradi kuligwiritsira ntchito. Koma pomasulira Baibulo limeneli panalowa ndalama zoposa madola 2 miliyoni. Ndiyeno mwachitsanzo, tikanamasulira lemba la Salmo 23 kuti ‘Yahweh ndiye mbusa wanga,’ ndiye kuti ndalamazo zikanalowa m’madzi.”

Komanso, ku Latin America matchalitchi alepheretsa anthu kudziwa dzina la Mulungu. Steven Voth, amene ndi mlangizi wa bungwe lomasulira mabaibulo la United Bible Societies (UBS) analemba kuti: “Nkhani imene imavuta m’matchalitchi amene si achikatolika ndi yokhudza dzina la Mulungu lakuti Jehová. . . . Chochititsa chidwi n’chakuti akuluakulu a tchalitchi china chachikulu kwambiri chachipentekosite chamakono . . . anatiuza kuti akufuna Baibulo la Reina Valera lomwe linatuluka koyamba mu 1960, koma iwo anati likhale lopanda dzina la Mulungu lakuti Jehová. Iwo anafuna kuti m’malomwake mukhale mawu akuti Señor [Ambuye].” Koma Voth ananena kuti poyamba bungweli linakana pempholi koma kenako linalolera ndipo linatulutsa Baibulo lina la Reina Valera “lopanda dzina lakuti Jehová.”

Kuchotsa dzina la Mulungu m’Baibulo, n’kuikamo dzina lakuti “Ambuye” kumalepheretsa anthu amene amaliwerenga kudziwa bwino dzina la Mulungu ndipo kuchita zimenezi kumasokoneza anthu. Mwachitsanzo, powerenga Mawu a Mulungu munthu angalephere kudziwa ngati mawu akuti “Ambuye” akunena za Yehova kapena Mwana wake, Yesu. N’chifukwa chake palemba limene mtumwi Petulo anagwira mawu a Davide akuti: “Yehova anati kwa Ambuye wanga [kutanthauza Yesu woukitsidwa]: ‘Khala ku dzanja langa lamanja,’” mabaibulo ambiri palembali amanena kuti: “Ambuye anati kwa Mbuye wanga.” (Machitidwe 2:34, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Kuwonjezera pamenepa, nkhani imene David Clines analemba ya mutu wakuti “Kodi Yahweh Ndi Mulungu wa Akhristu?” ananena kuti: “Kuchotsa dzina la Mulungu lakuti Yahweh m’Chikhristu kwachititsa kuti anthu azilemekeza kwambiri Khristu.” N’chifukwa chake anthu ambiri opemphera sadziwa kuti Mulungu woona amene Yesu ankamutchula m’mapemphero ake ndi munthu wa thupi lauzimu amene ali ndi dzina lenileni. Ndipo dzina lakelo ndi Yehova.

Satana wayesetsa kuchititsa khungu maganizo a anthu kuti asamudziwe bwino Mulungu. Ngakhale zili choncho, mungathe kumudziwa bwino Yehova.

Mungathe Kulidziwa Bwino Dzina la Mulungu Lakuti Yehova

Satana akuyesetsa kumenya nkhondo yofuna kuthetsa dzina la Mulungu, ndipo akugwiritsa ntchito chipembedzo chonyenga mochenjera pochita zimenezi. Koma palibe aliyense, kaya kumwamba kapena padziko lapansi amene angalepheretse Ambuye Mfumu Yehova kuti athandize anthu kumudziwa bwino ndiponso kudziwa zinthu zabwino kwambiri zimene iye akufuna kuchitira anthu okhulupirika.

Akhristu a Mboni za Yehova angasangalale kuphunzira nanu Baibulo n’cholinga choti mudziwe zimene mungachite kuti muyandikire Mulungu. Iwo amatsatira chitsanzo cha Yesu, amene anati: “Dzina lanu ndalidziwitsa kwa iwo ndipo ndidzalidziwitsabe.” (Yohane 17:26) Mukamaganizira malemba amene amanena za ntchito zosiyanasiyana zimene Yehova wachita kuti adalitse anthu, mudzazindikira makhalidwe ake ambiri apamwamba.

Munthu wokhulupirika Yobu ‘anali bwenzi lapamtima la Mulungu.’ Ndipo inunso mukhoza kukhala bwenzi Lake. (Yobu 29:4, NW) Mutawadziwa bwino Mawu a Mulungu, mukhoza kudziwa dzina la Mulungu lakuti Yehova. Kudziwa zimenezi kudzakuthandizani kukhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzachita zinthu mogwirizana ndi mawu amene ananena kuti ndi tanthauzo la dzina lake. Iye anati dzina lake limatanthauza kuti: ‘Amakhala amene wafuna kukhala.’ (Eksodo 3:14, NW) Choncho, iye adzakwaniritsadi zinthu zonse zabwino zimene walonjeza anthu.