Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Amaona Zabwino mwa Anthu

Amaona Zabwino mwa Anthu

Yandikirani Mulungu

Amaona Zabwino mwa Anthu

1 MAFUMU 14:13

“YEHOVA asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo.” (1 Mbiri 28:9) Cholinga cha mawu ouziridwa amenewa ndi kutithandiza kudziwa kuti Yehova amatikonda kwambiri. Yehova amaona zabwino zimene zili mumtima mwathu ngakhale kuti ndife ochimwa. Tikudziwa zimenezi chifukwa cha mawu amene Mulungu ananena okhudza Abiya, opezeka pa 1 Mafumu 14:13.

Abiya ankakhala ndi anthu oipa. Bambo ake Yerobiamu ndi amene anachititsa kuti banja lonse lachifumu likhale lopanduka. * Yehova anakonza zoti awonongeretu banja lonse la Yerobiamu ‘monga mmene munthu amachotsera ndowe.’ (1 Mafumu 14:10) Komabe Mulungu analamula kuti munthu mmodzi wa m’banja la Yerobiamu, dzina lake Abiya, amene ankadwala kwambiri, adzaikidwe m’manda mwaulemu. * N’chifukwa chiyani Mulungu analamula zimenezi? Mulungu anati: “Mwa iye mwapezedwa chokoma cha kwa Yehova Mulungu wa Israyeli m’nyumba ya Yerobiamu.” (1 Mafumu 14:1, 12, 13) Kodi mawu amenewa akutiuza chiyani za Abiya?

Baibulo silimanena ngati Abiya ankalambira Mulungu mokhulupirika. Komabe anali wabwino pa zinthu zina. Iye anali wabwino “kwa Yehova,” mwina pa nkhani yokhudza kumulambira. Mabuku ena a Arabi amanena kuti mwina Abiya anali wabwino chifukwa nthawi ina anapita kukalambira kukachisi wa ku Yerusalemu kapena chifukwa chakuti anachotsa alonda amene bambo ake anawaika kuti aziletsa Aisiraeli kupita ku Yerusalemu.

Ngakhale kuti sitikudziwa bwinobwino kuti anali wabwino pazifukwa ziti, mfundo ndi yakuti Abiya anali wabwino ndipo zinali zobisika. Choyamba, zinthu zabwinozo ankazichita kuchokera pansi pa mtima. Zimene Mulungu anaona kuti ndi zabwino mwa Abiya zinali “mwa iye,” kapena kuti mumtima mwake. Chachiwiri, m’banja lawo lonse iye yekha ndi amene ankachita zinthu zabwinozo. Abiya anasonyeza kuti anali wabwino ngakhale pamene anali “m’nyumba ya Yerobiamu.” Mbusa wina anati: “N’zosowa kwambiri munthu kukhalabe wabwino pamene akukhala m’dera loipa ndiponso m’banja lomwe anthu ake amachita zoipa.” Mbusa winanso ananena kuti zabwino zimene Abiya ankachita zinali “zoonekera kwa anthu . . . , monga mmene nyenyezi zimawalira kwambiri kunja kukakhala mdima, ndiponso ngati momwe mitengo ya mkungudza imakongolera kwambiri ikakhala pamalo a mitengo yopanda masamba.”

Chofunika kwambiri ndi chakuti mawu a pa 1 Mafumu 14:13 amatiphunzitsa mfundo ina yabwino kwambiri yokhudza Yehova ndiponso zimene amaona mwa ife. Kumbukirani kuti chinthu china chabwino ‘chinapezedwa mwa’ Abiya. Zikuoneka kuti Yehova anafufuza mumtima wa Abiya mpaka atapeza chinthu chabwino. Pomuyerekezera ndi anthu a m’banja lake, katswiri wina wamaphunziro ananena kuti Abiya anali “ngati mwala wamtengo wapatali womwe uli pamulu wamiyala wamba.” Yehova anasangalala chifukwa cha zabwino zimene Abiya anachita. Chifukwa cha zimenezi Mulungu anachitira chifundo munthu ameneyu, amene anali wabwino m’banja lawo lonse.

Ndi zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amaona zabwino mwa munthu ndipo amasangalala nazo ngakhale kuti ndife anthu ochimwa. (Salmo 130:3) Kudziwa zimenezi kuyenera kutilimbikitsa kuyandikira Yehova Mulungu, amene amafufuza mofatsa mumtima mwathu kuti apeze kalikonse kabwino, ngakhale katakhala kochepa bwanji.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Yerobiamu anayambitsa kulambira fano la mwana wang’ombe mu ufumu wakumpoto wa Isiraeli wa mafuko khumi. Iye anachita zimenezi n’cholinga choti anthu asiye kupita ku Yerusalemu kukalambira Yehova.

^ ndime 2 Nthawi imeneyo ngati munthu sanaikidwe m’manda mwaulemu, chinkaonedwa kuti ndi chizindikiro chakuti Mulungu samamukonda munthuyo.​—Yeremiya 25:32, 33.