Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Choonadi Chikubala Zipatso mwa Anthu Amene Mumawaphunzitsa?

Kodi Choonadi Chikubala Zipatso mwa Anthu Amene Mumawaphunzitsa?

Kodi Choonadi Chikubala Zipatso mwa Anthu Amene Mumawaphunzitsa?

PAMENE mnyamata wina dzina lake Eric ananena kuti sakufunanso kukhala wa Mboni za Yehova, makolo ake anakhumudwa kwambiri. Iwo sanaone chizindikiro chilichonse chakuti iye angachite zimenezi. Kuyambira ali mwana, Eric anali kuchita nawo phunziro la Baibulo la banja, kupita kumisonkhano yachikristu, ndi kulalikira nawo limodzi ndi mpingo. Tinganene kuti anali kuoneka ngati ali m’choonadi. Koma iye anachoka panyumba ndipo makolo ake anazindikira kuti choonadi cha m’Baibulo sichinali mwa iye. Izi zinawadzidzimutsa ndi kuwakhumudwitsa.

Enanso anamvapo chimodzimodzi pamene munthu amene anali kuphunzira naye Baibulo analeka phunzirolo mwadzidzidzi. Zoterezi zikachitika, anthu amadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani sindinadziwe kuti angachite zimenezi?’ Kodi n’zotheka kudziwiratu ngati choonadi chikubala zipatso mwa anthu amene timawaphunzitsa tsoka lauzimu lisanagwe? Kuwonjezera apo, kodi tingatsimikize bwanji kuti choonadi chikugwiradi ntchito mwa ife ndi mwa anthu amene timawaphunzitsa? M’fanizo la Yesu lodziwika bwino la wofesa, iye anapereka njira imene ingatithandize kuyankha mafunso amenewa.

Choonadi Chizikhudza Mtima

Yesu anati: “Mbewuzo ndizo mawu a Mulungu. Ndipo zija za m’nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mawu nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.” (Luka 8:11, 15) Choncho, kuti choonadi cha Ufumu chibale zipatso mwa ophunzira athu, choyamba chiyenera kumera mu mtima wawo wophiphiritsa. Yesu anatitsimikizira kuti monga imachitira mbewu yabwino m’nthaka yabwino, choonadi cha Mulungu chikakhudza mtima wabwino, chimayamba kugwira ntchito ndi kubala zipatso nthawi yomweyo. Tingadziwe bwanji ngati chikubaladi zipatso?

Tiyenera kuonetsetsa mtima wa munthu osati zochita zake zokha. Si nthawi zonse pamene kukhala ndi chizolowezi cha kulambira kumasonyeza zimene zilidi mu mtima wa munthu. (Yeremiya 17:9, 10; Mateyu 15:7-9) Tiyenera kuona kuposa pamenepo. Munthu ayenera kusinthiratu zokonda zake, zolinga zake ndi zimene amaika patsogolo m’moyo wake. Ayenera kukulitsa umunthu watsopano woyenerana ndi chifuniro cha Mulungu. (Aefeso 4:20-24) Mwachitsanzo: Paulo anati, Atesalonika atamva uthenga wabwino, anaulandira ndi mtima wonse mongadi mawu a Mulungu. Koma iye anatsimikizira kuti choonadi chinali kugwira ntchito mwa iwo chifukwa cha kupirira, kukhulupirika ndi chikondi chimene anasonyeza pambuyo pake.​—1 Atesalonika 2:13, 14; 3:6.

N’zoona kuti zimene zili mu mtima wa wophunzira, zidzaonekerabe m’makhalidwe ake monga anachitira Eric. (Marko 7:21, 22; Yakobo 1:14, 15) Koma vuto n’lakuti pamene makhalidwe oipa amaonekera, zimakhala mmbuyo mwa alendo. Chotero tiyenera kuyesetsa kuzindikira zofooka za munthuyo zisanam’punthwitse mwauzimu. M’pofunika kupeza njira yoonera zimene zili mu mtima wophiphiritsa. Tingachite bwanji zimenezi?

Phunzirani pa Zimene Yesu Anachita

Yesu ankatha kudziwa bwinobwino zimene zili m’mitima ya anthu. (Mateyu 12:25) Ife sitingathe kutero. Koma iye anasonyeza kuti ifenso tikhoza kuzindikira zimene munthu amakonda, zolinga zake ndi zimene amaika patsogolo pamoyo wake. Yesu anachita mofanana ndi zimene dokotala wodziwa bwino ntchito yake amachita pofuna kudziwa chimene chavuta ndi mtima wa munthu. Iye amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Nayenso Yesu anagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kuti adziwe ndi kuonetsa poyera ‘zolingalira ndi zitsimikizo za mtima,’ ngakhale zinali zobisika.​—Miyambo 20:5; Ahebri 4:12.

Mwachitsanzo, panthawi ina Yesu anathandiza Petro kudziwa kuti anali ndi vuto limene pambuyo pake linam’punthwitsa. Yesu ankadziwa kuti Petro amamukonda. Ndipotu panthawiyi n’kuti atapatsa Petro makiyi a Ufumu. (Mateyu 16:13-19) Koma Yesu anadziwanso kuti diso la Satana linali pa atumwiwo. M’tsogolo adzakumana ndi mavuto oopsa amene angagonjetse chikhulupiriro chawo. Yesu ayenera kuti anazindikira kuti ophunzira ake ena anali ndi zofooka m’chikhulupiriro chawo. Choncho sanazengereze kuwauza zoyenera kusintha. Taonani mmene anayambitsira nkhaniyo.

Pa Mateyu 16:21 pamati: “Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti ayenera . . . kukazunzidwa . . . ndi kukaphedwa.” Taonani kuti Yesu anawalangiza, osati kungowauza chabe zimene zidzam’chitikira. Ayenera kuti anagwiritsa ntchito malemba a m’Baibulo osonyeza kuti Mesiya adzazunzika ndi kufa, monga Salmo 22:14-18 ndi Yesaya 53:10-12. Yesu atawerenga kapena kugwira mawu a m’Malemba, zinapangitsa Petro ndi atumwi enawo kuonetsa zimene zinali pansi pa mitima yawo. Kodi anamva bwanji ndi mfundo yakuti Yesu adzazunzidwa?

Petro, pokhala munthu wodziwika ndi kulimba mtima ndiponso changu, anayankha nthawi yomweyo. Koma yankho lake panthawiyi linaonetsa kuti anali ndi maganizo olakwika kwambiri. Iye anati, “Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ayi.” Maganizo a Petro analidi atapotozedwa pakuti Yesu anati: “Susamalira za Mulungu, koma za anthu.” Zotsatira za maganizo amenewa zikanakhala zoopsa kwambiri. Kodi Yesu anatani? Yesu anadzudzula Petro ndipo kenako anamuuza limodzi ndi atumwi enawo kuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.” Pogwiritsa ntchito mfundo za pa Salmo 49:8 ndi 62:12, mokoma mtima anawakumbutsa kuti chiyembekezo chawo cha m’tsogolo sichinali mwa anthu amene sangathe kupulumutsa munthu, koma mwa Mulungu.​—Mateyu 16:22-28.

Ngakhale kuti mantha anagonjetsa Petro kwa nthawi yochepa moti anakana Yesu katatu, zimene Yesu ananena panthawiyi ndi panthawi zina, mosakayikira zinam’thandiza mwamsanga kukhalanso wolimba mwauzimu. (Yohane 21:15-19) Patangopita masiku 50, molimba mtima Petro anaimirira pamaso pa khamu lalikulu la anthu ku Yerusalemu kuchitira umboni za kuuka kwa Yesu. Kuchokera pamenepo, analolera kumangidwa, kumenyedwa ndi kum’tsekera m’ndende pafupipafupi. Anakhala chitsanzo chabwino kwambiri pa kukhala wokhulupirika mopanda mantha.​—Machitidwe 2:14-36; 4:18-21; 5:29-32, 40-42; 12:3-5.

Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhaniyi? Kodi mukuona zimene Yesu anachita kuti adziwe zimene zinali mu mtima wa Petro? Choyamba, anasankha malemba oyenera amene anapangitsa Petro kuganizira nkhani yofunika. Kenako anam’patsa mpata wofotokoza maganizo ake. Pomalizira, anam’patsa uphungu wa m’Malemba kum’thandiza kusintha maganizo ndi mtima wake. Mwina mukuganiza kuti simungathe kuphunzitsa motere. Koma tiyeni tione zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene kukonzekera ndi kudalira Yehova kungathandizire aliyense wa ife kutsatira chitsanzo cha Yesu.

Kudziwa Zimene Zili mu Mtima

Bambo wina wachikristu atamva kuti ana ake awiri aamuna, wa sitandade 1 ndi wa sitandade 2 anaba masiwiti pa desiki ya aphunzitsi, anakhala nawo pansi kuwafunsa nkhaniyi. Bamboyu sanaganize kuti amenewa ndi masewera chabe a ana. Iye anati, “Ndinayesetsa kudziwa chimene chinawachititsa kuchita zoipazi.”

Bamboyu anakumbutsa anawo zimene zinachitikira Akani m’nkhani yopezeka pa Yoswa chaputala 7. Nthawi yomweyo anyamatawo anaona ndi kuvomereza kuti analakwa ndipo anapepesa. Chikumbumtima chawo chinali chitayamba kale kuwatsutsa. Bamboyo anawawerengetsa lemba la Aefeso 4:28 limene limati: “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, . . . kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.” Iwo anauza anawo kuti akagule masiwiti ena ndi kukabweza kwa aphunzitsiwo. Zimenezi zinapangitsa uphungu wa m’Malembawu kukhala wamphamvu.

Bamboyo anati, “Tikangozindikira maganizo alionse oipa mwa ana athu, nthawi yomweyo tinkayesetsa kukambirana nawo ndi kuchotsa maganizowo n’kuwapatsa malangizo abwino.” Chifukwa cha kutsatira chitsanzo cha Yesu pophunzitsa ana awo, m’kupita kwa nthawi makolo amenewa anapindula. Anawo anaitanidwa kukatumikira ku Beteli ya ku likulu ku Brooklyn. Tsopano papita zaka 25 ndipo mmodzi wa iwo akutumikirabe kumeneko.

Taonaninso mmene mlongo wina anathandizira munthu amene anali kuphunzira naye Baibulo. Wophunzirayo anali kupita kumisonkhano, kulalikira, ndiponso ankafuna kubatizidwa. Koma zinkaoneka kuti anali kudzidalira kwambiri kuposa kudalira Yehova. Mphunzitsi wakeyo anati: “Pakuti wophunzirayo anali wosakwatiwa, sanazindikire kuti anali kudzidalira kwambiri. Ndinada nkhawa kuti mavuto adzafika pom’dwalitsa ndipo mwina akhoza kubwerera mmbuyo mwauzimu.”

Choncho mlongoyu anakambirana ndi wophunzira wakeyo lemba la Mateyu 6:33. Anamulimbikitsa kukonzanso zinthu pa moyo wake, kuika Ufumu patsogolo, ndi kukhulupirira kuti Yehova amusamala. Mosapita m’mbali anamufunsa kuti, “Kodi kukhala panokha nthawi zina kumakulepheretsani kudalira anthu ena ndi Yehova yemwe?” Wophunzirayo anavomereza ndipo anati anatsala pang’ono kuleka kupemphera. Kenako wofalitsayo anamulimbikitsa kutsatira langizo la pa Salmo 55:22 ndipo anamuuza kusenzetsa Yehova nkhawa zake chifukwa lemba la 1 Petro 5:7 limati, “Iye asamalira inu.” Mawu amenewa anam’fika pamtima. Mlongoyu anati, “Wophunzirayo analira ngakhale kuti anali munthu wosalira kawirikawiri.”

Choonadi Chizigwira Ntchito mwa Inu

Zimasangalatsa kwambiri kuona anthu amene tikuphunzira nawo akutsatira choonadi cha m’Baibulo. Koma kuti khama lathu pothandiza ena lipindule, ifeyo tiyenera kuonetsa chitsanzo chabwino. (Yuda 22, 23) Tonsefe tifunika ‘kugwira ntchito ya chipulumutso chathu ndi mantha, ndi kunthunthumira.’ (Afilipi 2:12) Zimenezi zikuphatikizapo kulola Malemba aunike mitima yathu nthawi zonse, afufuzemo maganizo oipa, zilakolako zoipa, ndi zinthu zosafunika zimene timakonda.​—2 Petro 1:19.

Mwachitsanzo, kodi changu chanu pantchito zachikristu chazilala posachedwapa? Ngati ndi choncho, n’chifukwa chiyani? Mwina n’chifukwa chakuti mukudzidalira kwambiri. Mungadziwe bwanji ngati limeneli ndilo vuto lanu? Werengani Hagai 1:2-11, ndipo moona mtima ganizirani zimene Yehova ananena kwa Ayuda atabwera ku ukapolo. Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikuda nkhawa kwambiri ndi kufunafuna chuma ndi katundu wabwino? Kodi ndimakhulupiriradi kuti Yehova adzasamalira banja langa ndikaika zinthu zauzimu patsogolo? Kapena ndimaona kuti ndiyenera kupeza zofunika pa moyo wanga choyamba?’ Ngati mukuona kuti muyenera kusintha maganizo ndi mtima wanu, musazengereze. Uphungu wa Malemba monga Mateyu 6:25-33, Luka 12:13-21, ndi 1 Timoteo 6:6-12, umatiuza mmene tiyenera kuonera zofunika pamoyo ndiponso chuma kuti Yehova azitidalitsa.​—Malaki 3:10.

Kudziunika moona mtima choncho kudzatichititsa kuganiza mozama. N’kovuta kuvomereza zofooka zathu ena akatiuza. Komabe kuthandiza mwana wanu kapena wophunzira Baibulo wanu mwachikondi, ngakhale inu eni, kungakhale mbali yoyamba yopulumutsa moyo wake kapena wanu. Mungachite zimenezi ngakhale nkhaniyo itakhala yaumwini ndi yovuta kwambiri.​—Agalatiya 6:1.

Nanga bwanji ngati simukuona kusintha kulikonse ngakhale mutayesetsa? Musafulumire kutaya mtima. Kuwongolera mtima wopanda ungwiro nthawi zina kungakhale kovuta, kotenga nthawi, ndiponso kogwetsa mphwayi. Koma kungakhalenso kopindulitsa.

Eric, mnyamata amene tam’tchula kuchiyambi kwa nkhani ino uja, pambuyo pake anazindikira kulakwa kwake ndipo anayambiranso ‘kuyenda m’choonadi.’ (2 Yohane 4) Iye anati, “Ndinazindikira kulakwa kwanga ndipo ndinabwerera kwa Yehova.” Ndi thandizo la makolo ake, tsopano Eric akutumikira Mulungu mokhulupirika. Ngakhale kuti nthawi ina ankaipidwa ndi zimene makolo ake ankachita pomuthandiza kulingalira bwino, tsopano akuyamikira kwambiri zimenezo. Iye anati, “Makolo anga ndi abwino kwambiri, sanaleke kundikonda.”

Kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kuunikira mitima ya amene timawaphunzitsa kumasonyeza kukoma mtima. (Salmo 141:5) Pitirizani kuunika mitima ya ana anu ndi ophunzira Baibulo anu kuti muone ngati umunthu watsopano wachikristu ukuyala maziko mwa iwo. Chititsani choonadi kugwira ntchito mwa inu ndi mwa anthu ena ‘polunjika nawo bwino mawu a choonadi.’​—2 Timoteo 2:15.

[Chithunzi patsamba 29]

Mawu a Yesu anaonetsa poyera kuti Petro anali ndi vuto linalake

[Chithunzi patsamba 31]

Gwiritsani ntchito Baibulo kuti mudziwe zimene zili mu mtima