Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Moyo Wanu Ndi Wamtengo Wapatali Motani?

Kodi Moyo Wanu Ndi Wamtengo Wapatali Motani?

 Kodi Moyo Wanu Ndi Wamtengo Wapatali Motani?

PAMENE miyoyo yosawerengeka inali kuwonongeka pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse ku Ulaya, munthu wina anachita khama kwambiri kuti apulumutse miyoyo kumalo ozizira kwambiri a Antarctica. Munthu ameneyu anali wofufuza malo wa ku Britain dzina lake Ernest Shackleton. Iye limodzi ndi anzake anali pa ulendo wa panyanja m’chombo chotchedwa Endurance, koma chombocho chinasweka ndi kumira chifukwa cha madzi oundana. Shackleton anapulumutsira anyamata ake pa chilumba chotchedwa Elephant chomwe chili m’nyanja ya mchere ya South Atlantic. Komabe zinthu sizinali bwino kwenikweni chifukwa malowo anali ozizira kwambiri.

Shackleton anaona kuti ayenera kukapempha thandizo ku mudzi wina wa asodzi pachilumba cha South Georgia kuti onse apulumuke. Unali ulendo wa makilomita 1,100 ndipo iye anali ndi  boti limodzi lokha lalitali mamita 7 limene anatenga pa chombo cha Endurance. Moyo wawo unalidi pachiswe.

Atayenda movutikira kwambiri kwa masiku 17, pa May 10, 1916, Shackleton ndi anyamata ake angapo anafika ku South Georgia. Koma chifukwa cha nyengo yoipa panyanja, boti lawo linakocheza mbali yolakwika ya chilumbacho. Kuchokera kumbali imeneyo, anayenera kuyenda mtunda wa makilomita 30 kudutsa m’mapiri okutidwa ndi madzi oundana ndiponso mopanda njira kuti akafike ku mudzi wa asodzi uja. Ulendowu unali woopsa chifukwa cha kuzizira kwambiri ndiponso analibe zipangizo zokwerera mapiri. Koma ngakhale zinkaoneka ngati n’zosatheka, Shackleton ndi anzakewo anafika kumudzi wa asodzi uja ndipo pambuyo pake anakapulumutsa anyamata ake onse pa chilumba cha Elephant. N’chifukwa chiyani Shackleton analolera kuvutika chonchi? “Cholinga chake chinali chakuti apulumutse anyamata ake onse,” anatero wolemba mbiri ya anthu Roland Huntford.

“Palibe Imodzi Isoweka”

Kodi n’chiyani chinathandiza anyamata a Shackleton kusataya mtima pamene anali khuma, kum’dikira “pa chilumba cha makilomita 30 okha chozizira ndi chakutali”? Anali ndi chikhulupiriro chakuti mtsogoleri wawo asunga lonjezo lake lakuti adzawapulumutsa.

Masiku ano, anthu ndi osowa pogwira mofanana ndi anthu aja amene anali pa chilumba cha Elephant. Ambiri akukhala mu umphawi wadzaoneni ndipo amavutika kwambiri kuti apeze chakudya chokha. Komabe angakhale ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu ‘adzapulumutsa wozunzika’ ku nsautso ndi kupsinjika. (Yobu 36:15) Musakayikire zoti moyo wa munthu aliyense ndi wamtengo wapatali kwa Mulungu. Mlengiyo, Yehova Mulungu amati, “Undiitane tsiku la chisautso: ndidzakulanditsa.”​—Salmo 50:15.

Kodi zikukuvutani kukhulupirira kuti mwa anthu mabiliyoni angapo padziko lapansili, Mlengi amakuonani inuyo panokha kuti ndinu wamtengo wapatali? Ngati ndi choncho, taonani zimene mneneri Yesaya analemba ponena za nyenyezi zambirimbiri zimene zili m’milalang’amba yambirimbiri imene ili mu mlengalengamu. Timawerenga kuti: ‘Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziwerenga; azitcha zonse mayina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.’​—Yesaya 40:26.

Kodi mukumvetsa tanthauzo lake? Dzuwa ndi zonse zimene zimalizungulira zili mbali yochepa chabe ya mlalang’amba, kapena kuti gulu la nyenyezi lotchedwa Milky Way. Mlalang’amba umenewu, uli ndi nyenyezi pafupifupi 100 biliyoni. Koma kodi milalang’amba ilipo ingati? Palibe amene anganene motsimikiza koma ena amaganiza kuti ingakwane 125 biliyoni. Kodi kuchuluka kwa nyenyezi si kodabwitsa? Komatu Baibulo limatiuza kuti Mlengi wa chilengedwe chonse amadziwa nyenyezi iliyonse ndi dzina lake lomwe.

‘Amawerenga Tsitsi Lonse la M’mutu Mwanu’

Mwina ena angatsutse kuti, ‘Kungodziwa mayina a nyenyezi zambirimbiri kapena a anthu sikutanthauza kuti munthuyo amakhudzika ndi nyenyezi iliyonse kapena munthu aliyense payekha.’ Kompyuta yamphamvu ingasunge mayina ambirimbiri a anthu. Koma palibe anganene kuti kompyutayo imakhudzika ndi moyo wa anthuwo. Komatu Baibulo limasonyeza kuti Yehova Mulungu samangodziwa chabe mayina a anthu ambirimbiri koma amasamala za munthu aliyense payekha. Mtumwi Petro analemba kuti: ‘Tayani pa Iye nkhawa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.’​—1 Petro 5:7.

Yesu Kristu anati: “Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu: komatu inu, matsitsi onse  a m’mutu mwanu awerengedwa. Chifukwa chake musamawopa; inu mupambana mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29-31) Taonani kuti Yesu sanati Mulungu atha kungodziwa chabe zimene zachitikira mpheta kapena anthu. Anati: “Inu mupambana mpheta zambiri.” N’chifukwa chiyani muli opambana kapena kuti ofunika kwambiri? Chifukwa ‘munapangidwa m’chifanizo cha Mulungu.’ Izi zikutanthauza kuti mukhoza kukhala ndi khalidwe labwino, nzeru, ndiponso makhalidwe auzimu amene amasonyeza makhalidwe a Mulungu apamwamba.​—Genesis 1:26, 27.

‘Zinapangidwa ndi Winawake Wanzeru’

Musasochezedwe ndi anthu amene amalimbikira kunena kuti kulibe Mlengi. Iwo amati munapangidwa mwangozi ndi mphamvu inayake yachilengedwe yosadziwika bwino. Amatinso inu simunapangidwe “m’chifanizo cha Mulungu,” ndipo simusiyana ndi nyama zina zonse padziko lapansi pano kuphatikizapo mpheta.

Kodi ndi mfundo yomveka kwa inu kuti zamoyo zinangokhalako mwangozi? Malinga ndi zimene ananena katswiri wa sayansi ya zamoyo Michael J. Behe, ‘dongosolo la tizigawo ting’onoting’ono timene timapanga zamoyo, n’lodabwitsa kwambiri’ moti n’zosamveka kunena kuti zamoyo zinangokhalako mwangozi. Iye anati, umboni umene sayansi imeneyi yapeza umasonyeza mfundo imodzi yosapeweka yakuti, “chamoyo chilichonse padziko lapansi . . . chinapangidwa ndi winawake wanzeru.” Limatero buku lakuti Darwin’s Black Box​—The Biochemical Challenge to Evolution.

Baibulo limatiuza kuti chamoyo chilichonse padziko lapansi chinapangidwa ndi winawake wanzeru. Ndiponso limatiuza kuti Yehova Mulungu, Mlengi wa chilengedwe chonse, ndiye Mwini wake wa zolengedwa zimenezi.​—Salmo 36:9; Chivumbulutso 4:11.

Musalole zopweteka ndi masautso amene timakumana nawo nthawi zonse m’dzikoli kukulepheretsani kukhulupirira kuti kuli Mlengi amene anakonza dziko lapansili ndi zamoyo zonse. Pali mfundo ziwiri zofunika kumazikumbukira. Yoyamba ndi yakuti, Mulungu sanakonze kuti zinthu zikhale zoipa mmene zililimu. Yachiwiri ndi yakuti, pali zifukwa zomveka zimene Mlengi wathuyo walolera kuti kusalungama kukhalepo kwa kanthawi kochepa. Monga mmene magazini ino imanenera kawirikawiri, Yehova Mulungu walola kuti zoipa zikhalepo kwa kanthawi kochepa chabe. Walolera zimenezi pofuna kuthetseratu nkhani zimene zinayamba pamene anthu anakana ulamuliro wake pachiyambi penipeni. *​—Genesis 3:1-7; Deuteronomo 32:4, 5; Mlaliki 7:29; 2 Petro 3:8, 9.

“Adzapulumutsa Waumphawi Wofuulayo”

Komatu ngakhale kuti pali mavuto aakulu amene anthu ambiri tikukumana nawo masiku ano, moyo ndi mphatsobe yosangalatsa. Ndipo timayesetsa kuti tikhalebe ndi moyo. Moyo wa m’tsogolo umene Mulungu analonjeza, si moyo wongokhalira kuvutika ngati anthu a Shackleton pa chilumba cha Elephant. Cholinga cha Mulungu n’chakuti atipulumutse ku moyo wopweteka ndi wopanda pakewu, ndi kuti ‘tikagwire moyo weniweniwo’ umene Mulungu anakonzera anthu pachiyambi pomwe.​—1 Timoteo 6:19.

Mulungu adzachita zimenezi chifukwa chakuti aliyense wa ife ndi wamtengo wapatali kwa iye. Anakonza kuti Mwana wake Yesu Kristu apereke nsembe ya dipo imene ili yofunika kutiwombola ku uchimo, kupanda ungwiro, ndi imfa imene  tinalandira kwa makolo athu oyambirira Adamu ndi Hava monga cholowa. (Mateyu 20:28) Yesu Kristu anati, “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye . . . akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

Kodi Mulungu adzawachitira chiyani anthu amene panopa moyo wawo uli wamavuto ndi woponderezedwa? Mawu a Mulungu ouziridwa amatiuza kuti Mwana wake “adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.” Kodi adzachitiranji zimenezi? Chifukwa ‘mwazi wawo [kapena kuti moyo wawo] udzakhala wa mtengo wapatali pamaso pake.’​Salmo 72:12-14.

Kwa zaka mazanamazana, anthufe takhala tikuvutika ndi goli la uchimo ndi kupanda ungwiro. Zili ngati ‘tikubuula’ chifukwa cha ululu waukulu ndi zovuta. Mulungu analolera zimenezi podziwa kuti akhoza kuthetsa mavuto onse amene angakhalepo. (Aroma 8:18-22) Posachedwapa ‘adzakonzanso zinthu zonse’ pogwiritsa ntchito boma la Ufumu lotsogoleredwa ndi Mwana wake Yesu Kristu.​—Machitidwe 3:21; Mateyu 6:9, 10.

Zimenezi zikuphatikizapo kuukitsa anthu amene anavutika ndipo anafa. Anthu amenewo Mulungu akuwakumbukira. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Posachedwapa adzalandira moyo “wochuluka.” Umenewu ndi moyo wosatha ndi wangwiro padziko lapansi la paradaiso lopanda zowawa ndi mavuto. (Yohane 10:10; Chivumbulutso 21:3-5) Aliyense adzasangalala ndi moyo mokwanira. Adzatha kukhala ndi makhalidwe abwino ndi luso lodabwitsa loyeneradi anthu opangidwa “m’chifanizo cha Mulungu.”

Kodi mukufuna kudzakhala ndi moyo wosangalatsawu umene Yehova walonjeza? Zonse zili ndi inu. Tikukulimbikitsani kutsatira dongosolo limene Mulungu waika kuti abweretse madalitso onsewa. Ofalitsa magazini ino ndi okonzeka kukuthandizani kutero.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Kuti mumve tsatanetsatane wa nkhaniyi, werengani mutu 8 wakuti, “Kodi Mulungu Waloleranji Kuvutika?” m’buku la Mboni za Yehova lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Anyamata a Shackleton anali ndi chikhulupiriro chakuti iye asunga lonjezo lake lakuti adzawapulumutsa

[Mawu a Chithunzi]

© CORBIS

[Chithunzi patsamba 6]

“Inu mupambana mpheta zambiri”