Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo, Kodi Ndi Wamtengo Wapatali, Kapena Wopanda Pake?

Moyo, Kodi Ndi Wamtengo Wapatali, Kapena Wopanda Pake?

 Moyo, Kodi Ndi Wamtengo Wapatali, Kapena Wopanda Pake?

“Popeza kuti munthu anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, kupha munthu n’kuwononga chinthu chamtengo wapatali ndi chopatulika kwambiri padziko lapansi.” Limatero buku lakuti The Plain Man’s Guide to Ethics, lolembedwa ndi William Barclay.

KODI inunso mumaona kuti moyo wa munthu ndi ‘chinthu cha mtengo wapatali kwambiri padziko lapansi?’ Zimene anthu ambiri amachita zimaonetseratu kuti sagwirizana ndi zimene wolemba bukuli ananena. Anthu ambiri aphedwa mwankhanza ndi anthu achiwawa ongofuna kukwaniritsa zolinga zawo mosaganizira moyo wa anthu anzawo.​—Mlaliki 8:9.

Anthu Oonedwa Ngati Osafunika ndi Opanda Pake

Chitsanzo pankhaniyi ndi nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Wolemba mbiri yakale A.J.P. Taylor anati, panthawi imene nkhondo yoopsayo inali mkati, nthawi ndi nthawi “anthu anali kufa popanda chifukwa chenicheni.” Pofuna kutchuka ndi ulemerero, atsogoleri a asilikali ankagwiritsa ntchito asilikaliwo ngati kuti moyo wawo unali wopanda ntchito ndi wosafunika. Pa kumenyana kumene kunachitikira ku Verdun m’dziko la France, asilikali oposa 700,000, anaphedwa. A Taylor anati, “malo amene anali kulimbiranawo analibe phindu lililonse pankhondoyo. Iwo ankangofuna kuphana ndi kupeza ulemerero basi.” Limatero buku lakuti The First World War.

Kusalemekeza moyo kotero kukadali kofala. Katswiri wina wa maphunziro Kevin  Bales anati, masiku ano “kuchuluka kwa anthu padziko lonse kwapangitsa kuti pakhale anthu ambiri osauka ndi osowa pogwira amene akufunafuna ntchito.” Amavutika kwambiri kupeza zofunika pa moyo wawo m’dziko lino lopondereza pa zachuma limene lachititsa “moyo kukhala wopanda pake.” Anthu amene amawagwiritsa ntchito saganizira za moyo wawo, ndipo amawagwiritsa ntchito ngati akapolo, “monga zida zopangira ndalama basi.” Anatero a Bales m’buku lakuti Disposable People.

“Kungosautsa Mtima”

Pali zifukwa zambiri zimene zimachititsa anthu ambirimbiri kudziona kuti ndi opanda ntchito ndi osowa pogwira. Amaona kuti anthu alibe nawo ntchito kaya akhale ndi moyo kapena ayi. Zifukwa zina ndi nkhondo, kupanda chilungamo, chilala, njala, matenda, imfa, ndi mavuto ena osawerengeka amene akusautsa anthu. Izi zimapangitsa anthu kukayika ngati kukhala ndi moyo kulidi kwamtengo wapatali.​—Mlaliki 1:8, 14.

N’zoona kuti si anthu onse amene akuvutika ndi umphawi wadzaoneni. Komabe ngakhale anthu amene sali m’mavuto aakulu, kawirikawiri amanena mawu ofanana ndi a Mfumu Solomo ya dziko lakale la Israyeli. Iyo inafunsa kuti: “Munthu ali ndi chiyani m’ntchito zake zonse, ndi m’kusauka kwa mtima wake amasauka nazozo kunja kuno?” Anthu ambiri amati akaganiza mofatsa, amaona kuti zambiri zimene achita zangokhala ‘zachabe ndi kungosautsa mtima.’​—Mlaliki 2:22, 26.

Akamaona mmene moyo wawo wakhalira, amadzifunsa kuti, “kodi moyo ndi umenewu basi?” Zoonadi, ndi angati amene kumapeto kwa moyo wawo amakhala atakhutira ndi ukalamba wabwino wa masiku ambiri, monga Abrahamu wakale? (Genesis 25:8) Ambiri amaona kuti moyo wawo wakhala wopanda pake. Komatu moyo suyenera kukhala wopanda pake. Mulungu amaona kuti moyo wa munthu aliyense ndi wa mtengo wapatali ndipo amafuna kuti aliyense akhale ndi moyo wabwino ndi wokhutiritsa. Kodi zimenezi zidzatheka bwanji? Taonani zimene nkhani yotsatira ikunena pankhaniyi.