Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tonthozanani

Tonthozanani

Tonthozanani

“Ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.”​—AKOLOSE 4:11.

1, 2. N’chifukwa chiyani anzake a Paulo ankapita kukamuona kundende ngakhale kuti kuchita zimenezi kunali koopsa?

ZINGAKHALE zoopsa kukhala bwenzi la munthu amene akuvutika kundende, ngakhale mnzanuyo ataikidwa m’ndende mopanda chilungamo. Oyang’anira kundendeko angamakukayikireni, angamayang’anitsitse chilichonse chimene mukuchita pofuna kuonetsetsa kuti simukuchita chilichonse chophwanya lamulo. Motero, pamafunika kulimba mtima kuti mupitirize kulankhulana ndi mnzanuyo ndiponso kumapita kukamuona kundendeko.

2 Komatu, zimenezi n’zimene anzake ena a Paulo anachita zaka pafupifupi 1,900 zapitazo. Sanazengereze kupita kukamuona Paulo kundende kuti akamutonthoze ndi kumulimbikitsa mwauzimu. Kodi anzake okhulupirikaŵa anali ndani? Ndipo tingaphunzire chiyani pa kulimba mtima kwawo, kukhulupirika kwawo, ndiponso ubwenzi wawo?​—Miyambo 17:17.

‘Onditonthoza Mtima’

3, 4. (a) Kodi anzake asanu a Paulo anali ndani, ndipo anakhala otani kwa iye? (b) Kodi ‘chotonthoza mtima’ n’chiyani?

3 Tiyeni tibwerere m’mbuyo pafupifupi m’chaka cha 60 C.E. Mtumwi Paulo anali m’ndende ku Roma chifukwa cha mlandu womunamizira wakuti anali woukira. (Machitidwe 24:5; 25:11, 12) Paulo anatchula Akristu asanu amene anali kum’thandiza. Akristu ameneŵa anali Tukiko, nthumwi yake, wa ku chigawo cha ku Asiya ndiponso ‘kapolo mnzake mwa Ambuye’; Onesimo, “mbale wokhulupirika ndi wokondedwa” wa ku Kolose; Aristarko Mmakedoniya wa ku Tesalonika ndipo nthaŵi ina anali ‘wam’ndende mnzake’ wa Paulo; Marko, msuwani wa mmishonale mnzake wa Paulo, Barnaba, ndiponso amene analemba Uthenga Wabwino umene uli ndi dzina lake; ndi Yusto, mmodzi mwa antchito anzake a mtumwiyu “mu Ufumu wa Mulungu.” Paulo ananena za anthu asanu ameneŵa kuti: “Ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.”​—Akolose 4:7-11.

4 Paulo anagwiritsa ntchito mawu amphamvu pofotokoza thandizo limene anzake okhulupirikaŵa anam’patsa. Anagwiritsa ntchito liwu lachigiriki (lakuti pa·re·go·riʹa) limene lamasuliridwa kuti “chotonthoza mtima,” lomwe m’Baibulo limangopezeka pa vesi lokhali basi. Liwu limeneli lili ndi matanthauzo osiyanasiyana ndipo linali kugwiritsidwa ntchito makamaka pankhani ya zamankhwala. * Liwuli lingamasuliridwe kuti ‘kutonthoza, kuziziritsa, kulimbikitsa, kapena kupatsa mpumulo.’ Paulo ankafunika chitonthozo choterocho, ndipo amuna asanu ameneŵa anamutonthoza.

Chifukwa Chake Paulo Ankafunika ‘Chotonthoza Mtima’

5. Ngakhale kuti Paulo anali mtumwi, kodi anafunikira chiyani, ndipo tonsefe timafunikira chiyani nthaŵi zina?

5 Ena angadabwe kuti Paulo, yemwe anali mtumwi, anafunikira kutonthozedwa. Inde, anafunikiradi. N’zoona kuti Paulo anali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo anapirira mazunzo, “m’mikwingwirima mosaŵerengeka, muimfa kaŵirikaŵiri,” ndiponso zopweteka zina. (2 Akorinto 11:23-27) Komabe, iye anali munthu, ndipo anthu onse nthaŵi zina amafunika kutonthozedwa ndi kulimbitsa chikhulupiriro chawo pothandizidwa ndi anthu ena. Ngakhale Yesu anafunikira zimenezi. Pa usiku woti m’maŵa mwake aphedwa, mngelo anaonekera kwa iye ku Getsemane ndipo “[a]nam’limbitsa iye.”​—Luka 22:43.

6, 7. (a) Kodi ndani anakhumudwitsa Paulo ku Roma, ndipo ndani anamulimbikitsa? (b) Kodi abale achikristu a Paulo anam’tumikira motani ku Roma, zimene zinachititsa kuti akhale ‘otonthoza mtima’?

6 Paulo ankafunanso kulimbikitsidwa. Atafika ku Roma monga mkaidi, sanalandiridwe ndi manja aŵiri ndi anthu a mtundu wake. Ambiri mwa Ayuda amenewo sanalabadire uthenga wa Ufumu. Akuluakulu a Ayuda atakamuona Paulo kundende, nkhaniyo m’buku la Machitidwe imati: “Ena anamvera zonenedwazo, koma ena sanamvera. Koma popeza sanavomerezana, anachoka.” (Machitidwe 28:17, 24, 25) Kusayamikira kwawo chifundo cha Yehova kuyenera kuti kunam’pweteka mtima Paulo. Maganizo ake amphamvu pa nkhani imeneyi anaonekera m’kalata yake imene analembera mpingo wa ku Roma zaka zingapo zimenezi zisanachitike. Anati: “Ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kupwetekedwa mtima kosaleka. Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Kristu chifukwa cha abale anga [Ayuda], ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi.” (Aroma 9:2, 3) Komabe, ku Roma anapeza anzake enieni okhulupirika amene kulimba mtima ndi chikondi chawo zinatonthoza mtima wake. Ameneŵa anali abale ake auzimu enieni.

7 Kodi abale asanu amenewo anakhala bwanji omutonthoza mtima? Iwo sanalole kuti kukhala m’ndende kwa Paulo kuwachititse kumupeŵa. M’malo mwake, anamutumikira Paulo mofunitsitsa ndiponso mwachikondi, kugwira ntchito zimene Pauloyo sakanatha kuzigwira yekha chifukwa chakuti anali m’ndende. Mwachitsanzo, anam’tumikira monga amithenga ndipo anapititsa makalata a Paulo ndi malangizo apakamwa ku mipingo yosiyanasiyana. Ankam’bweretsera Paulo malipoti olimbikitsa osimba za umoyo wa abale a ku Roma ndi a m’madera ena. Ayeneranso kuti ankam’pezera Paulo zinthu zofunika pa moyo, monga zovala za nthaŵi yozizira, mipukutu, ndi zipangizo zolembera. (Aefeso 6:21, 22; 2 Timoteo 4:11-13) Kumuthandiza konseku kunalimbikitsa mtumwi wa m’ndendeyo motero kuti nayenso akanakhala ‘chotonthoza mtima’ kwa ena, kuphatikizapo mipingo yathunthu.​—Aroma 1:11, 12.

Mmene Tingakhalire ‘Otonthoza Mtima’

8. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa kuvomereza modzichepetsa kwa Paulo kuti anafunikira ‘chotonthoza mtima’?

8 Kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani imeneyi ya Paulo ndi antchito anzake asanu? Tiyeni tione phunziro limodzi mwapadera, phunziro lakuti: Pamafunika kulimba mtima ndi kudzimana kuti tithandize ena amene ali m’mavuto. Ndiponso, pamafunika kudzichepetsa kuti tivomereze kuti tingafunike kuthandizidwa panthaŵi imene takumana ndi mavuto. Paulo sanangovomereza kuti anafunikira thandizo koma analandiranso thandizolo mwaulemu ndipo anayamikira anthu amene anali kum’thandizawo. Iye sanaone kuti kulandira thandizo kwa ena ndi chizindikiro cha kufooka kapena chomuchititsa manyazi, ndipo ifenso sitiyenera kuona motero. Ngati tinganene kuti sitifunika kutonthozedwa zingatanthauze kuti ndife zolengedwa zauzimu. Kumbukirani kuti chitsanzo cha Yesu chikusonyeza kuti ngakhale munthu wangwiro nthaŵi zina angafunikire kupempha thandizo.​—Ahebri 5:7.

9, 10. Kodi pangakhale zotsatira zabwino ziti munthu akavomereza kuti amafunika kuthandizidwa, ndipo zimenezi zingakhudze bwanji ena m’banja ndi mumpingo?

9 Pangakhale zotsatira zabwino ngati anthu amene ali pa maudindo avomereza kuti pali zina zimene sangathe kuchita ndi kuti amadalira thandizo la ena. (Yakobo 3:2) Kuvomereza koteroko kumalimbitsa mgwirizano umene ulipo pakati pa anthu audindowo ndi anthu amene akuwayang’anira, zimene zimalimbikitsa kulankhulana momasuka ndiponso mwaubwenzi. Kudzichepetsa kwa anthu amene ndi okonzeka kulandira thandizo kumakhala phunziro kwa ena amene angafunenso kutero. Zimasonyeza kuti amene akutsogolera nawonso ndi anthu ndipo ndi osavuta kulankhula nawo.​—Mlaliki 7:20.

10 Mwachitsanzo, ana sizingawavute kulandira thandizo la makolo polimbana ndi mavuto ndi zokopa akadziŵa kuti makolo awowo nawonso anakumana ndi mavuto ofanana ndi amenewo pamene anali ana. (Akolose 3:21) Motero, pangakhale kukambirana kwabwino pakati pa kholo ndi mwana. Angakambirane mogwira mtima njira za m’Malemba zothetsera mavutowo ndipo angazitsatire mosavuta. (Aefeso 6:4) Mofanana ndi zimenezi, anthu mumpingo angakhale okonzeka kulandira thandizo la akulu ngati angadziŵe kuti nawonso akulu amalimbana ndi mavuto, zinthu zochititsa mantha, ndiponso kusadziŵa kuti chichitike n’chiyani pankhani zina. (Aroma 12:3; 1 Petro 5:3) Apanso, pangakhale kukambirana kwabwino, angakambirane malangizo a m’Malemba, ndipo angalimbikitsane chikhulupiriro. Kumbukirani kuti abale ndi alongo athu akufunika kulimbikitsidwa panopa kuposa ndi kale lonse.​—2 Timoteo 3:1.

11. N’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano akufunikira ‘chotonthoza mtima’?

11 Zilibe kanthu kuti tikukhala kuti, ndife ndani, kapena ndife achichepere kapena achikulire, tonsefe nthaŵi ina tidzakumana ndi mavuto m’moyo. Ndi mmene moyo ulili m’dzikoli masiku ano. (Chivumbulutso 12:12) Mavuto ameneŵa amene amakhudza thupi lathu kapena maganizo athu amayesa mmene chikhulupiriro chathu chilili. Tingakumane ndi mavuto kuntchito, kusukulu, m’banja, kapena mumpingo. Mavuto angakhaleponso mwina chifukwa cha matenda akayakaya kapena kupwetekedwa mtima chifukwa cha zimene zinachitika kale. Ngati mwamuna kapena mkazi wathu, mkulu, kapena mnzathu atilimbikitsa mokoma mtima ndi mawu abwino ndiponso kuchita zinthu zina zofuna kutithandiza, zingakhale zotonthoza kwambiri. Inde, kuli ngati kuika mankhwala pa khungu pamene pakupweteka. Motero, mukaona mmodzi mwa abale anu akudwala kapena kuvutika maganizo, mutonthozeni mtima. Kapena ngati vuto lalikulu likukuvutitsani maganizo, pemphani anthu oyenerera mwauzimu kuti akuthandizeni.​—Yakobo 5:14, 15.

Mmene Mpingo Ungathandizire

12. Kodi aliyense mumpingo angatani kuti alimbikitse abale ake?

12 Anthu onse mumpingo, kuphatikizapo ana, angachite zinthu zolimbikitsa ena. Mwachitsanzo, kupezeka kwanu nthaŵi zonse pamisonkhano ndiponso mu utumiki wa kumunda kumalimbikitsa kwambiri chikhulupiriro cha ena. (Ahebri 10:24, 25) Kuchita kwanu utumiki wopatulika mosalekeza ndi umboni wakuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova ndipo zimasonyeza kuti mukukhala maso mwauzimu ngakhale kuti mungakhale mukukumana ndi mavuto. (Aefeso 6:18) Kupitirizabe kuchita zimenezo kungalimbikitse ena.​—Yakobo 2:18.

13. Kodi n’chiyani chingachititse ena kusiya kulalikira, ndipo angathandizidwe bwanji?

13 Nthaŵi zina mavuto amene timakumana nawo pa moyo wathu angachititse anthu ena kubwerera m’mbuyo kapena kusiya kuchita nawo utumiki wa kumunda. (Marko 4:18, 19) Mwina tingaone kuti anthu amene asiya kulalikira sakubwera pa misonkhano ya mpingo. Koma angakhale akukondabe Mulungu mumtima mwawo. Kodi n’chiyani chingachitike pofuna kulimbitsa chikhulupiriro chawo? Akulu angathandize mokoma mtima powayendera anthu oterowo. (Machitidwe 20:35) Anthu ena mumpingo angapemphedwenso kuthandiza. Kuwayenderako kukhoza kukhala kuti ndi mankhwala amene amafunikira, tingatero kunena kwake, polimbitsanso chikhulupiriro chawo chimene chinafooka.

14, 15. Kodi Paulo anapereka malangizo otani okhudza kulimbikitsa ena? Perekani chitsanzo cha mpingo wina umene unatsatira langizo limeneli.

14 Baibulo limatilimbikitsa kuti “limbikitsani amantha mtima, chirikizani ofooka.” (1 Atesalonika 5:14) Mwina “amantha mtima” kapena kuti ovutika maganizo oterowo amaona kuti kulimba mtima kwawo kukucheperachepera ndipo kuti sangathe kugonjetsa zopinga popanda kuthandizidwa. Kodi mungawathandize? Mawu akuti “chirikizani ofooka” amasuliridwanso kuti “kugwiritsa” kapena “kumamatira” wofooka. Yehova amakonda nkhosa zake zonse. Saziona ngati zosafunika kwenikweni, ndipo safuna kuti ina imusiye. Kodi mungathandize mpingo “kugwiritsa” ofooka mwauzimu mpaka atalimba?​—Ahebri 2:1.

15 Mkulu wina anapita kunyumba kwa banja lina limene linasiya kulalikira kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Mkuluyo analemba kuti: “Kuwaganizira mokoma mtima ndiponso mwachikondi kumene mpingo wonse unasonyeza kunawakhudza kwambiri moti zinawalimbikitsa kubwerera ku gulu.” Kodi mlongo wa m’banjalo amene sanali kulalikira anamva bwanji za kuyendera ena kumene anthu mumpingo anachita? Iye tsopano akuti: “Chimene chinatithandiza kuti tiyambenso kulalikira chinali chakuti abale amene anatichezerawo ngakhalenso alongo amene anali nawo limodzi sanali ndi maganizo otiweruza kapena otidzudzula. M’malo mwake, anali omvetsa ndipo anatilimbikitsa ndi Malemba.”

16. Kodi ndani amene ali wokonzeka nthaŵi iliyonse kuthandiza amene akufuna kutonthozedwa?

16 Inde, Mkristu woona mtima amakonda kutonthoza mtima ena. Ndipo zinthu zikasintha pa moyo wathu, abale athu angatitonthoze ifenso. Komabe, tiyenera kuzindikira kuti zingatheke kuti panthaŵi imene tikufuna thandizo, palibe munthu aliyense amene angatithandize. Koma pali Gwero limodzi la chitonthozo limene limakhalapo nthaŵi zonse, Yehova Mulungu, amene nthaŵi iliyonse amakhala wokonzeka kutithandiza.​—Salmo 27:10.

Yehova Ndiye Gwero Lalikulu la Chitonthozo

17, 18. Kodi Yehova anatonthoza motani Mwana wake, Yesu Kristu?

17 Yesu atakhomeredwa pa mtengo, anafuula kuti: “Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga.” (Luka 23:46) Ndiyeno anamwalira. Maola angapo chabe zimenezi zisanachitike, iye anamangidwa ndipo anzake enieni anamusiya n’kuthaŵa chifukwa cha mantha. (Mateyu 26:56) Yesu anatsala yekha ndi Gwero limodzi lokha la chilimbikitso, Atate wake wakumwamba. Komabe, kukhulupirira kwake Yehova sikunapite pachabe. Kukhulupirika kwa Yesu kwa Atate wake kunafupidwa pamene Yehova anamuthandiza mokhulupirika kapena kuti mwachifundo.​—Salmo 18:25.

18 Mu utumiki wonse wa Yesu padziko lapansi, Yehova anapatsa Mwana wake zimene anafunikira kuti akhalebe wokhulupirika mpaka pamene anamwalira. Mwachitsanzo, Yesu atangobatizidwa kumene, kusonyeza chiyambi cha utumiki wake, anamva mawu a Atate wake omuvomereza ndi kumutsimikizira kuti amamukonda. Yesu akafunika kuthandizidwa, Yehova ankatumiza angelo kuti amulimbikitse. Pamene Yesu anakumana ndi chiyeso chachikulu pamapeto a moyo wake padziko lapansi, Yehova anamvera kupemphera ndi kupembedzera kwake momuyanja. Mosakayika, zonsezi zinamutonthoza Yesu.​—Marko 1:11, 13; Luka 22:43.

19, 20. Kodi tingatsimikize bwanji kuti Yehova adzatilimbitsa panthaŵi imene tikufunika thandizo?

19 Yehova amafunanso kukhala Gwero lathu lalikulu la chitonthozo. (2 Mbiri 16:9) Popeza iye ndi Gwero lenileni la mphamvu zazikulu ndiponso wolimba mphamvu, angatitonthoze pamene tikufunika thandizo. (Yesaya 40:26) Nkhondo, umphaŵi, matenda, imfa, kapena kupanda ungwiro kwathu zingatichititse kuvutika maganizo kwambiri. Ngati mavuto a moyo akuoneka olemetsa monga ‘mdani wamphamvu,’ Yehova angakhale mphamvu yathu. (Salmo 18:17; Eksodo 15:2) Amatipatsa thandizo lamphamvu, mzimu wake woyera. Pogwiritsa ntchito mzimu wake, Yehova ‘angalimbitse olefuka’ kuti ‘auluke pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga.’​—Yesaya 40:29, 31.

20 Mzimu wa Mulungu ndiye chinthu champhamvu kwambiri kuposa china chilichonse m’chilengedwe chonse. Paulo anafotokoza kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” Inde, Atate wathu wachikondi wakumwamba angatipatse “ukulu woposa wamphamvu” kuti tipirire mavuto onse opweteka mpaka pamene adzapanga “zonse zikhale zatsopano” m’Paradaiso amene iye walonjeza yemwe watsala pang’ono kufika.​—Afilipi 4:13; 2 Akorinto 4:7; Chivumbulutso 21:4, 5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Buku lakuti Vine’s Complete Expository Dictionary of Old and New Testament Words, lolembedwa ndi W. E. Vine, limati: “Mneni wa liwuli [pa·re·go·riʹa] amanena za mankhwala amene amachepetsa ululu.”

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi abale ku Roma anakhala bwanji ‘otonthoza mtima’ kwa Paulo?

• Kodi tingakhale bwanji ‘otonthoza mtima’ mumpingo?

• Kodi ndi motani mmene Yehova alili Gwero lathu lalikulu la chitonthozo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Abale anakhala ‘otonthoza mtima’ kwa Paulo mwa kumuthandiza mokhulupirika, kumulimbikitsa, ndiponso kumutumikira

[Chithunzi patsamba 21]

Akulu amatsogolera polimbikitsa nkhosa