Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Gonjerani Mokhulupirika Ulamuliro Umene Mulungu Waika

Gonjerani Mokhulupirika Ulamuliro Umene Mulungu Waika

Gonjerani Mokhulupirika Ulamuliro Umene Mulungu Waika

“Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu.”​—YESAYA 33:22.

1. Kodi n’chiyani chinachititsa mtundu wa Israyeli kukhala wapadera?

MTUNDU wa Israyeli unakhazikitsidwa mu 1513 B.C.E. Panthaŵiyo, mtunduwu unalibe mzinda waukulu, dziko lawolawo, ndiponso mfumu yooneka ndi maso. Nzika zake zinali omwe kale anali akapolo. Komabe, mtundu watsopano umenewo unali wapadera m’njira inanso. Yehova Mulungu ndiye anali Woweruza, Wopereka malamulo, ndiponso Mfumu yawo yosaoneka. (Eksodo 19:5, 6; Yesaya 33:22) Palibe mtundu wina uliwonse umene ukananena kuti unali wapadera motero.

2. Kodi pali funso liti lokhudza mmene Israyeli anali kulamulidwira, ndipo n’chifukwa chiyani yankho lake n’lofunika kwambiri kwa ife?

2 Popeza Yehova ndi Mulungu wa dongosolo, ndiponso wa mtendere, tingayembekezere kuti mtundu uliwonse umene iye anali kuulamulira unali wolinganizidwa bwino. (1 Akorinto 14:33) Ndi mmenedi zinalili ndi Israyeli. Koma kodi gulu looneka la padziko lapansi lingalamulidwe bwanji ndi Mulungu wosaoneka? Tingachite bwino kupenda mmene Yehova analamulira mtundu wakale umenewo, ndi kuona makamaka mmene zochita zake ndi Israyeli zikusonyezera kufunika kogonjera mokhulupirika ulamuliro umene Mulungu waika.

Mmene Israyeli Wakale Anali Kulamulidwira

3. Kodi Yehova anakonza dongosolo lothandiza liti kuti atsogolere anthu ake?

3 Ngakhale kuti Yehova ndiye anali Mfumu yosaoneka ya Israyeli, iye anasankha amuna okhulupirika kukhala omuimira ooneka ndi maso. Panali akalonga, akulu a nyumba za makolo, ndi akulu amene anali kutumikira anthu monga aphungu ndi oweruza. (Eksodo 18:25, 26; Deuteronomo 1:15) Komabe, sitiyenera kuganiza kuti popanda Mulungu kutsogolera amuna amaudindowo bwenzi akuweruza mwanzeru ndi kumvetsa mwangwiro. Iwo sanali angwiro, ndipo sakanadziŵa zimene zinali m’mitima ya olambira anzawo. Komabe, oweruza oopa Mulungu ankatha kupereka uphungu wothandiza kwa okhulupirira anzawo chifukwa chakuti uphunguwo unali kuchokera m’Chilamulo cha Yehova.​—Deuteronomo 19:15; Salmo 119:97-100.

4. Kodi ndi makhalidwe achibadwa ati amene oweruza okhulupirika a Israyeli anafunika kuwapeŵa, ndipo chifukwa chiyani?

4 Komabe, oweruza anafunika kuchita zambiri osati kungodziŵa kokha Chilamulo. Popeza anali opanda ungwiro, akuluwo anafunika kupeŵa makhalidwe awo oipa achibadwa, monga kudzikonda, kukondera, ndi dyera, zimene zikanapotoza kaweruzidwe kawo. Mose anawauza kuti: ‘Musamasamalira munthu poweruza mlandu; aang’ono ndi aakulu muwamvere mmodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo n’cha Mulungu.’ Inde, oweruza a Israyeli anali kuweruza m’malo mwa Mulungu. Imeneyitu inali ntchito yapamwamba ndiponso yapadera!​—Deuteronomo 1:16, 17.

5. Kuphatikiza pa kuika oweruza, kodi ndi dongosolo lina liti limene Yehova anakonza kuti asamalire anthu ake?

5 Yehova anakonzanso dongosolo lina losamalira zofunika zauzimu za anthu ake. Ngakhale pamene anali asanafike ku Dziko Lolonjezedwa, iye anawalamula kumanga chihema, malo a kulambira koona. Iye anaikanso ansembe kuti aziphunzitsa Chilamulo, kupereka nsembe za nyama, ndiponso kufukiza m’mawa ndi madzulo. Mulungu anaika mkulu wake wa Mose, Aroni, kukhala mkulu wa ansembe woyamba wa Israyeli ndipo anaika ana a Aroni kuti azithandiza atate awo pa ntchito zimene ankagwira.​—Eksodo 28:1; Numeri 3:10; 2 Mbiri 13:10, 11.

6, 7. (a) Kodi panali ubale wotani pakati pa Alevi ansembe ndi amene sanali ansembe? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo yakuti Alevi anali kugwira ntchito zosiyanasiyana? (Akolose 3:23)

6 Kusamalira zosoŵa zauzimu za anthu miyandamiyanda inali ntchito yaikulu, ndipo ansembe anali ochepa. Motero, anakonza dongosolo loti anthu ena a m’fuko la Levi aziwathandiza. Yehova anauza Mose kuti: “Uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ochokera kwa ana a Israyeli.”​—Numeri 3:9, 39.

7 Alevi anawalinganiza bwino kwambiri. Anawagaŵa monga mwa mabanja awo atatu​—Agerisoni, Akohati, ndi Amerari​—ndipo banja lililonse linali ndi ntchito yake. (Numeri 3:14-17, 23-37) Ntchito zina mwina zinkaoneka zofunika kwambiri kuposa zina, komabe zonse zinali zofunika. Ntchito ya Alevi Achikohati inafunikira kuti azikhala pafupi ndi likasa lopatulika la chipangano ndi ziwiya za m’chihema. Komabe, Mlevi aliyense, kaya ndi Mkohati kapena ayi, anali ndi mwayi wa utumiki wabwino kwambiri. (Numeri 1:51, 53) N’zomvetsa chisoni kuti ena sanayamikire utumiki wawo. M’malo mogonjera ulamuliro umene Mulungu anaika, iwo sanakhutire nawo ndipo anayamba kunyada, kufuna maudindo, ndiponso kuchita nsanje. Mmodzi mwa iwo anali Mlevi wina dzina lake Kora.

“Kodi Mufunanso Ntchito ya Nsembe?”

8. (a) Kodi Kora anali ndani? (b) Kodi n’chiyani chiyenera kuti chinachititsa Kora kuwaona ansembe mwa umunthu?

8 Kora sanali mkulu wa nyumba ya makolo a Alevi, ndiponso sanali mkulu wa mabanja a Akohati. (Numeri 3:30, 32) Komabe, iye anali kalonga wolemekezeka mu Israyeli. Ntchito za Kora ziyenera kuti zinam’chititsa kukhala pafupi kwambiri ndi Aroni ndi ana ake. (Numeri 4:18, 19) Podzionera yekha kupanda ungwiro kwa amuna ameneŵa, Kora mwina anaganiza kuti: ‘Ansembe aŵa ndi opandiratu ungwiro, koma eti ndiyenera kuwagonjera! Si kale kwambiri pamene Aroni anapanga mwana wang’ombe wagolidi. Kupembedza mwana wang’ombeyo kunachititsa anthu athu kulambira mafano. Tsopano Aroni yemweyo, mbale wa Mose, ndi mkulu wa ansembe! Kukondera kwakeko inu! Nanga bwanji za ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu? Iwo sanalemekeze m’pang’ono pomwe mwayi wa utumiki umene anali nawo moti Yehova anawapha!’ * (Eksodo 32:1-5; Levitiko 10:1, 2) Kaya Kora anaganiza zotani, n’zoonekeratu kuti anayamba kuwaona ansembe mwa umunthu. Zimenezi zinam’chititsa kuukira Mose ndi Aroni ndipo, koposa ameneŵa, anaukira Yehova.​—1 Samueli 15:23; Yakobo 1:14, 15.

9, 10. Kodi Kora ndi anzake oukira anaimba Mose mlandu wotani, ndipo n’chifukwa chiyani sanayenera kuchita zimenezi?

9 Popeza anali munthu wodziŵika kwambiri, sikunali kovuta kuti Kora apeze anzake a maganizo ngati akewo. Iye, pamodzi ndi Datani ndi Abiramu, anapeza anzawo okwana 250 ndipo onsewo anali akalonga a khamulo. Onse pamodzi anapita kwa Mose ndi Aroni ndipo anati: “Khamu lonse n’lopatulika, onseŵa, ndipo Yehova ali pakati pawo; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?”​—Numeri 16:1-3.

10 Poganizira zimene anthuŵa anali kudziŵa kale, sanayenera kuukira ulamuliro wa Mose. Si kale kwambiri pamene Aroni ndi Miriamu anachitanso zimenezi. Eetu, iwonso anaganiza monga mmene Kora anachitira! Malinga ndi Numeri 12:1, 2, iwo anafunsa kuti: “Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? Sananenanso ndi ife nanga?” Yehova anali kumva. Iye analamula Mose, Aroni ndi Miriamu kuti asonkhane pakhomo la chihema chokumanira kuti akawasonyeze mtsogoleri amene Iye anasankha. Ndiyeno mosapita m’mbali, Yehova anati: “Pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m’masomphenya, ndinena naye m’kulota. Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m’nyumba mwanga monse.” Atatero, Yehova anakantha Miriamu ndi khate kwa kanthaŵi.​—Numeri 12:4-7, 10.

11. Kodi Mose anachita chiyani pa nkhani ya Kora?

11 Kora ndi anthu amene anali kumbali yake ayenera kuti anali kuidziŵa bwinobwino nkhani imeneyi. Panalibe zifukwa zoti aukire. Komabe, Mose anayesa kukambirana nawo moleza mtima. Anawalimbikitsa kuti aziyamikira kwambiri utumiki umene anali nawo. Iye anati: “Kodi muchiyesa chinthu chaching’ono, kuti Mulungu wa Israyeli anakusiyanitsani ku khamu la Israyeli, kukusendezani pafupi pa iye?” Ayi, sichinali “chinthu chaching’ono.” Alevi anali kale ndi zochita zambiri. N’chiyaninso china chimene akanafuna? Mawu otsatira a Mose anavumbula zimene anali kuganiza m’mitima yawo. Anati: “Kodi mufunanso ntchito ya nsembe?” * (Numeri 12:3; 16:9, 10) Koma kodi Yehova anachita chiyani anthuŵa ataukira ulamuliro umene iye anaika?

Woweruza wa Israyeli Analoŵererapo

12. Kodi kuti Israyeli akhalebe pa ubale wabwino ndi Mulungu zinadalira chiyani?

12 Yehova atapereka Chilamulo kwa Israyeli, anauza anthuwo kuti ngati akanamvera, akanakhala “mtundu wopatulika” ndipo mtunduwo ukanakhalabe wopatulika malinga ngati akanatsatira dongosolo la Yehova. (Eksodo 19:5, 6) Tsopano, popeza kuukira koonekeratu kunali m’kati, inali nthaŵi yoti Woweruza ndiponso Wopereka Malamulo wa Israyeli aloŵererepo. Mose anauza Kora kuti: “Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwoŵa, ndi Aroni; nimutenge munthu yense mbale yake yofukizamo, nimuike chofukiza m’mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yake yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana aŵiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yake yofukizamo.”​—Numeri 16:16, 17.

13. (a) N’chifukwa chiyani kunali kudzikuza kuti oukirawo afukize pamaso pa Yehova? (b) Kodi Yehova anachita nawo chiyani oukirawo?

13 Malinga ndi Chilamulo cha Mulungu, ansembe okha ndiwo ankayenera kufukiza. Mfundo yakuti Alevi amene sanali ansembe afukize pamaso pa Yehova ikanayenera kuwathandiza oukirawo kuganiza mofatsa. (Eksodo 30:7; Numeri 4:16) Koma Kora ndi om’tsatira ake sanachite zimenezo. M’maŵa mwake, iye “anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana [ndi Mose ndi Aroni] ku khomo la chihema chokomanako.” Nkhaniyo imatiuza kuti: “Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Dzipatuleni pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m’kamphindi.” Koma Mose ndi Aroni anapempha kuti asaphedwe anthu onse. Yehova anamvera pempho lawolo. Koma za Kora ndi gulu lake, “moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana aŵiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza.”​—Numeri 16:19-22, 35. *

14. N’chifukwa chiyani Yehova analanga msonkhano wa Israyeli?

14 N’zodabwitsa kuti Aisrayeli omwe anaona mmene Yehova anachitira ndi anthu oukirawo sanaphunzirepo kanthu. “M’mawa mwake khamu lonse la ana a Israyeli anadandaula pa Mose ndi Aroni, nati, Mwapha anthu a Yehova, inu.” Ha! Aisrayeli anali kumbali ya anthu achiwembu aja eti! Ndiyeno, kuleza mtima kwa Yehova kunafika pamapeto. Tsopano palibenso amene akanapempha m’malo mwa anthuwo, ngakhale Mose kapena Aroni. Yehova anabweretsa mliri kuti uwononge anthu osamverawo, ndipo “akufa nawo mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinayi mphambu mazana asanu ndi aŵiri, osaŵerenga aja adafera chija cha Kora.”​—Numeri 16:41-49.

15. (a) N’chifukwa chiyani Aisrayeli anayenera kutsatira utsogoleri wa Mose ndi Aroni mosanyinyirika? (b) Kodi nkhani imeneyi yakuphunzitsani chiyani za Yehova?

15 Anthu ameneŵa sakanataya miyoyo yawo ngati akanangoiganizira bwino nkhaniyi. Akanadzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi ndani amene anapita kwa Farao, kuika moyo wawo pachiswe? Ndani anapempha kuti Aisrayeli amasulidwe? Ndani yekha amene anauzidwa kuti akwere pa Phiri la Horebu Aisrayeli atalanditsidwa kuti akalankhule pamaso m’pamaso ndi mngelo wa Mulungu?’ Kunena zoona, mbiri yabwino ya Mose ndi Aroni inapereka umboni wa kukhulupirika kwawo kwa Yehova ndiponso kukonda kwawo anthu. (Eksodo 10:28; 19:24; 24:12-15) Yehova sizinam’sangalatse kupha anthu oukirawo. Komabe, zitaoneka kuti anthuwo akanapitiriza kuukira kwawoko, iye anachitapo kanthu mwamphamvu. (Ezekieli 33:11) Zonsezi zili ndi tanthauzo lalikulu kwa ife masiku ano. Chifukwa chiyani?

Kudziŵa Njira Masiku Ano

16. (a) Kodi ndi umboni wotani umene ukanathandiza Ayuda kukhulupirira kuti Yesu anali woimira Yehova? (b) Kodi Yehova anaika chiyani m’malo mwa ansembe Achilevi ndipo chifukwa chiyani?

16 Masiku ano, pali “mtundu” watsopano umene Yehova ndiye Woweruza, Wopereka Malamulo, ndiponso Mfumu yake yosaoneka. (Mateyu 21:43) “Mtundu” umenewo unakhazikitsidwa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Nthaŵi imeneyi isanafike, chihema cha m’nthaŵi ya Mose chinaloŵedwa m’malo ndi kachisi wokongola mu Yerusalemu, kumene Alevi anali kugwirabe ntchito yawo. (Luka 1:5, 8, 9) Komabe, m’chaka cha 29 C.E., kachisi wina, yemwe anali wauzimu, anakhazikitsidwa ndipo Yesu Kristu anakhala Mkulu wa Ansembe. (Ahebri 9:9, 11) Nkhani ya ulamuliro umene Mulungu anaika inabukanso. Kodi Yehova akanagwiritsa ntchito ndani kutsogolera “mtundu” watsopano umenewu? Yesu anali wokhulupirika kotheratu kwa Mulungu. Anakonda anthu. Anachitanso zizindikiro zodabwitsa zambirimbiri. Komabe, mofanana ndi makolo awo ouma khosi, Alevi ambiri anakana kumutsatira Yesu. (Mateyu 26:63-68; Machitidwe 4:5, 6, 18; 5:17) Motero, Yehova anaika ansembe achifumu m’malo mwa ansembe Achilevi aja. Ansembe achifumu ameneŵa akupitirizabe mpaka pano.

17. (a) Kodi ndi gulu liti limene lili ansembe achifumu masiku ano? (b) Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji ansembe achifumu?

17 Kodi ndani amene ali ansembe achifumu ameneŵa masiku ano? Mtumwi Petro anayankha funso limenelo m’kalata yake youziridwa yoyamba. Petro analembera ziwalo zodzozedwa za thupi la Kristu kuti: “Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.” (1 Petro 2:9) Malinga ndi mawu ameneŵa, n’zoonekeratu kuti, monga gulu, odzozedwa otsatira mapazi a Kristu ndiwo “ansembe achifumu” amenenso Petro anawatcha kuti “mtundu woyera mtima.” Iwo ndiwo njira imene Yehova amagwiritsa ntchito pophunzitsa anthu ake ndi kuwapatsa malangizo auzimu.​—Mateyu 24:45-47.

18. Kodi pali mgwirizano wotani pakati pa akulu oikidwa ndi ansembe achifumu?

18 Ansembe achifumuwo amaimiridwa ndi akulu oikidwa amene ali ndi udindo m’mipingo ya anthu a Yehova padziko lonse. Amuna ameneŵa tiyenera kuwalemekeza ndi kuwathandiza ndi mtima wonse, kaya ndi odzozedwa kapena ayi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti, mwa mzimu wake woyera, Yehova waika akuluwo pa udindo umenewo. (Ahebri 13:7, 17) Kodi zingatheke bwanji zimenezo?

19. Kodi akulu amaikidwa ndi mzimu woyera m’njira yotani?

19 Akulu ameneŵa amakwaniritsa ziyeneretso zimene zili m’Mawu a Mulungu, omwe anauziridwa ndi mzimu wake. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9) N’chifukwa chake tinganene kuti amaikidwa ndi mzimu woyera. (Machitidwe 20:28) Akulu ayenera kudziŵa bwino Mawu a Mulungu. Mofanana ndi Woweruza Wamkulu amene anawaika, akulu ayenera kudana ndi kuweruza kulikonse kooneka kuti n’kokondera.​—Deuteronomo 10:17, 18.

20. Kodi mumayamikira chiyani kwa akulu ogwira ntchito molimbika?

20 Mmalo motsutsana ndi ulamuliro wawo, tiyenera kuyamikira akulu athu ogwira ntchito molimbika. Mbiri yawo yotumikira mokhulupirika, nthaŵi zambiri kwa zaka zochuluka, imatilimbikitsa kuwakhulupirira. Iwo mokhulupirika amakonzekera ndi kuchititsa misonkhano ya mpingo, kugwira nafe ntchito limodzi polalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu,’ ndiponso kutipatsa malangizo a m’Malemba pakafunika kutero. (Mateyu 24:14; Ahebri 10:23, 25; 1 Petro 5:2) Amabwera kudzationa tikadwala ndiponso amatitonthoza tikaonekedwa maliro. Amathandizira zinthu za Ufumu mokhulupirika ndiponso mopanda dyera. Ali ndi mzimu wa Yehova ndipo iye amawayanja.​—Agalatiya 5:22, 23.

21. Kodi akulu afunika kusamala chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?

21 Komabe, akulu ndi opanda ungwiro. Pozindikira kuti ali ndi zofooka, iwo sayesa kuchita ufumu pa gululo lomwe ndi “choloŵa cha Mulungu.” (NW) M’malo mwake, amadziona kukhala “antchito anzawo kuti abale awo akhale ndi chimwemwe.” (1 Petro 5:3; 2 Akorinto 1:24, NW) Akulu odzichepetsa ogwira ntchito molimbika amakonda Yehova, ndipo amadziŵa kuti akamutsanzira kwambiri, adzapindulitsanso kwambiri mpingo. Poganizira zimenezi, iwo amayesetsa nthaŵi zonse kutsanzira Mulungu mwa kukulitsa makhalidwe monga chikondi, chifundo, ndi kuleza mtima.

22. Kodi n’chifukwa chiyani kupenda nkhani ya Kora kwalimbikitsa chikhulupiriro chanu m’gulu la Yehova looneka ndi maso?

22 Ndife okondwa kuti Yehova ndiye Wolamulira wathu wosaoneka, Yesu Kristu ndiye Mkulu wathu wa Ansembe, ansembe achifumu odzozedwa ndiwo aphunzitsi athu, ndiponso akulu achikristu okhulupirika ndiwo alangizi athu. Ngakhale kuti palibe gulu lotsogoleredwa ndi anthu limene lingakhale langwiro, ndife okondwa kutumikira Mulungu pamodzi ndi okhulupirira anzathu okhulupirika, amene amagonjera ulamuliro woikidwa ndi Mulungu mokondwa!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Ana ena aŵiri a Aroni, Eleazara ndi Itamara, anapereka chitsanzo chabwino potumikira Yehova.​—Levitiko 10:6.

^ ndime 11 Anzake a Kora achiwembu, Datani ndi Abiramu, anali a fuko la Rubeni. Choncho, mwachionekere iwo sanali kufuna ntchito ya unsembe. M’malo mwake iwo anali kuipidwa ndi utsogoleri wa Mose ndiponso kuti mpaka pa nthaŵi imeneyo, anali asanaloŵebe m’Dziko Lolonjezedwa limene anali kuliyembekezera.​—Numeri 16:12-14.

^ ndime 13 M’nthaŵi za makolo akale, mwamuna aliyense anali kuimira mkazi wake ndi ana ake kwa Mulungu, ngakhalenso kupereka nsembe m’malo mwawo. (Genesis 8:20; 46:1; Yobu 1:5) Komabe, atakhazikitsa Chilamulo, Yehova anaika amuna a m’banja la Aroni kukhala ansembe kuti nsembe ziziperekedwa kudzera mwa iwo. Anthu oukira 250 amenewo mwachionekere sanafune kutsatira kusintha kwa zinthu kumeneku.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi ndi dongosolo lachikondi liti limene Yehova anakonza kuti asamalire Aisrayeli?

• N’chifukwa chiyani panalibe zifukwa zoti Kora aukire Mose ndi Aroni?

• Kodi tikuphunzira chiyani pa mmene Yehova anachitira ndi anthu oukirawo?

• Kodi tingachite chiyani kuti tisonyeze kuti timayamikira dongosolo la Yehova masiku ano?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi mumaona ntchito iliyonse yotumikira Yehova kukhala mwayi wamtengo wapatali?

[Chithunzi patsamba 10]

“Mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?”

[Chithunzi patsamba 13]

Akulu oikidwa amaimira ansembe achifumu