Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yehova Amalidalitsa Liti Khama la Munthu?

Kodi Yehova Amalidalitsa Liti Khama la Munthu?

 Kodi Yehova Amalidalitsa Liti Khama la Munthu?

“NDILEKE ndimuke, chifukwa kulikucha.”

“Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.”

“Dzina lako ndani?”

“Yakobo.”

“Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israyeli, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.”​Genesis 32:26-28.

Kukambirana kochititsa chidwi kumeneku kunachitika chifukwa cha mphamvu zimene Yakobo wa zaka 97 anaonetsa. Ngakhale kuti Baibulo silinena kuti Yakobo ankachita maseŵera olimbitsa thupi, iye analimbana ndi mngelo usiku wonse. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Yakobo ankaganizira kwambiri zomwe Yehova analonjeza makolo ake. Lonjezo limenelo linali choloŵa chake chauzimu.

Zaka zambiri mmbuyomo izi zisanachitike, Esau, mkulu wake wa Yakobo, anagulitsa ufulu wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi mbale ya mphodza. Tsopano Yakobo anamva kuti Esau akubwera ndi amuna 400. Mpake kuti Yakobo anali ndi nkhaŵa ndipo ankafuna kuti Yehova amutsimikizire zomwe anam’lonjeza kuti banja lake lidzapeza bwino m’dziko lapatsidya pa mtsinje wa Yordano. Yakobo mogwirizana ndi mapemphero ake anachitapo kanthu. Iye anatumiza mphatso zambiri kwa Esau amene anali kuyandikira. Anachitanso zinthu zina pofuna kudziteteza. Anagaŵa gulu lake m’magulu aŵiri ndiponso anaolotsa akazi ndi ana ake pa doko la Yaboki. Ndiyeno mwakhama ndiponso ndi misozi, analimbana ndi mngelo usiku wonse kuti ‘amudalitse.’​—Hoseya 12:4, NW; Genesis 32:1-32.

Taganizirani chitsanzo china choyambirira izi zisanachitike. Chitsanzochi n’cha Rakele mkazi wachiŵiri wa Yakobo ndiponso amene anali kumukonda kwambiri. Rakele ankadziŵa bwino kwambiri za lonjezo la Yehova loti adzadalitsa Yakobo. Mkulu wake Leya, mkazi woyamba wa Yakobo, anali atabereka ana aamuna anayi pamene Rakele anali wosabereka. (Genesis 29:31-35) Mmalo modzimvera chisoni, iye anapitiriza kumudandaulira Yehova m’pemphero ndiponso anachitapo kanthu mogwirizana ndi mapemphero akewo. Monga momwe linachitira kholo lake lakale Sara ndi Hagara, Rakele anapatsa Yakobo mdzakazi wake Biliha kuti akhale mkazi wake wachiŵiri kuti monga mmene Rakele ananenera, “inenso ndionerepo ana pa  iye.” * Biliha anabalira Yakobo ana aamuna aŵiri, Dani ndi Nafitali. Panthaŵi yomwe Nafitali ankabadwa, Rakele ananena za khama lomwe iye anachita. Anati: “Ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana.” Rakele anadalitsidwanso mwa kubereka ana aamuna akeake aŵiri, Yosefe ndi Benjamini.​—Genesis 30:1-8; 35:24.

N’chifukwa chiyani Yehova anadalitsa khama la Yakobo ndi Rakele? Chifukwa chakuti iwo anaika zofuna za Yehova patsogolo ndipo anaona choloŵa chawo kukhala chamtengo wapatali. Anapemphera moona mtima kuti Mulungu awadalitse pa moyo wawo ndipo anachitapo kanthu mogwirizana ndi zofuna zake ndiponso mogwirizana ndi mapemphero awo.

Monga anachitira Yakobo ndi Rakele, ambiri lerolino angavomereze kuti pamafunika khama kuti munthu alandire madalitso a Yehova. Nthaŵi zambiri, anthu a khama otereŵa amakumana ndi zinthu zopweteka, zogwetsa ulesi, ndiponso zokhumudwitsa. Mayi wina wachikristu dzina lake Elizabeti, anasimba khama lomwe anachita kuti ayambenso kupita kumisonkhano yachikristu atajomba nthaŵi yaitali. Zinali zomuvuta kwambiri kupita kumisonkhano chifukwa anali ndi ana aamuna aang’ono asanu, mwamuna wake anali wosakhulupirira, ndiponso Nyumba ya Ufumu inali kutali, mtunda wamakilomita 30. “Kudzimana kunali kofunika kuti ndizitha kupita kumisonkhano nthaŵi ndi nthaŵi. Ndinkadziŵa kuti kuchita zimenezi n’kopindulitsa kwa ine ndiponso kwa ana anga. Zinawathandiza kuona kuti kuchita zimenezi n’kwaphindu.” Yehova anadalitsa khama la mayiyu. Mwa ana ake aamuna atatu amene akutumikira mwakhama mumpingo wachikristu, aŵiri akuchita utumiki wanthaŵi zonse. Posonyeza kusangalala ndi kupita kwawo patsogolo mwauzimu, mayiyu anati: “Iwo akula kwambiri mwauzimu kundiposa ine.” Madalitso abwinotu kwambiri ameneŵa chifukwa cha khama lake!

Khama Limene Yehova Amadalitsa

Kunena zoona, khama ndiponso kugwira ntchito molimbika kuli ndi phindu lake. Tikagwira ntchito molimbika kwambiri m’pamenenso timakhala okhutira kwambiri pamapeto pake. Ndi mmene Yehova anatipangira anthufe. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.” (Mlaliki 3:13; 5:18, 19) Komabe, kuti tilandire madalitso a Mulungu tifunika kuonetsetsa kuti tikuchita khama pa zinthu zoyenera. Mwachitsanzo, kodi n’kwanzeru kuyembekeza madalitso a Yehova pa moyo wathu ngati tikuika zinthu zauzimu pa malo achiŵiri? Kodi Mkristu wodzipatulira angayembekezere madalitso a Yehova ngati atayamba ntchito inayake kapena kulola kukwezedwa pantchito, zomwe zingam’chititse kumaphonya macheza olimbitsa chikhulupiriro ndiponso malangizo pamisonkhano yachikristu?​—Ahebri 10:23-25.

Kugwira ntchito yolembedwa molimbika kwa moyo wonse n’cholinga choti ntchitoyo isathe kapena kufuna kupeza chuma sikungachititse munthu ‘kuona zabwino’ ngati akunyalanyaza zinthu zauzimu. Yesu m’fanizo lake la wofesa anafotokoza zotsatira za kuchita khama pa zinthu zosayenera. Pa za mbewu ‘yofesedwa paminga,’ Yesu ananena kuti, “uyu ndiye wakumva mawu;  ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mawu, ndipo akhala wopanda chipatso.” (Mateyu 13:22) Paulo anachenjezanso za msampha womwewo ndipo ananena kuti ofunafuna chuma “amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.” Kodi tingatani kuti tipeŵe moyo wotayika mwauzimu umenewo? Paulo anapitiriza kuti: ‘Thaŵa izi; usayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma yembekezera Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.’​—1 Timoteo 6:9, 11, 17.

Kaya tili ndi zaka zingati, kapena tatumikira Yehova kwanthaŵi yaitali bwanji, tonsefe tingapindule mwa kutsanzira khama la Yakobo ndi Rakele. Pofunafuna madalitso a Mulungu, iwo sanaiŵale m’pang’ono pomwe choloŵa chawo ndipo anachita zimenezi ngakhale anakumana ndi zinthu zoopsa ndiponso zokhumudwitsa. Masiku anonso, masautso ndiponso mavuto amene tikukumana nawo angakhale oopsa, okhumudwitsa ndiponso ogwetsa ulesi. Tingalakelake kungosiya nkhondo yathu yauzimu ndi kugonja kwa Satana. Iye angagwiritse ntchito njira iliyonse yomwe angathe kaya ndi zosangalatsa, maseŵera, zizoloŵezi, ntchito, kapena chuma, kuti akwaniritse zolinga zake. Munthu angaone ngati adzapeza zinthu zabwino koma nthaŵi zambiri sizimapezeka. Anthu amene amanyengedwa kufunafuna zinthu zotere nthaŵi zambiri mapeto ake amaloŵa m’mavuto. Monga anachitira Yakobo ndi Rakele, tiyeni tikulitse mzimu wakhama ndi kugonjetsa machenjera a Satana.

Mdyerekezi akufunitsitsa kuti tigonje basi, tikumaganiza kuti ‘mavutoŵa sadzatha. Palibe chomwe tingachite. Palibenso chifukwa chochitira khama.’ Choncho, tonsefe tifunika kusamala kuti tisakhale ndi malingaliro ofooketsa ameneŵa, tikumaganiza kuti ‘palibe amene amandikonda’ ndipo ‘Yehova wandiiŵala ine.’ Kukhala ndi malingaliro otereŵa n’kungodzivulaza. Kodi n’kutheka kuti mwina zimenezi zikusonyeza kuti tagwa mphwayi ndipo tasiyira panjira khama lathu tisanalandire madalitso? Kumbukirani kuti Yehova amadalitsa khama lathu.

Pitirizani Kuchita Khama Kuti Yehova Akudalitseni

Kuti moyo wathu wauzimu ukhale wabwino zimadalira kwambiri pa kudziŵa kwathu mfundo zazikulu ziŵiri izi zokhudza moyo wathu monga atumiki a Yehova. (1) Aliyense amakumana ndi mavuto, matenda, ndiponso zothetsa nzeru pa moyo. (2) Yehova amamva madandaulo a anthu amene amamupempha ndi mtima wonse kuti awathandize ndiponso kuwadalitsa.​—Eksodo 3:7-10; Yakobo 4:8, 10; 1 Petro 5:8, 9.

Kaya zinthu zikuvuteni motani kapena kuona ngati palibe chomwe mungachite, musagonjere ku ‘tchimoli lomwe limangotizinga’​—tchimo la kutaya chikhulupiriro. (Ahebri 12:1) Pitirizani kuchita khama mpaka mutalandira madalitso. Dikirani, mukumakumbukira Yakobo wokalambayo amene analimbana ndi mngelo usiku wonse kuti alandire madalitso. Mofanana ndi mlimi yemwe amadzala mbewu m’nyengo yachilimwe n’kudikira mpaka nyengo yokolola, dikirani madalitso a Yehova chifukwa cha ntchito zanu zauzimu, ngakhale mukuona ngati simunachite zambiri. (Yakobo 5:7, 8) Nthaŵi zonse kumbukirani mawu a wamasalmo aŵa: “Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.” (Salmo 126:5; Agalatiya 6:9) Khalani wosasunthika ndipo musachoke m’gulu la anthu a khama.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Kukhala ndi akazi apambali kunkachitika pangano la Chilamulo lisanakhazikitsidwe ndipo litakhazikitsidwa, kunakhalabe kovomerezeka ndipo panali Malamulo okhudza nkhani imeneyi. Mulungu sanaone kuti inali nthaŵi yabwino yobwezeretsa lamulo loyambirira lomwe anakhazikitsa m’munda wa Edene loti munthu azikhala ndi mkazi kapena mwamuna mmodzi, koma anadikira mpaka m’nthaŵi ya Yesu Kristu. Komabe Iye anateteza akazi apambaliwo mwa kuika malamulo okhudza iwo. Akazi ameneŵa anathandiza kwambiri kuti mtundu wa Israyeli uchulukane mofulumira.