Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Zipembedzo

Zipembedzo

N’chifukwa chiyani pali zipembedzo zambiri chonchi?

“Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu, ndi kuumirira mwambo wa anthu.”Maliko 7:8.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Anthufe mwachibadwa timafunika zinthu “zauzimu” ndipo timazipeza tikamalambira Mulungu. (Mateyu 5:3) Pofuna kukwaniritsa zimenezi, anthu ambiri ayambitsa zipembedzo zosiyanasiyana. Koma vuto ndi loti zipembedzo zimene anthu amayambitsazi, zimaphunzitsa maganizo a anthu osati zimene Mulungu amafuna.

Mwachitsanzo, Baibulo limanena zokhudza anthu ena m’nthawi ya atumwi omwe anali m’chipembedzo chinachake. Limati anthuwa anali ‘odzipereka potumikira Mulungu, koma sankamudziwa molondola. Ndipo posadziwa chilungamo cha Mulungu, iwo sanagonjere chilungamocho koma anayesetsa kukhazikitsa chawochawo.’ (Aroma 10:2, 3) Masiku anonso pali zipembedzo zambiri zimene ‘zimaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.’—Maliko 7:7.

 Kodi kukhala m’chipembedzo chinachake n’kofunika?

“Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.”Aheberi 10:24, 25.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Palemba la Aheberi 10:25 pali mawu akuti, “tisaleke kusonkhana pamodzi.” Mawu amenewa akusonyeza kuti Mulungu amafuna pakhale gulu la anthu kuti azisonkhana pamodzi n’kumamulambira. Kodi munthu aliyense ayenera kukhala ndi zikhulupiriro zakezake zokhudza Mulungu komanso zimene Mulunguyo amafuna kuti tizichita? Ayi, chifukwa Baibulo limanena kuti anthu amene amalambira Mulungu moyenera, ayenera ‘kumalankhula mogwirizana’ komanso kukhala “ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.” (1 Akorinto 1:10) Ayenera kukhala m’mipingo komanso ‘kukonda gulu lonse la abale’ lapadziko lonse lapansi. (1 Petulo 2:17; 1 Akorinto 11:16) Mulungu amasangalala ndi kulambira kotereku.

Kodi n’zotheka kudziwa chipembedzo choona?

“Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”Yohane 13:35.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Pofuna kutithandiza kudziwa chipembedzo choona, Baibulo limayerekezera zipembedzo ndi mitengo. Limati: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Anthu sathyola mphesa paminga kapena nkhuyu pamitula, amatero kodi?” (Mateyu 7:16) Simungachite kufunikira kukhala katswiri wodziwa za mitengo kuti muthe kusiyanitsa mtengo wa nkhuyu ndi mtengo wa mitula. N’chimodzimodzinso ndi zipembedzo. Simufunika kuchita kukhala katswiri wa zachipembedzo kuti muthe kusiyanitsa pakati pa chipembedzo choona ndi chabodza. Ndiye kodi zina mwa zipatso kapena kuti zizindikiro za chipembedzo choona ndi ziti?

  • Chipembedzo choona chimaphunzitsa choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. (Yohane 4:24; 17:17) Sichiphunzitsa maganizo a anthu.

  • Chipembedzo choona chimathandiza anthu kudziwa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova komanso kudziwa zambiri zokhudza Mulunguyo.—Yohane 17:3, 6.

  • Chipembedzo choona chimauza anthu kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto amene anthu akukumana nawo, osati maboma a anthu.—Mateyu 10:7; 24:14.

  • Chipembedzo choona chimalimbikitsa anthu kuti azikondana. (Yohane 13:35) Chimaphunzitsa anthu kuti asamasankhane mitundu, azigwiritsa ntchito nthawi yawo ndi zinthu zawo kuthandiza ena komanso kuti asamachite nawo nkhondo.—Mika 4:1-4.

  • Anthu a m’chipembedzo choona nthawi zonse amatsatira zimene amaphunzira ndipo sachita zosiyana ndi zimene amalalikira.—Aroma 2:21; 1 Yohane 3:18.

A Mboni za Yehova, omwe ndi amene amafalitsa magaziniyi, amayesetsa kulemekeza Mulungu mwa zolankhula ndi zochita zawo. Tikukupemphani kuti mukasonkhane nawo ku Nyumba ya Ufumu kuti mukaone nokha zimenezi.