Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | ACHINYAMATA

Kodi Mungasonyeze Bwanji Khalidwe Labwino Mukamatumiza ndi Kulandira Mameseji pa Foni?

Kodi Mungasonyeze Bwanji Khalidwe Labwino Mukamatumiza ndi Kulandira Mameseji pa Foni?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Tiyerekeze kuti mukucheza ndi mnzanu, ndipo pafoni yanu pabwera meseji. Kodi mungatani?

  1. Kuwerenga mesejiyo kwinaku mukulankhula ndi mnzanuyo.

  2. Kupempha mnzanuyo kuti akudikireni kaye, n’kuyamba kuwerenga mesejiyo.

  3. Kupitiriza kucheza ndi mnzanuyo, osawerenga mesejiyo.

Zimene mungasankhe kuchita pamenepa zingasonyeze ngati mumalemekeza mnzanuyo kapena ayi.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Kulembera meseji mnzanu nthawi imene mukucheza ndi mnzanu winanso, kuli ngati kuchita masewera amene mumawakonda mosatsatira malamulo a masewerawo. Mwina mungaganize kuti, ‘Palibe vuto poti onsewa ndi anzanga.’ Koma kodi anzanuwo ndiye safuna kupatsidwa ulemu? N’zoona kuti munthu amatha kuchita zinthu momasuka akakhala ndi anzake. Koma dziwani kuti, ngati simulemekeza anzanu, ubwenzi wanu ndi anzanuwo ukhoza kutha.

N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa palibe munthu amene amasangalala akamachitiridwa zinthu mwamwano. Mtsikana wina, dzina lake Beth, * ananena kuti, “Zimandikhumudwitsa mnzanga akamacheza nane kwinaku akuwerenga mameseji pa foni yake. Ndimangoona ngati sakusangalala kucheza nane.” Kodi mukuganiza kuti ubwenzi wa Beth ndi mnzakeyu ungapite patali?

Ganizirani zimene inuyo mumachita pa nkhani yolemba komanso kulandira mameseji, ndipo kenako onaninso zomwe zili pansi pa kamutu kakuti, “Vuto Limene Limakhalapo.” Kodi inuyo mukanachita chiyani? N’kutheka kuti mwaona zoti si ulemu kuchita zimene zili pa A. Koma kodi zaulemu ndi ziti pakati pa zimene zalembedwa pa B ndi C? Kodi mukuona kuti n’kupanda ulemu kusiya kaye kucheza ndi mnzanu kuti muwerenge meseji? Kapena mukuganiza kuti si bwino kumangopitiriza kucheza ndi mnzanuyo osawerenga kaye meseji imene mwalandira?

Apatu n’zoonekeratu kuti nthawi zina zingakhale zovuta kudziwa kuti zoyenera ndi ziti. Koma Baibulo lingakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita. Lemba la Luka 6:31 limati: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.” Kodi mungagwiritse ntchito bwanji malangizo amenewa pa nkhani yolemba ndi kulandira mameseji?

 ZIMENE MUNGACHITE

Muzilemba mameseji nthawi yoyenera. Mnyamata wina, dzina lake Richard, ananena kuti: “Nthawi zina anzanga amanditumizira meseji usiku nditagona. Zimene amalemba zimakhala zosafunika moti zimangondisokoneza tulo basi.” Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimalembera anthu mameseji pa nthawi yoti agona?’—Lemba lothandiza: Mlaliki 3:1.

Muzilemba mawu aulemu. Tikamalankhula ndi munthu, zinthu monga mawu amene tikugwiritsa ntchito, mmene akumvekera komanso mmene nkhope yathu ikuonekera, zimathandiza munthuyo kudziwa zimene tikutanthauza. Koma zinthu zimenezi sizioneka pa meseji. Ndiye kodi mungatani? Mtsikana wina, dzina lake Jasmine, ananena kuti: “Ndi bwino kugwiritsa ntchito mawu aulemu, osonyeza kupempha komanso osonyeza kuyamikira.” —Lemba lothandiza: Akolose 4:6.

Muzichita zinthu mozindikira. Onaninso zimene zili pakamutu kakuti, “Vuto Limene Limakhalapo.” Ngati mukuyembekezera meseji yofunika kwambiri ndipo mesejiyo yafika pa nthawi imene mukucheza ndi mnzanu, zingakhale bwino kupempha mnzanuyo kuti akudikireni n’cholinga choti muwerenge kaye mesejiyo. Koma mameseji ambiri amakhala oti mukhoza kuwerenga nthawi ina. Mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Amy, ananena kuti, “Meseji singadandaule utaiwerenga mochedwa koma mnzako akhoza kudandaula ngati wasiya kulankhula naye n’kuyamba kuwerenga meseji.” Mungachitenso bwino kupewa kulemba mameseji mukakhala pagulu. Mtsikana wina, wazaka 18 dzina lake Jane, ananena kuti: “Si bwino kumangokhalira kulemba mameseji. Zimakhala ngati ukuuza anzakowo kuti, ‘mukundibowa. Bola ndizicheza ndi anthu ena pafoni.’”

Muzionetsetsa zimene mwalemba musanatumize. Muzidzifunsa kuti, “Kodi akamvetsa zimene ndikutanthauza?” Mwina kuika zizindikiro zosonyeza kusangalala kungathandize kuti mnzanuyo amvetse zimene mukutanthauza. Mtsikana wina wazaka 21, dzina lake Amber, ananena kuti: “Munthu akhoza kutumizira mnzake meseji yongocheza, mnzakeyo n’kuganiza kuti akunena zenizeni. Zikatere amatha kukhumudwitsana mwinanso mpaka kukangana.—Lemba lothandiza: Miyambo 12:18.

Choncho ndi bwino kuganiziranso zimene mumachita pa nkhani ya kutumiza ndi kulandira mameseji.

Dziwani izi: Chikondi n’chimene chimapangitsa munthu kuti azilemekeza anzake. Kodi mungasonyeze bwanji khalidwe limeneli? Baibulo limati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya.” (1 Akorinto 13:4, 5) Pa nkhani ya chikondiyi, kodi inuyo mukuona kuti ndi zinthu ziti zimene mukuyenera kumachita?

^ ndime 11 Mayina ena m’nkhaniyi tawasintha.