Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Ireland

Dziko la Ireland

DZIKO la Ireland ndi chilumba ndipo limadziwikanso kuti Emerald Isle. Chilumbachi chapangidwa ndi mayiko awiri. Loyamba ndi la Republic of Ireland, lomwe ndiye lalikulu, ndipo lina ndi la Northern Ireland, lomwenso ndi mbali ya United Kingdom.

Malo otchedwa Giant Causeway

Dziko la Ireland limatchedwa kuti Emerald Isle chifukwa choti kumagwa mvula yambiri imene imapangitsa kuti kuzikhala zomera zobiriwira nthawi zonse. Dzikoli limaonekanso lokongola chifukwa choti lili ndi nyanja, mitsinje, malo okwera komanso mapiri.

Nyumba yaudzu

Pa nthawi ina m’mbuyomu, m’dzikoli munali mavuto adzaoneni. Mwachitsanzo, anthu ena amati kuyambira mu 1845 mpaka 1851, anthu pafupifupi 1 miliyoni anafa chifukwa cha matenda komanso njala. Izi zinachitika chifukwa choti mbatata yakachewere, yomwe anthu a m’dzikoli amadalira kwambiri, inagwidwa ndi matenda. Chifukwa choti m’dzikoli munali umphawi wadzaoneni, anthu ambiri anasamukira m’mayiko ena monga Australia, Britain, Canada ndi United States. Masiku ano anthu pafupifupi 35 miliyoni a ku America, makolo awo ndi a ku Ireland.

Anthu a ku Ireland amadziwika kuti ndi ansangala komanso okonda kuchereza alendo. Anthuwa amakonda kukwera mahatchi, kusewera mpira wamiyendo ndi wamanja  komanso kuchita masewera ena osiyanasiyana. Azimayi amakonda kuchita masewera enaake otchedwa camogie, omwe ndi ofanana ndi hockey.

Anthuwa amakonda kucheza ndipo amakondanso nyimbo. Pali gule wina wa ku Ireland yemwe ndi wotchuka padziko lonse. Povina guleyu, munthu sagwedera kuyambira m’chiuno kumapita kumtunda koma amavinitsa miyendo ndi mapazi ake mofulumira ndi mwadongosolo kwambiri.

Gulu loimba la ku Ireland

A Mboni za Yehova akhala akupezeka ku Ireland kwa zaka zoposa 100. Panopa m’dzikoli muli a Mboni oposa 6,000 ndipo akugwira mwakhama ntchito yawo yothandiza anthu kuphunzira Baibulo.

Poimba nyimbo, anthu a ku Ireland amagwiritsa ntchito azeze, zitoliro, mawezulo, makodiyoni, ng’oma ndi zina.

KODI MUKUDZIWA?

Malo enaake otchedwa Giant’s Causeway, omwe ali kumpoto kwa Northern Ireland anapangidwa ndi miyala imene inabwera chifukwa cha chiphalaphala chomwe chinaphulika kuchokera pansi pa nyanja ndipo chitazizira chinapanga miyalayi.