Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Pali Vuto Ngati Munthu Atakhala Kuti Sali M’chipembedzo Chilichonse?

Kodi Pali Vuto Ngati Munthu Atakhala Kuti Sali M’chipembedzo Chilichonse?

Yankho la m’Baibulo

 Inde pali vuto. Tikutero chifukwa Mulungu amafuna kuti anthu azimulambira monga gulu. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.”​—Aheberi 10:24, 25.

 Zimene Yesu ananena zinasonyezanso kuti otsatira ake ayenera kumalambira Mulungu monga gulu. Iye anawauza kuti: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:35) Zimenezi zikanakhala zosatheka ngati akanakhala kuti aliyense amangochita zinthu yekha. Choncho nthawi zonse ankayenera kumasonkhana m’mipingo yosiyanasiyana kuti alambire Mulungu. (1 Akorinto 16:19) Ndiyeno mipingo imeneyi inkakhala ngati gulu limodzi la padziko lonse.​—1 Petulo 2:17.

Kungokhala m’chipembedzo chinachake si kokwanira

 Monga taonera kale, Mulungu amafuna kuti tizimulambira monga gulu. Komabe, si kuti Mulungu angamasangalale nafe ngati titangokhala m’chipembedzo chinachake basi. Ngati timafuna kuti Mulungu azisangalala nafe, tiyenera kumachita zinthu mogwirizana ndi zimene timaphunzira. Pa nkhani imeneyi Baibulo limati: “Kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’masautso awo, ndi kukhala wopanda banga la dzikoli.”​—Yakobo 1:27.