Pitani ku nkhani yake

Kodi Ndingachidziwe Bwanji Chipembedzo Cholondola?

Kodi Ndingachidziwe Bwanji Chipembedzo Cholondola?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo lingatithandize kudziwa anthu amene ali m’chipembedzo cholondola kapena ayi. Limanena kuti chipembedzo chili ngati mtengo. Limati: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Anthu sathyola mphesa paminga kapena nkhuyu pamitula, amatero kodi?” (Mateyu 7:16) Mtengo uliwonse wabwino umabereka zipatso zabwino pomwe mtengo woipa subereka zipatso zabwino. Choncho tingachidziwe chipembedzo cholondola poyang’ana zipatso zimene chipembedzocho chimatulutsa. Chipembedzo cholondola chimachita zinthu zotsatirazi.

  1.   Anthu amene ali m’chipembedzo cholondola amaphunzitsa mfundo zochokera m’Baibulo, osati za m’mutu mwawo. (Yohane 4:24; 17:17) Amaphunzitsa mfundo zolondola zokhudza mzimu komanso zoti anthu adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. (Salimo 37:29; Yesaya 35:5, 6; Ezekieli 18:4) Anthu a m’chipembedzo cholondola amalengeza poyera zimene zipembedzo zabodza zimachita.—Mateyu 15:9; 23:27, 28.

  2.   Anthu a m’chipembedzo cholondola amathandiza anthu kudziwa Mulungu komanso dzina lake, lomwe ndi Yehova. (Salimo 83:18; Yesaya 42:8; Yohane 17:3, 6) Chipembedzo cholondola chimathandiza anthu kudziwa kuti n’zotheka kumudziwa bwino Mulungu ndiponso kukhala naye paubwenzi.—Yakobo 4:8.

  3.   Anthu a m’chipembedzo cholondola amakhulupirira kuti Mulungu anagwiritsa ntchito Yesu kuti anthu adzapulumuke. (Machitidwe 4:10, 12) Amayesetsanso kumvera malamulo amene Yesu anapereka komanso kutengera chitsanzo chake.—Yohane 13:15; 15:14.

  4.   Anthu a m’chipembedzo cholondola amaona kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto a anthu ndipo amauza ena zokhudza Ufumuwu.—Mateyu 10:7; 24:14.

  5.   Anthu a m’chipembedzo cholondola amakondana ndi mtima wonse. (Yohane 13:35) Amakonda komanso kulemekeza anthu amitundu, zikhalidwe, zinenero ndiponso ochokera kosiyanasiyana. (Machitidwe 10:34, 35) Samenya nawo nkhondo chifukwa amakondana.—Mika 4:3; 1 Yohane 3:11, 12.

  6.   Atsogoleri a m’chipembedzo cholondola salandira malipiro aliwonse, ndipo sapatsidwa mayina aulemu.—Mateyu 23:8-12; 1 Petulo 5:2, 3.

  7.   Anthu a m’chipembedzo cholondola salowerera ndale. (Yohane 17:16; 18:36) Komabe iwo amayesetsa kulemekeza komanso kumvera olamulira a m’dziko limene akukhala. Amayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara [kutanthauza olamulira a dziko], koma zinthu za Mulungu muzizipereka kwa Mulungu.”—Maliko 12:17; Aroma 13:1, 2.

  8.   Anthu a m’chipembedzo cholondola sikuti amangochita miyambo yachipembedzo basi. Koma amayesetsa kutsatira mfundo za makhalidwe abwino pa moyo wawo. (Aefeso 5:3-5; 1 Yohane 3:18) Nawonso anthu a m’chipembedzo cholondola amasangalala akamalambira Mulungu wawo, yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe.”—1 Timoteyo 1:11.

  9.   Anthu a m’chipembedzo cholondola ndi ochepa. (Mateyu 7:13, 14) Anthu amenewa amanyozedwa komanso kuzunzidwa chifukwa chochita zimene Mulungu amafuna.—Mateyu 5:10-12.

Munthu sangadziwe chipembedzo cholondola pongotengera mmene iyeyo akuchionera

 Zingakhale zovuta kwambiri kudziwa chipembedzo cholondola pongotengera mmene ifeyo tikuchionera. Baibulo linaneneratu kuti anthu “adzadzipezera aphunzitsi [achipembedzo] kuti amve zowakomera m’khutu.” (2 Timoteyo 4:3) Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limatilimbikitsa kukhala m’chipembedzo chomwe ndi ‘choyera ndi chosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu’ ngakhale chipembedzocho chitakhala kuti ndi chosatchuka.—Yakobo 1:27; Yohane 15:18, 19.