Pitani ku nkhani yake

Kodi Muli ndi Abusa Amene Amalipidwa?

Kodi Muli ndi Abusa Amene Amalipidwa?

Potsatira chitsanzo cha Akhristu a m’nthawi ya atumwi, m’gulu la Mboni za Yehova simukhala anthu ena amene amaonedwa kuti ndi apamwamba monga abusa. Akhristu onse obatizidwa amakhala odzipereka ndipo amagwira nawo ntchito yolalikira ndiponso kuphunzitsa anthu mawu a Mulungu. Mpingo uliwonse wa Mboni za Yehova umakhala ndi anthu pafupifupi 100. Mumpingo uliwonse mumakhala amuna odziwa bwino Baibulo ndipo amatumikira monga “akulu.” (Tito 1:5) Ndipo iwo salipidwa chifukwa cha utumiki wawo.