Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka 4:1-44

  • Mdyelekezi ayesa Yesu (1-13)

  • Yesu ayamba kulalikila ku Galileya (14, 15)

  • Yesu akanidwa ku Nazareti (16-30)

  • Zimene zinacitika m’sunagoge ku Kaperenao (31-37)

  • Apongozi aakazi a Simoni ndi anthu ena acilitsidwa (38-41)

  • Khamu la anthu lipeza Yesu ku malo opanda anthu (42-44)

4  Yesu atadzazidwa ndi mzimu woyela, anacoka ku Yorodano, ndipo mzimuwo unali kumutsogolela uku ndi uku m’cipululu 2  kwa masiku 40. Kumeneko Mdyelekezi anali kumuyesa. Yesu sanadye ciliconse pa masiku amenewo. Conco masikuwo atatha, anamva njala. 3  Mdyelekezi ataona izi anamuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mtanda wamkate.” 4  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha ai.’” 5  Conco anapita naye pa malo okwela n’kumuonetsa maufumu onse a padziko lapansi m’kanthawi kocepa. 6  Ndiyeno Mdyelekezi anamuuza kuti: “Ulamulilo wonsewu ndi ulemelelo wake ndikupatsani cifukwa zinapelekedwa kwa ine, ndipo ndingazipeleke kwa aliyense amene ndafuna. 7  Conco ngati mungagwade pansi ndi kundilambilako kamodzi kokha, zonsezi zikhala zanu.” 8  Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.’” 9  Ndiyeno anapita naye ku Yerusalemu n’kumukwezeka pamwamba penipeni pa* kacisi. Kenako anamuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, dziponyeni pansi kucokela pano, 10  cifukwa Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake za inu kuti akutetezeni,’ 11  ndipo, ‘Iwo adzakunyamulani ndi manja ao kuti phazi lanu lisagunde mwala.’” 12  Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Usamuyese Yehova* Mulungu wako.’” 13  Conco Mdyelekezi atatsiliza mayeselo onsewo anacoka n’kumusiya, ndipo anayembekezela nthawi ina yabwino. 14  Tsopano Yesu atadzazidwa ndi mphamvu ya mzimu anabwelela ku Galileya. Ndipo mbili yake yabwino inafalikila m’madela onse ozungulila. 15  Komanso iye anayamba kuphunzitsa m’masunagoge ao, ndipo anthu onse anali kumulemekeza. 16  Ndiyeno anapita ku Nazareti kumene anakulila. Mwacizolowezi cake, pa tsiku la Sabata analowa m’sunagoge ndi kuimilila kuti awelenge. 17  Conco anamupatsa mpukutu wa mneneli Yesaya. Iye anautambasula ndipo anapeza pamene panalembedwa mau akuti: 18  “Mzimu wa Yehova* uli pa ine cifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kuti ndilengeze za ufulu kwa anthu ogwidwa ukapolo, komanso kuti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula anthu opondelezedwa, 19  ndi kudzalalikila za caka cobvomelezeka ca Yehova.”* 20  Atatelo, anapinda mpukutuwo n’kuubweza kwa mtumiki wa m’sunagogemo. Kenako anakhala pansi. Maso a anthu onse m’sunagogemo anangoti dwii pa iye. 21  Ndiyeno anayamba kuwauza kuti: “Lelo, lemba limene mwangolimva kumeneli lakwanilitsidwa.” 22  Anthu onsewo anayamba kum’tamanda ndipo anadabwa ndi mau otsitsimula otuluka pakamwa pake. Iwo anali kufunsana kuti: “Kodi ameneyu si mwana wa Yosefe?” 23  Iye atamva zimenezi anawauza kuti: “Mosakaikila, mudzakamba mwambi uwu pa ine wakuti ‘Iwe wocilitsa anthu, dzicilitse wekha. Zinthu zimene tinamva kuti unazicita ku Kaperenao, uzicitenso kuno kwanu.’” 24  Conco iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, palibe mneneli amene amalandilidwa kwao. 25  Mwacitsanzo, ndithu ndikukuuzani kuti: Mu Isiraeli munali akazi ambili amasiye m’masiku a Eliya pamene kumwamba kunatsekedwa kwa zaka zitatu ndi miyezi 6, ndipo m’dziko lonselo munagwa njala yaikulu. 26  Koma Eliya sanatumizidwe kwa aliyense wa akaziwo. M’malomwake, anatumizidwa kwa mkazi wamasiye wa ku Zarefati m’dziko la Sidoni. 27  Komanso m’nthawi ya mneneli Elisa, mu Isiraeli munali anthu ambili akhate. Koma palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anacilitsidwa,* kupatulapo Namani wa ku Siriya.” 28  Tsopano onse amene anali kumvetsela zimenezi m’sunagogemo anakwiya kwambili. 29  Iwo ananyamuka ndipo mofulumila anamutulutsila kunja kwa mzinda. Kenako anapita naye pamwamba pa phili pamene panamangidwa mzinda wao, kuti akamuponye kuphompho. 30  Koma iye anangodutsa pakati pao n’kumapita. 31  Ndiyeno anapita ku Kaperenao, mzinda wa ku Galileya. Ndipo anali kuphunzitsa anthu pa Sabata. 32  Anthuwo anadabwa kwambili ndi kaphunzitsidwe kake cifukwa anali kukamba mwaulamulilo. 33  Tsopano m’sunagogemo munali munthu wina wogwidwa ndi mzimu, inde ciwanda conyansa. Munthuyo anali kukuwa mwamphamvu kuti: 34  “Aa! Mufuna ciani kwa ife inu Yesu Mnazareti? Kodi mwabwela kudzationonga? Ine ndikudziwa bwino kuti ndinu Woyela wa Mulungu.” 35  Koma Yesu anaudzudzula mzimuwo kuti: “Khala cete, ndipo tuluka mwa iye.” Pamenepo ciwandaco cinamugwetsela pansi munthuyo pakati pao, basi n’kutuluka mwa iye popanda kumubvulaza. 36  Anthu onsewo ataona izi, anadabwa kwambili, ndipo anayamba kukambilana kuti: “Onani, mau ake ndi amphamvu kwambili cifukwa mwa ulamulilo ndi mphamvu akulamula mizimu yonyansa kutuluka, ndipo ikutulukadi!” 37  Conco mbili yake inafalikila paliponse m’madela onse ozungulila. 38  Atatuluka m’sunagoge muja, anakalowa m’nyumba ya Simoni. Pa nthawiyo, apongozi aakazi a Simoni anali kudwala malungo aakulu. Conco iwo anamupempha kuti awathandize. 39  Ndiyeno iye anaimilila pafupi ndi maiwo n’kudzudzula malungowo, ndipo malungowo anathelatu. Nthawi yomweyo maiwo anauka n’kuyamba kuwakonzela cakudya. 40  Koma pamene dzuwa linali kulowa, onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyana-siyana anawabweletsa kwa iye. Ndipo anawacilitsa mwa kuika manja ake pa aliyense wa iwo. 41  Nazonso ziwanda zinatuluka mwa anthu ambili zikupfuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” Koma anali kuzidzudzula ndipo sanali kuzilola kuti zilankhule, cifukwa zinali kumudziwa kuti ndi Khristu. 42  Kutaca m’mawa, iye anacoka n’kupita ku malo opanda anthu. Koma khamu la anthu linayamba kumufuna-funa,* mpaka anafika kumene iye anali. Ndipo iwo anamucondelela kuti asawasiye. 43  Koma iye anawauza kuti: “Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso, cifukwa n’zimene ndinatumidwa kudzacita.” 44  Atatelo, anapita kukalalikila m’masunagoge a ku Yudeya.

Mau a m'Munsi

^ Kapena kuti, “pamwamba pa mpanda wa.”
^ Kapena kuti, “anayeletsedwa.”
^ Kapena kuti, “kumusaka-saka.”