Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka 13:1-35

  • Lapani, apo ai muonongedwa (1-5)

  • Fanizo la mtengo wamkuyu wosabala zipatso (6-9)

  • Mzimai wopindika msana acilitsidwa pa Sabata (10-17)

  • Fanizo la kanjele ka mpilu komanso la zofufumitsa (18-21)

  • Khama n’lofunika kuti tilowe pa khomo lopanikiza (22-30)

  • Herode achulidwa kuti “nkhandwe” (31-33)

  • Yesu adandaula za Yerusalemu (34, 35)

13  Pa nthawi imeneyo, ena amene analipo anamufotokozela za anthu a ku Galileya amene Pilato anasakaniza magazi ao ndi nsembe zao. 2  Iye anawayankha kuti: “Muganiza kuti Agalileyawo anali ocimwa kwambili kuposa Agalileya ena onse cifukwa zimenezo zinawacitikila? 3  Ai ndithu. Koma ndikukuuzani kuti ngati simungalape, nonsenu mudzaonongedwa ngati iwo. 4  Kapena muganiza kuti anthu 18 aja omwe nsanja inawagwela ku Siloamu n’kuwapha, anali ocimwa kwambili kuposa anthu ena onse okhala mu Yerusalemu? 5  Ai ndithu, koma ndikuuzani kuti ngati simulapa, nonsenu mudzaonongedwa ngati iwo.” 6  Ndiyeno anayamba kuwauza fanizo ili: “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu m’munda wake wampesa, ndipo anapita kukafuna zipatso mu mtengowo, koma sanapezemo ciliconse. 7  Kenako munthuyo anauza wosamalila munda wa mpesawo kuti, ‘Kwa zaka zitatu ndakhala ndikubwela kudzafunafuna zipatso mu mtengo wamkuyu uwu, koma sindikupezamo kalikonse. Udule! N’cifukwa ciani ukungoononga nthaka?’ 8  Poyankha, wosamalila mundayo anati, ‘Mbuyanga, ulekeni kwa caka cina cimodzi, ndipo ndidzakumba m’mbali mwake n’kuikamo manyowa. 9  Ngati udzabala zipatso m’tsogolo zidzakhala bwino. Koma ngati sudzabala mudzaudule.’” 10  Tsopano Yesu anali kuphunzitsa m’sunagoge winawake pa Sabata. 11  Ndiyeno mmenemo munali mai wina amene anali ndi mzimu umene unali kumufooketsa* kwa zaka 18. Iye anali wopindika kwambili msana, ndipo sanali kuwelamuka ngakhale pang’ono. 12  Yesu atamuona maiyo analankhula naye n’kumuuza kuti: “Mainu, mwamasulidwa ku matenda anu.” 13  Ndiyeno anaika manja ake pa maiyo, ndipo nthawi yomweyo anawelamuka n’kuyamba kutamanda Mulungu. 14  Koma mtsogoleli wa sunagoge ataona izi anakwiya, cifukwa cakuti Yesu anacilitsa munthu pa Sabata. Conco anauza khamu la anthulo kuti: “Pali masiku 6 amene tiyenela kugwila nchito. Cotelo muzibwela kudzacilitsidwa pa masiku amenewo, osati pa tsiku la Sabata ai.” 15  Koma Ambuye anamuyankha kuti: “Onyenga inu, kodi aliyense wa inu samasula ng’ombe yake kapena bulu wake m’khola pa Sabata n’kupita naye kukamumwetsela madzi? 16  Kodi maiyu, amene ndi mwana wamkazi wa Abulahamu, amenenso Satana anamumanga kwa zaka 18, sayenela kumasulidwa m’maunyolo amenewa pa tsiku la Sabata?” 17  Iye atakamba zimenezi, anthu onse omutsutsa anacita manyazi. Koma khamu lonse la anthu linayamba kukondwela cifukwa ca zinthu zodabwitsa zimene iye anacita. 18  Conco anapitiliza kunena kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati ciani, nanga ndingauyelekezele ndi ciani? 19  Uli ngati kanjele ka mpilu, kamene munthu anatenga n’kukabzala m’munda wake. Ndiyeno kanakula n’kukhala mtengo, ndipo mbalame za mumlengalenga zinamanga zisa m’nthambi zake.” 20  Iye anakambanso kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu ndingauyelekezele ndi ciani? 21  Uli ngati zofufumitsa zimene mai wina anatenga n’kuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zikulu-zikulu zopimila,* ndipo mtanda wonsewo unafufuma.” 22  Ndiyeno iye anayenda mzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi akuphunzitsa, n’kupitiliza ulendo wake wopita ku Yerusalemu. 23  Tsopano munthu wina anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi amene adzapulumuka ndi ocepa?” Iye anawauza kuti: 24  “Yesetsani mwamphamvu kulowa pa khomo lopanikiza, cifukwa ndikukuuzani kuti ambili adzafuna kulowa koma sadzakwanitsa kutelo. 25  Mwininyumba akadzauka n’kukhoma citsekoco, mudzaimilila panja n’kumagogoda, ndipo mudzakamba kuti ‘Ambuye, titsegulileni.’ Koma iye adzakuyankhani kuti: ‘Sindikudziwani.’ 26  Ndiyeno mudzayamba kukamba kuti, ‘Tinali kudya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munali kuphunzitsa m’miseu yathu ikulu-ikulu.’ 27  Koma ine ndidzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwani. Cokani pamaso panga nonsenu ocita zosalungama!’ 28  Kumeneko, muzikalila ndi kukukuta mano mukadzaona Abulahamu, Isaki, Yakobo, ndi aneneli onse ali mu Ufumu wa Mulungu, koma inu mutaponyedwa kunja. 29  Komanso anthu adzabwela kucokela kum’mawa ndi kumadzulo, ndiponso kucokela kumpoto ndi kum’mwela n’kudzakhala pathebulo mu Ufumu wa Mulungu. 30  Ndipo pali othela amene adzakhala oyamba, komanso pali oyamba amene adzakhala othela.” 31  Nthawi yomweyo Afarisi ena anabwela n’kumuuza kuti: “Pitani, cokani kuno, cifukwa Herode akufuna kukuphani.” 32  Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Pitani mukaiuze nkhandwe imeneyo kuti, ‘Ndikutulutsa ziwanda ndi kucilitsa anthu lelo komanso mawa, ndipo ndidzatsiliza pa tsiku lacitatu.’ 33  Ngakhale n’telo, ndipitiliza kugwila nchito yanga lelo, mawa, komanso mkuca. Pambuyo pake, ndidzapita ku Yerusalemu, cifukwa n’kosayenela* kuti mneneli amuphele kunja kwa Yerusalemu. 34  Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneli komanso woponya miyala anthu otumidwa kwa iwe. Mobweleza-bweleza ndinafuna kusonkhanitsa pamodzi ana ako, monga mmene nkhuku imasonkhanitsila anapiye ake m’mapiko ake! Koma inu simunafune zimenezo. 35  Tsopano mvelani! Mulungu wakusiilani nyumba yanu. Ndikukuuzani kuti, simudzandionanso kufikila mutanena kuti: ‘Wodalitsika ndi iye wobwela m’dzina la Yehova!*’”

Mau a m'Munsi

Kapena kuti, “mzimu wolemalitsa.”
Kucokela ku Cigiriki, “wokwana miyeso ya seya.” Muyeso umodzi wa seya unali kukwana malita 7.33. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “n’zosamveka.”